Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w98 5/1 tsamba 30-31
  • Yobu Afupidwa Chifukwa Chokhulupirika

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Yobu Afupidwa Chifukwa Chokhulupirika
  • Nsanja ya Olonda—1998
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Atonthozedwa ndi Kupatsidwanso Zake Zonse
  • Zimene Ife Tingaphunzirepo
  • Yehova Amasangalala Tikamapempherera Ena
    Utumiki Komanso Moyo Wathu wa Chikhristu—Ndandanda ya Misonkhano—2016
  • Yobu Anapirira—Nafenso Tingatero!
    Nsanja ya Olonda—1994
  • Phunziro pa Kusamalira Mavuto
    Nsanja ya Olonda—1995
  • Yobu Analemekeza Dzina la Yehova
    Nsanja ya Olonda—2009
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1998
w98 5/1 tsamba 30-31

Anachita Chifuniro cha Yehova

Yobu Afupidwa Chifukwa Chokhulupirika

YOBU anali mwamuna wachifundo, wothandiza akazi amasiye, ana amasiye, ndi anthu ovutika. (Yobu 29:12-17; 31:16-21) Kenaka, mwadzidzidzi masoka anamgwera, chuma chinamthera, ana ake anafa, ndiponso iye anadwala. Zinali zomvetsa chisoni kuti munthu wokoma mtima chotereyu amene anali kuthandiza kwambiri anthu oponderezedwa, analandira chithandizo chochepa panthaŵi ya mavuto ake. Ngakhale mkazi wake anamuuza kuti ‘achitire Mulungu mwano ndi kufa.’ Ndipo “mabwenzi” ake Elifazi, Bilidadi, ndi Zofari sanamtonthoze konse. M’malo mwake, iwo analimbikira kunena kuti Yobu anachimwa ndipo anayeneradi kuvutika.​—Yobu 2:9; 4:7, 8; 8:5, 6; 11:13-15.

Ngakhale kuti anavutika kwambiri, Yobu anakhalabe wokhulupirika. Chifukwa cha zimenezi, pomalizira pake Yehova anachitira Yobu chifundo ndipo anamdalitsa. Nkhani ya mmene anachitira zimenezo imatsimikizira atumiki onse okhulupirika a Mulungu kuti nthaŵi ina iwonso adzafupidwa.

Atonthozedwa ndi Kupatsidwanso Zake Zonse

Choyamba, Yehova anadzudzula Elifazi, Bilidadi, ndi Zofari. Polankhula kwa Elifazi, mwachionekere amene anali wamkulu kuposa enawo, iye anati: “Mkwiyo wanga wakuyakira iwe ndi mabwenzi ako aŵiri, pakuti simunandinenera choyenera monga ananena mtumiki wanga Yobu. Ndipo tsono, mudzitengere ng’ombe zisanu ndi ziŵiri, ndi nkhosa zamphongo zisanu ndi ziŵiri, mumuke kwa mtumiki wanga Yobu mudzifukizire nokha nsembe yopsereza; ndi mtumiki wanga Yobu adzapempherera inu.” (Yobu 42:7, 8) Tangolingalirani zimene zinaloŵetsedwamo!

Yehova analamula Elifazi, Bilidadi, ndi Zofari kuti apereke nsembe ziŵeto zambiri, mwinamwake ncholinga chakuti iwo adziŵe kuti tchimo lawo linali lalikulu kwambiri. Ndithudi, kaya zinali zadala kapena ayi, iwo ananyoza Mulungu mwa kunena kuti iye “sakhulupirira atumiki ake” ndiponso kuti zinalibe kanthu kwa iye kuti kaya Yobu anali wokhulupirika kapena ayi. Elifazi ananenanso kuti pamaso pa Mulungu, Yobu anali wopanda pake monga gulugufe! (Yobu 4:18, 19; 22:2, 3) Nchifukwa chake Yehova anati: “Simunandinenera choyenera”!

Komatu sizokhazo. Elifazi, Bilidadi, ndi Zofari anachimwiranso Yobu iyemwini mwa kumuuza kuti mavuto akewo anawadzetsa yekha. Zidzudzulo zawo zopanda umbonizo ndi kusoŵa chifundo kwawo zinapangitsa kuti Yobu akwiye kwambiri ndi kuchita tondovi, zimene zinamchititsa kulira kuti: “Mudzasautsa moyo wanga kufikira liti, ndi kundithyolathyola nawo mawu?” (Yobu 10:1; 19:2) Tangolingalirani mmene amuna atatuwo anachitira manyazi pamene analamulidwa kuti apite kwa Yobu nakapereke nsembe ya machimo awo!

Koma Yobu sanafunikire kusangalala chifukwa cha kuchita manyazi kwawo. Ndithudi, Yehova anamuuza kuti apempherere omdzudzulawo. Yobu anachitadi zimene anauzidwazo, ndipo anadalitsidwa chifukwa cha zimenezo. Choyamba, Yehova anachiritsa matenda ake oopsawo. Kenaka, abale, alongo, ndi mabwenzi akale a Yobu anafika kudzamtonthoza, “nampatsanso yense ndalama ndi mphete.”a Ndiponso, Yobu “anali nazo nkhosa zikwi khumi ndi zinayi, ndi ngamila zikwi zisanu ndi chimodzi, ndi ng’ombe zamagoli chikwi chimodzi, ndi abulu aakazi chikwi chimodzi.”b Ndipo mwachionekere mkazi wa Yobu anasintha maganizo nayanjana nayenso. M’kupita kwa nthaŵi, Yobu anadalitsidwa ndi ana aamuna asanu ndi aŵiri ndi ana aakazi atatu, ndipo anakhala ndi moyo mpaka mbadwo wachinayi wa mbadwa zake.​—Yobu 42:10-17.

Zimene Ife Tingaphunzirepo

Yobu anapereka chitsanzo chachikulu kwa atumiki amakono a Mulungu. Iye anali “wangwiro ndi woongoka,” munthu amene Yehova anasangalala kumutcha “mtumiki wanga.” (Yobu 1:8; 42:7, 8) Komabe, zimenezi sizikutanthauza kuti Yobu anali wosachimwa. Nthaŵi ina pamene anali kuyang’anizana ndi ziyeso zake, iye analingalira molakwa kuti Mulungu ndiye anadzetsa mavuto akewo. Iye anadzudzulanso Mulungu chifukwa cha mmene Iye amachitira ndi anthu. (Yobu 27:2; 30:20, 21) Ndipo ananenanso kuti iyeyo ndiye anali wolungama osati Mulungu. (Yobu 32:2) Koma Yobu sanafune mpang’ono pomwe kusiya Mlengi wake, ndipo modzichepetsa iye analola kuwongoleredwa ndi Mulungu. “Ndinafotokozera zimene sindinazizindikira,” iye anatero. “Ndidzinyansa, ndi kulapa m’fumbi ndi mapulusa.”​—Yobu 42:3, 6.

Pamene tiyang’anizana ndi chiyeso, ifenso tingaganize, kulankhula, kapena kuchita zosayenera. (Yerekezerani ndi Mlaliki 7:7.) Komabe, ngati timakondadi Mulungu kuchokera pansi pa mtima, sitidzampandukira kapena kumkwiyira chifukwa chotilola kuti tikumane ndi mavuto. M’malo mwake, tidzapirirabe ndipo tikadzatero pomalizira pake tidzalandira madalitso ochuluka. Ponena za Yehova, wamasalmo anati: “Pa munthu wangwiro mukhala wangwiro.”​—Salmo 18:25.

Yobu asanachiritsidwe, Yehova anamuuza kuti apempherere onse amene anamchitira zoipa. Chimenecho nchitsanzo chabwino chotani nanga kwa ife! Kuti atikhululukire machimo athu, Yehova amafuna kuti choyamba tizikhululukira ena amene atichimwira. (Mateyu 6:12; Aefeso 4:32) Ngati sitifuna kukhululukira ena pamene tili ndi chifukwa chabwino chochitira zimenezo, kodi tingayembekezeredi Yehova kuti atichitire chifundo?​—Mateyu 18:21-35.

Tonsefe timayang’anizana ndi ziyeso nthaŵi zina. (2 Timoteo 3:12) Komabe, tingapirire monga Yobu. Mwa kuchita zimenezo, tidzapeza mphotho yaikulu. Yakobo analemba kuti: “Taonani tiwayesera odala opirirawo; mudamva za chipiriro cha Yobu, ndipo mwaona chitsiriziro cha Ambuye, kuti Ambuye ali wodzala chikondi, ndi wachifundo.”​—Yakobo 5:11.

[Mawu a M’munsi]

a Mtengo wa “ndalama” iliyonse (m’Chihebri, qesi·tahʹ) sudziŵika bwino. Koma m’tsiku la Yakobo anthu anali kugula malo aakulu ndithu ndi “ndalama zana” limodzi. (Yoswa 24:32) Choncho, “ndalama” imodzi yochokera kwa mlendo aliyense mwinamwake inali mphatso yaikulu ndithu.

b Mwachionekere, anatchula kuti panali abulu aakazi pofuna kusonyeza phindu lawo la kuswana.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena