CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | YOBU 38-42
Yehova Amasangalala Tikamapempherera Ena
Yehova ankayembekezera kuti Yobu apempherere Elifazi, Bilidadi ndi Zofari
Yehova anauza Elifazi, Bilidadi ndi Zofari kuti apite kwa Yobu kukadziperekera nsembe
Yehova ankayembekezera kuti Yobu awapempherere
Yobu atapempherera anzakewo Yehova anamudalitsa
Yehova anadalitsa Yobu chifukwa anali wokhulupirika komanso wopirira
Yehova anathetsa mavuto onse a Yobu n’kumupatsanso moyo wathanzi
Yobu anatonthozedwa kwambiri ndi anzake komanso achibale
Yehova anapatsanso Yobu chuma chochuluka, kuwirikiza kawiri chuma chomwe anali nacho poyamba
Yobu ndi mkazi wake anaberekanso ana 10
Yobu anakhalanso ndi moyo kwa zaka zina 140 ndipo anaona mibadwo 4 ya banja lake