Nyimbo 194
Loŵani m’Mabwalo a Kachisi wa Yehova!
1. M’dziko lonse Mboni za Ya zikulalika:
‘M’lungu ndi Kristu alamulira!’
Ndinthaŵi yolambira Wamphamvuyonseyo,
Ndi kukhalabe munyumba yake.
2. Tsekulani zipata ofatsa aloŵe.
M’loŵe mkati, m’bwalo la Mulungu.
Mudze ndi mphatso kuphiri lake loyera.
Musangalale mumtima mwanu.
3. Tsikuli nloti ‘wamng’ono wakhala chikwi.’
“Nkhosa zina” zikuyandikira.
Ngati njiŵa aloŵa m’bwalo lakachisi
Mmene angalemekeze M’lungu.
4. Loŵani m’zipata ndi kutama Yehova.
Nchiitano chomveka konseko.
Msonkhane m’bwalo la kulambira kowona.
M’dzakhale mmenemo nthaŵi zonse.