Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w97 3/15 tsamba 8-11
  • Kodi Mukulakalaka kuwonjezera Utumiki Wanu?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Mukulakalaka kuwonjezera Utumiki Wanu?
  • Nsanja ya Olonda—1997
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Mlevi Ayamikira
  • Phunzirani Kukhutira
  • Musalefuke
  • Ikani Zonulirapo Zofikika
  • Kaonedwe Kabwino
  • Khalani ndi Zolinga Zauzimu Kuti Mulemekeze Nazo Mlengi Wanu
    Nsanja ya Olonda—2004
  • Tingatani Kuti Tizikhala ndi Zolinga Zauzimu N’kumazikwaniritsa?
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2022
  • Timayamikira Kwambiri Mwayi Umene Tili Nawo
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2007
  • Kodi Achinyamatanu Mukupita Patsogolo Mwauzimu?
    Nsanja ya Olonda—2003
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1997
w97 3/15 tsamba 8-11

Kodi Mukulakalaka kuwonjezera Utumiki Wanu?

“NDINAMKWIYIRA Yehova,” akutero Laura. “Ndinapemphera mosaleka kuti atithandize kuthetsa mavuto athu a ndalama kuti ndipitirize ndi upainiya​—koma mosaphula kanthu. Pomalizira pake ndinangosiya upainiya. Ndiponso sindingakane kuti ndinawachitira kaduka awo amene anapitiriza.”

Lingaliraninso za Michael, mtumiki wotumikira mumpingo wa Mboni za Yehova. Iye anali kukhumba udindo wa woyang’anira. (1 Timoteo 3:1) Pamene chikhumbo chake sichinakwaniritsidwe zaka zingapo, anaŵaŵidwa mtima kwambiri moti sanafunenso ndi kumlingalira nkomwe ngati angapatsidwe mwaŵiwo. “Sindikanathanso kupirira kupweteka kwa kugwiritsidwa mwala,” iye akutero.

Kodi zachitikanso kwa inu? Kodi mwasiya thayo lokondeka lateokrase? Mwachitsanzo, kodi mwasiya kutumikira monga mpainiya, wolengeza Ufumu wa nthaŵi zonse? Kapena kodi mukulakalaka mathayo ena a mumpingo opatsidwa kwa ena? Mwina mukukhumba kwambiri kukatumikira pa Beteli kapena monga mmishonale, koma mikhalidwe yanu siikulonani.

“Chiyembekezo chozengereza chidwalitsa mtima,” limavomereza motero buku la Miyambo. (Miyambo 13:12) Zimenezi zingakhale choncho makamaka ngati ena akulandira thayo limodzimodzilo limene mungakonde kukhala nalo. Kodi Mawu a Mulungu akupereka nzeru, chitonthozo ndi chiyembekezo kwa aliyense amene wagwira mwala pa zimenezi? Inde, iwo amatero. Kwenikweni, Salmo la 84 limafotokoza malingaliro a mtumiki wa Yehova amene anali ndi zikhumbo zofananazo zosakwaniritsidwa zokhudza utumiki wa Yehova.

Mlevi Ayamikira

Olemba Salmo la 84 ndi ana a Kora, Alevi omwe ankatumikira pakachisi wa Yehova ndi kuchitadi kaso ndi mwaŵi wawo wautumiki. “Pokhala Inu mpotikonda ndithu, Yehova wa makamu!” akufuula mmodzi wa iwo. “Moyo wanga ulakalaka, inde ukomokanso ndi kufuna mabwalo a Yehova; mtima wanga ndi thupi langa zifuulira kwa Mulungu wamoyo.”​—Salmo 84:1, 2.

Mleviyu anali kulakalaka kwambiri kutumikira pakachisi wa Yehova moti ngakhale maonekedwe wamba a malo m’mbali mwa msewu wa ku Yerusalemu anaoneka okopa kwa iye. “Popyola chigwa cha kulira misozi,” iye akutero, “achiyesa cha akasupe.” (Salmo 84:6) Inde, dera limene limakhala louma linali ngati la madzi ambiri kwa iye.

Chifukwa chakuti wamasalmoyo sanali Mlevi wansembe, anali kutumikira pakachisi mlungu umodzi wokha patapita miyezi isanu ndi umodzi. (1 Mbiri 24:1-19; 2 Mbiri 23:8; Luka 1:5, 8, 9) Nthaŵi yake yonse yotsala anali kukhala kunyumba mu umodzi wa midzi ya Alevi. Choncho iye anaimba kuti: “Mbawanso inapeza nyumba, ndi namzeze chisa chake choikamo ana ake, pamaguwa a nsembe anu, Yehova wa makamu, Mfumu yanga ndi Mulungu wanga.” (Salmo 84:3) Mleviyo akanakondwera chotani nanga akanakhala ngati mbalamezo zimene zinali ndi malo okhazikika pakachisi!

Mleviyu akanaŵaŵidwa mtima mosavuta chifukwa chakuti sanali kutumikira kaŵirikaŵiri pakachisi. Komabe, anakondwera kutumikira motero, ndipo anazindikiradi kuti kudzipereka ndi mtima wonse kwa Yehova ndiko kofunika. Kodi nchiyani chinathandiza Mlevi wokhulupirikayu kukhalabe wokhutira ndi mwaŵi wake wautumiki?

Phunzirani Kukhutira

“Tsiku limodzi m’mabwalo anu likoma koposa masiku ambirimbiri akukhala pena,” akutero Mleviyo. “Kukhala ine wapakhomo m’nyumba ya Mulungu wanga, kundikonda ine koposa kugonera m’mahema a choipa.” (Salmo 84:10) Iye anazindikira kuti kukhala panyumba ya Yehova ngakhale tsiku limodzi lokha kuli mwaŵi wosayerekezereka. Ndipo Mleviyu anali ndi masiku ambiri ndithu otumikira pakachisi. Kukhutira kwake ndi mwaŵi wake kunamchititsa kuimba ndi chisangalalo.

Nanga bwanji ifeyo? Kodi timawaŵerengera madalitso athu, kapena kodi timangoiŵala zimene tili nazo kale mu utumiki wa Yehova? Yehova wapatsa anthu ake mwaŵi ndi ntchito zambiri zosiyanasiyana chifukwa cha kudzipereka kwawo kwa iye. Zimenezi zimaphatikizapo mathayo olemera kwambiri a kuyang’anira, kuŵeta, kuphunzitsa, ndi mbali zosiyanasiyana za utumiki wa nthaŵi zonse. Komanso zimaphatikizapo zinthu zina zamtengo wapatali zokhudza kulambira Yehova.

Mwachitsanzo, talingalirani za utumiki wachikristu. Mtumwi Paulo akufanizira mwaŵi wathu wa kulalikira uthenga wabwino ndi kukhala ndi ‘chuma m’zotengera zadothi.’ (2 Akorinto 4:7) Kodi utumiki umenewu mumauona monga chuma chamtengo wapatali kopambana? Yesu Kristu, amene anatsogolera ntchito yolalikira Ufumu imeneyi, anaiona motero, naika chitsanzo. (Mateyu 4:17) “Popeza tili nawo utumiki umene, . . . sitifooka,” anatero Paulo.​—2 Akorinto 4:1.

Misonkhano yachikristu ilinso chogaŵira chopatulika chosatengera mopepuka. Pamisonkhano yathu, timalandira malangizo ofunika kwambiri ndi kusangalala ndi mayanjano ofunikira. Pamisonkhano tingasonyezenso poyera chikhulupiriro ndi chiyembekezo chathu mwa kuyankha kaŵirikaŵiri ndi mwa kutengamo mbali m’programu mwanjira zina. (Ahebri 10:23-25) Ndithudi misonkhano yathu ili chogaŵira choyenera kukondedwa kwambiri!

Michael, wotchulidwa poyambayo, anaona madalitsowa kukhala amtengo wapatali kwambiri nawayamikira kuchokera mumtima. Koma kugwiritsidwa kwake mwala posakhoza kutumikira monga mkulu kunakankhira pambali kuyamikira kwake madalitsowa kwa kanthaŵi. Mwa kuwaganiziranso mwakuya, anatha kulinganizanso malingaliro ake ndi kudikira kwa Yehova modekha.

M’malo mwa kusakhutira posakhala ndi mwaŵi wakutiwakuti, timachita bwino kupendanso njira zimene Yehova akutidalitsira, monga wamasalmo anachitira.a Ngati tilephera kuona zambiri, tiyenera kupenyanso, ndi kupempha Yehova kutitsegula maso athu kuti tione mwaŵi wathu ndi njira zimene akutidalitsira ndi kutigwiritsira ntchito kupereka chitamando kwa iye.​—Miyambo 10:22.

Nkofunikanso kuzindikira kuti mwaŵi wapadera, monga udindo wa woyang’anira, umafuna ziyeneretso zakutizakuti. (1 Timoteo 3:1-7; Tito 1:5-9) Choncho tifunikira kudzipenda, kufunafuna mbali zilizonse zimene tifunikira kuwongolera ndi kuyesetsa mwakhama kuziwongolera.​—1 Timoteo 4:12-15.

Musalefuke

Ngati sitilandira mwaŵi wakutiwakuti wa utumiki, tisaganize kuti Yehova amakonda kwambiri awo omwe ali nawo kapena kuti akutimana zabwino. Ndithudi, sitiyenera kuganiza modukidwa kuti enawa apeza mwaŵi wawo ngakhale sanauyenere chifukwa cha kukondera kwa anthu m’malo mwa kuikidwa mwa teokrase. Kuvutika mtima ndi malingaliro ameneŵa kungachititse njiru, makangano, ndipo ngakhale kutisiyitsa zonse.​—1 Akorinto 3:3; Yakobo 3:14-16.

Laura, wotchulidwa pachiyambipo, sanaleke. M’kupita kwa nthaŵi anathetsa mkwiyo wake ndi kaduka kake. Laura anapemphera kwa Mulungu mobwerezabwereza kuti amthandize kuletsa kuvutika kwake maganizo posakhoza kuchita upainiya. Anapemphanso thandizo kwa amuna oyenerera mumpingo ndipo anatsimikizanso kuti Mulungu amamkonda. “Yehova anandipatsa mtendere wamaganizo,” iye akutero. “Pamene kuli kwakuti ineyo ndi mwamuna wanga sitingachitenso upainiya tsopano, tikuyamikiradi nthaŵi imene tinali kuuchita ndipo timalimbitsidwa ndi zimene tinakumana nazo. Timathandizanso mwana wathu wamwamuna wosinkhuka mu upainiya wake.” Pokhala wokhutira, Laura tsopano amatha ‘kukondwa nawo iwo akukondwera’ mu utumiki wawo waupainiya.​—Aroma 12:15.

Ikani Zonulirapo Zofikika

Kukhala kwathu okhutira ndi mwaŵi wa utumiki umene tili nawo sikumatanthauza kuti tileke kuika zonulirapo zina zateokrase. Polongosola chiukiriro chakumwamba, Paulo ananena za “kutambalitsira zamtsogolo.” Iye anatinso: “Kumene tidafikirako, mayendedwe athu alinganeko.” (Afilipi 3:13-16) Zonulirapo zateokrase zingatithandize kutambalitsira mtsogolo. Komabe, vuto lokha ndilo kuika zonulirapo zotheka.

Zonulirapo zotheka zili zanzeru ndi zofikika. (Afilipi 4:5) Zimenezi sizikutanthauza kuti chonulirapo chofuna zaka zambiri za ntchito yolimba sichotheka. Chonulirapo chofuna nthaŵi yaitali chimenechi chingafikidwe pang’onopang’ono mwa kuika zonulirapo zapakati zotsatizana, kapena kuti masitepe. Zimenezi zidzakhala zizindikiro zosonyeza kupita patsogolo kwauzimu. Kutsiriza sitepe lililonse mwachipambano kudzapereka chikhutiro paulendowo m’malo mogwiritsa mwala.

Kaonedwe Kabwino

Komabe, kuli bwino kudziŵa kuti chifukwa cha mikhalidwe yathu ndi zofooka zathu, mwaŵi wina sitingaupeze. Kuuika kukhala zonulirapo kumangogwiritsa mwala ndi kutayitsa mtima. Zonulirapo zimenezi ziyenera kuikidwa padera, makamaka pakali pano. Kuchita zimenezi sikudzakhala kovuta ngati tipempherera kukhutira kwaumulungu ndipo ngati kuchita chifuniro cha Yehova kukhala chinthu chachikulu kopambana kwa ife. Pamene tikalimira mathayo autumiki, ulemerero wa Yehova ndiwo wofunika, osati kudzipangira dzina ndi zinthu zaumwini zomwe takwaniritsa. (Salmo 16:5, 6; Mateyu 6:33) Moyenerera Baibulo limatiuza kuti: “Pereka zochita zako kwa Yehova, ndipo zolingalira zako zidzakhazikika.”​—Miyambo 16:3.

Mwa kupenda Salmo la 84, tatha kuona kuti wamasalmo anasonyeza mzimu umenewu pamwaŵi wa utumiki, ndipo Yehova anamdalitsa kwambiri. Ndiponso, salmo limeneli likupindulitsabe anthu a Yehova mpaka lero.

Mwa kudalira Yehova mwapemphero, mungalinganize chikhumbo chanu cha mwaŵi wowonjezereka ndi chikhutiro cha umene muli nawo kale. Musalole konse chikhumbo chanu cha kuchita zowonjezereka kukulandani chiyamikiro cha zimene muli nazo tsopano ndi chisangalalo cha kutumikira Yehova kosatha. Khulupirirani Yehova, popeza kuti zimenezi zimadzetsa chimwemwe, monga momwe mawu a Mleviyo akusonyezera: “Yehova wa makamu, wodala munthu wakukhulupirira Inu.”​—Salmo 84:12.

[Mawu a M’munsi]

a Chonde onani nkhani yakuti “Kodi Mumayamikira Zinthu Zopatulika?” m’kope la June 15, 1988 la Nsanja ya Olonda.

[Bokosi patsamba 11]

Zonulirapo Zimene Tingaike

Kuŵerenga Baibulo tsiku ndi tsiku.​—Yoswa 1:8; Mateyu 4:4

Kuwongolera mphamvu zathu za kuzindikira mwa kuphunzira Malemba.​—Ahebri 5:14

Kukhala ndi unansi wapafupi ndi Mulungu.​—Salmo 73:28

Kukulitsa chipatso chilichonse cha mzimu.​—Agalatiya 5:22, 23

Kuwongolera mapemphero athu.​—Afilipi 4:6, 7

Kukhala wogwira mtima kwambiri polalikira ndi pophunzitsa.​—1 Timoteo 4:15, 16

Kuŵerenga ndi kusinkhasinkha kope lililonse la magazini a Nsanja ya Olonda ndi Galamukani!​—Salmo 49:3

[Zithunzi patsamba 9]

Poika zonulirapo zaumwini, kuchita chifuniro cha Mulungu kukhale patsogolo

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena