Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 8/07 tsamba 1
  • Timayamikira Kwambiri Mwayi Umene Tili Nawo

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Timayamikira Kwambiri Mwayi Umene Tili Nawo
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—2007
  • Nkhani Yofanana
  • Kodi Mukulakalaka kuwonjezera Utumiki Wanu?
    Nsanja ya Olonda—1997
  • Kodi Mumayamikira Mwayi Wogwira Ntchito ndi Yehova?
    Nsanja ya Olonda—2014
  • Ngati Munatumikirapo pa Udindo Wina Mumpingo, Kodi Mungatumikirenso?
    Nsanja ya Olonda—2009
  • Kalata Yochokera ku Bungwe Lolamulira
    Gulu Lochita Chifuniro cha Mulungu
Onani Zambiri
Utumiki Wathu wa Ufumu—2007
km 8/07 tsamba 1

Timayamikira Kwambiri Mwayi Umene Tili Nawo

1 Kuchokera nthawi imene anthu analengedwa, Yehova wapatsa atumiki ake mwayi wochita zinthu zosiyanasiyana. Iye wapereka mwayi umenewu kwa aliyense kaya akhale mkazi kapena mwamuna, wolemera kapena wosauka, mwana kapena wachikulire. (Luka 1:41, 42; Mac. 7:46; Afil. 1:29) Kodi masiku ano watipatsa mwayi wotani?

2 Mwayi Umene Tili Nawo: Tili ndi mwayi wophunzitsidwa ndi Yehova. (Mat. 13:11, 15) Mwayi wina umene tili nawo ndiwo kutamanda Yehova mwa kuyankhapo pamisonkhano ya mpingo. (Sal. 35:18) Tikakhala ndi mwayi woyankhapo, timachita zimenezi ndi mtima wonse. Ndipo gawo lililonse limene tapatsidwa pampingo tikamaliona kukhala mwayi, tidzalichita mwakhama kwambiri. Kodi nthawi zonse timachita nawo ntchito yosamalira Nyumba ya Ufumu?

3 Ngakhale kuti anthu ambiri amakayikira kuti mapemphero awo amayankhidwa ndi Mulungu, ifeyo tili ndi mwayi woti mapemphero athu amayankhidwa ndi munthu wofunika kwambiri m’chilengedwe chonse. (Miy. 15:29) Yehova iye mwini amamvetsera mapemphero a atumiki ake. (1 Pet. 3:12) Iye satiikira malire a nthawi zimene tiyenera kulankhula naye ndipo timatha kupemphera “pa chochitika chilichonse.” Imeneyitu ndi mphatso yamtengo wapatali.—Aef. 6:18.

4 “Antchito Anzake a Mulungu”: Mwayi wina wapadera kwambiri umene tili nawo ndiwo kulengeza uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu monga “antchito anzake a Mulungu.” (1 Akor. 3:9) Ntchito imeneyi imatipatsa chimwemwe ndiponso imatitsitsimula. (Yoh. 4:34) Yehova safunikira kugwiritsa ntchito anthu kuti achite ntchito imeneyi, koma watipatsa ntchitoyi chifukwa chakuti amatikonda. (Luka 19:39, 40) Ngakhale zili choncho, sanapereke mwayi umenewu kwa wina aliyense. Anthu amene amapatsidwa mwayi wochita nawo utumiki afunikira kukhala ndi ziyeneretso zauzimu nthawi zonse. (Yes. 52:11) Kodi timasonyeza kuti timaona mwayi wotumikira umenewu kukhala wofunika kwambiri mwa kuchita nawo utumikiwo mlungu uliwonse?

5 Mwayi wochita zinthu zosiyanasiyana umene Yehova watipatsa umatilemeretsa. (Miy. 10:22) Mwayi umenewu tisamauone mopepuka. Ndipo tikamasonyeza kuti timaona mwayi wotumikira kukhala wofunika kwambiri, timasangalatsa Atate wathu wakumwamba, yemwe amatipatsa “mphatso iliyonse yabwino ndi mtulo uliwonse wangwiro.”—Yak. 1:17.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena