MUTU 7
Misonkhano Imene Imatilimbikitsa “pa Chikondi Ndi Ntchito Zabwino”
KUYAMBIRA kale, anthu a Yehova akhala akuchita misonkhano yosiyanasiyana. Kale ku Isiraeli, amuna onse ankapita ku Yerusalemu kukakhala nawo pa zikondwerero zitatu zikuluzikulu zimene zinkachitika chaka chilichonse. (Deut. 16:16) Munthawi ya atumwi, Akhristu ankasonkhananso nthawi zonse ndipo kawirikawiri ankasonkhana m’nyumba za anthu. (Filim. 1, 2) Masiku ano, timasangalala ndi misonkhano ya mpingo komanso ikuluikulu. Koma kodi n’chifukwa chiyani atumiki a Mulungu amasonkhana pamodzi? Chifukwa chachikulu n’choti misonkhano ndi mbali yofunika ya kulambira kwathu.—Sal. 95:6; Akol. 3:16.
2 Misonkhano imapindulitsanso anthu amene amapezekapo. Ponena za Chikondwerero cha Misasa cha nambala 7, Aisiraeli anauzidwa kuti: “Sonkhanitsani anthu, amuna, akazi, ana ndi alendo okhala m’mizinda yanu, kuti amvetsere ndi kuphunzira, pakuti ayenera kuopa Yehova Mulungu wanu ndi kutsatira mosamala mawu onse a m’Chilamulo ichi.” (Deut. 31:12) Choncho chifukwa chachikulu chimene timasonkhanira pamodzi ndi choti ‘tiziphunzitsidwa ndi Yehova.’ (Yes. 54:13) Misonkhano imatipatsanso mwayi wodziwana ndi ena, kucheza ndiponso kulimbitsa chikhulupiriro chathu.
MISONKHANO YA MPINGO
3 Ophunzira a Yesu omwe anasonkhana pambuyo pa Pentekosite mu 33 C.E. anapitiriza kumvera zimene atumwi ankaphunzitsa ndipo “tsiku ndi tsiku anali kusonkhana kukachisi mogwirizana.” (Mac. 2:42, 46) Patapita nthawi, Akhristu akasonkhana, ankawerenga makalata ouziridwa, kuphatikizapo makalata olembedwa ndi atumwi komanso ophunzira ena a Yesu. (1 Akor. 1:1, 2; Akol. 4:16; 1 Ates. 1:1; Yak. 1:1) Ankaperekanso pemphero la mpingo wonse. (Mac. 4:24-29; 20:36) Komanso nthawi zina ankafotokoza mmene utumiki wawo waumishonale ukuyendera m’madera ena. (Mac. 11:5-18; 14:27, 28) Ankakambirana zimene Baibulo limaphunzitsa komanso mmene maulosi ankakwaniritsidwira. Ankalandiranso malangizo okhudza makhalidwe oyenera Akhristu ndiponso zimene ayenera kuchita posonyeza kuti ndi odzipereka kwa Mulungu. Onse ankalimbikitsidwa kuti azigwira ntchito yolalikira uthenga wabwino mwakhama.—Aroma 10:9, 10; 1 Akor. 11:23-26; 15:58; Aef. 5:1-33.
M’masiku otsiriza ano, tikufunika kuti tizipezeka pa misonkhano nthawi zonse kuti tizilimbikitsidwa
4 Masiku ano, misonkhano yachikhristu imachitika potsatira chitsanzo cha mmene inkachitikira munthawi ya atumwi. Timamvera malangizo ouziridwa opezeka pa Aheberi 10:24, 25, akuti: “Tiyeni tiganizirane. . . . Tisaleke kusonkhana pamodzi, monga mmene ena achizolowezi chosafika pamisonkhano akuchitira. Koma tiyeni tilimbikitsane, ndipo tiwonjezere kuchita zimenezi, makamaka pamene mukuona kuti tsikulo likuyandikira.” M’masiku otsiriza ano, pamene tikukumana ndi mavuto ambiri, tikufunika kuti tizipezeka pa misonkhano nthawi zonse kuti tizilimbikitsidwa komanso kuti tipitirizebe kukhala olimba ndi okhulupirika kwa Mulungu. (Aroma 1:11, 12) Akhristufe tikukhala pakati pa m’badwo wopotoka maganizo ndi wokhotakhota. Komabe sititengera makhalidwe oipa komanso mzimu wa dziko wosaopa Mulungu. (Afil. 2:15, 16; Tito 2:12-14) Palibe kwina kumene tingakonde kukhala kuposa kukhala ndi anthu a Yehova. (Sal. 84:10) Komanso palibe chilichonse chimene chingakhale chopindulitsa kuposa kuphunzira ndi kukambirana Mawu a Mulungu. Tiyeni tione misonkhano yosiyanasiyana yomwe inakonzedwa n’cholinga choti izitipindulitsa.
MSONKHANO WA KUMAPETO KWA MLUNGU
5 Mbali yoyamba ya msonkhano wa kumapeto kwa mlungu imakhala nkhani ya onse ya m’Baibulo yomwe amakonzera anthu onse amene amabwera kudzasonkhana ndipo ena mwa anthuwa amakhala oti n’koyamba kupezeka pamisonkhano. Anthu onse, kaya akhale amene angoyamba kumene kusonkhana kapena ofalitsa a mpingowo, amapindula kwambiri mwauzimu ndi nkhani ya onseyi.—Mac. 18:4; 19:9, 10.
6 Khristu Yesu, atumwi ake komanso anthu ena ankachititsa misonkhano yofanana ndi imeneyi, yomwe anthu a Yehova amasangalala nayo masiku ano. Yesu ankakamba nkhani mwaluso kwambiri kuposa aliyense moti anthu ena amene anamvetserapo nkhani yake ananena kuti: “Palibe munthu amene analankhulapo ngati iyeyu n’kale lonse.” (Yoh. 7:46) Anthu amene ankamvetsera nkhani za Yesu, ankadabwa kwambiri chifukwa ankafotokoza zinthu mosonyeza kuti ali ndi ulamuliro. (Mat. 7:28, 29) Anthu amene ankagwiritsa ntchito zimene anamva ankapindula kwambiri. (Mat. 13:16, 17) Nawonso atumwi anatengera chitsanzo chake. Pa Machitidwe 2:14-36, timawerenga za nkhani yogwira mtima imene Petulo anakamba pa Pentekosite mu 33 C.E. Anthu ambiri anakhudzidwa mtima atamva nkhani imeneyi ndipo anabatizidwa. Patapita nthawi, anthu enanso anakhala ophunzira atamvetsera nkhani imene Paulo anakamba ku Atene.—Mac. 17:22-34.
7 Masiku anonso anthu ambiri amapindula ndi nkhani za onse zimene zimakambidwa pa mpingo komanso pa misonkhano ikuluikulu. Nkhani zimenezi zimatikumbutsa mfundo zachikhristu ndi kutithandiza kukhalabe okhulupirika pogwira ntchito za Ufumu. Tikamaitanira anthu achidwi, timathandiza anthu ambiri kuti amve uthenga wa m’Baibulo.
8 Nkhani za onse zimene zimakambidwa zimakhala ndi mitu yosiyanasiyana. Nkhani zina zimafotokoza mfundo komanso maulosi a m’Baibulo, malangizo a m’Malemba othandiza mabanja, mavuto amene achinyamata amakumana nawo komanso makhalidwe achikhristu. Nkhani zina zimafotokoza za zinthu zochititsa chidwi zimene Yehova analenga. Pomwe zina zimafotokoza mfundo zimene tingaphunzire kuchokera kwa anthu otchulidwa m’Baibulo omwe anasonyeza chikhulupiriro komanso kulimba mtima.
9 Kuti tipindule kwambiri ndi nkhani za onse, ndi bwino kuti tizimvetsera mwatcheru ndipo tizitsegula Baibulo lathu akatchula lemba loti liwerengedwe komanso kutsatira pamene akuwerenga ndi kulifotokozera. (Luka 8:18) Tikamayesetsa kuchita zimenezi, zidzatithandiza kuti tigwire mwamphamvu zimene taphunzira ndi kuzigwiritsa ntchito.—1 Ates. 5:21.
10 Ngati pali abale okwanira okamba nkhani za onse, mpingo umakhala ndi nkhani ya onse mlungu uliwonse. Mipingo imene ilibe okamba nkhani okwanira ikhozabe kumakhala ndi nkhani za onse mlungu uliwonse ngati itamapempha okamba nkhani ena kuchokera m’mipingo yoyandikana nayo. Koma ngati m’deralo mulibe okamba nkhani okwanira, mipingo imayesetsabe kukamba nkhanizi pafupipafupi mmene angathere.
11 Mbali yachiwiri ya msonkhano wa kumapeto kwa mlungu ndi Phunziro la Nsanja ya Olonda. Pa phunziroli, anthu amakambirana mafunso a mu nkhani za mu Nsanja ya Olonda yophunzira. Phunziro la Nsanja ya Olonda ndi njira imene Yehova amatipatsira chakudya chauzimu cha pa nthawi yake.
12 Nthawi zambiri nkhani zimene timaphunzira zimasonyeza mmene tingagwiritsire ntchito mfundo za m’Baibulo pa moyo wathu. Zimalimbikitsanso Akhristu kulimbana ndi “mzimu wa dziko” ndi kupewa makhalidwe oipa. (1 Akor. 2:12) Nsanja ya Olonda imatithandiza kudziwa tanthauzo latsopano la zimene Baibulo limaphunzitsa ndi maulosi a m’Baibulo ndipo zimenezi zimatithandiza kuti timvetse choonadi ndi kupitiriza kuyenda m’njira ya olungama. (Sal. 97:11; Miy. 4:18) Kupezeka pa Phunziro la Nsanja ya Olonda komanso kuyankhapo kumathandiza kuti tizisangalala chifukwa cha chiyembekezo chimene tili nacho cha dziko latsopano lolungama. (Aroma 12:12; 2 Pet. 3:13) Misonkhano yathu yachikhristu imatithandiza kukhala ndi makhalidwe amene mzimu woyera umatulutsa komanso imatithandiza kuti tipitirize kukhala ndi mtima wofuna kutumikira Yehova mwakhama. (Agal. 5:22, 23) Imatilimbikitsanso kupirira mayesero komanso kumanga ‘maziko abwino a tsogolo lathu’ n’cholinga choti ‘tigwire mwamphamvu moyo weniweniwo.’—1 Tim. 6:19; 1 Pet. 1:6, 7.
13 Kodi tingatani kuti tizipindula mokwanira ndi njira yolandirira chakudya chauzimu imeneyi? Tiyenera kukonzekereratu phunziroli patokha kapena limodzi ndi banja lathu ndipo tiyenera kuwerenga malemba amene sanagwidwe mawu munkhaniyo. Pamene tikuyankha, tiyenera kufotokoza mfundo zathu m’mawu athuathu. Kuchita zimenezi kudzathandiza kuti mfundo za choonadi zikhazikike mumtima mwathu komanso zidzathandiza kuti anthu ena apindule ndi ndemanga zathu zosonyeza kuti tili ndi chikhulupiriro. Komanso tikamamvetsera mwachidwi pamene ena akuyankha, tidzapindula ndi phunziro la mlungu uliwonse.
MSONKHANO WA MKATI MWA MLUNGU
14 Mlungu uliwonse, mipingo imasonkhana pa Nyumba ya Ufumu kuti ichite msonkhano wa Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu. Msonkhanowu umakhala ndi mbali zitatu zomwe cholinga chake n’kutithandiza kuti tikhale “oyenera kugwira ntchito” monga atumiki a Mulungu. (2 Akor. 3:5, 6) Zinthu zoyenera kukambirana zimapezeka mu Kabuku ka Msonkhano wa Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu komwe timalandira mwezi ndi mwezi. Kabukuka kamakhalanso ndi zitsanzo za zimene tinganene mu utumiki.
15 Mbali yoyamba ya msonkhano umenewu, ya mutu wakuti Chuma Chopezeka M’Mawu a Mulungu, imatithandiza kudziwa mmene zinthu zinalili pa nthawi imene nkhani za m’Baibulo zinkalembedwa komanso kumvetsa nkhanizo ndi kuona mmene tingagwiritsire ntchito malangizo ake. Mbali imeneyi imakhala ndi nkhani, kuwerenga, ndiponso kukambirana mfundo za m’Baibulo za m’machaputala amene tawerenga mlungu umenewo. Zinthu zothandiza pophunzira nkhani zimenezi zimapezeka mu Kabuku ka Msonkhano wa Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu. Kukambirana mfundo za m’Baibulo m’njira imeneyi kumatithandiza pa moyo wathu komanso pophunzitsa ena, n’cholinga choti ‘tikhale oyenerera bwino ndi okonzeka mokwanira kuchita ntchito iliyonse yabwino.’—2 Tim. 3:16, 17.
16 Mutu wa mbali yachiwiri ndi wakuti, Kuphunzitsa Mwaluso mu Utumiki ndipo cholinga chake ndi kuthandiza onse kukonzekera zokanena mu utumiki kuti akulitse luso lawo lolalikira komanso kuphunzitsa. Kuwonjezera pa nkhani za ophunzira, timaonera komanso kukambirana mavidiyo a zitsanzo za zimene tinganene mu utumiki. Mbali imeneyi imatithandiza kuti tikhale ndi “lilime la anthu ophunzitsidwa bwino” kuti ‘tidziwe mmene tingamuyankhire munthu wotopa.’—Yesaya 50:4.
17 M’mbali yachitatu, yakuti Moyo Wathu Wachikhristu, timakambirana mmene tingagwiritsire ntchito mfundo za m’Baibulo pa zochita zathu za tsiku ndi tsiku. (Sal. 119:105) Pulogalamu yaikulu m’mbali imeneyi ndi Phunziro la Baibulo la Mpingo. Pa Phunziro la Baibulo la Mpingo, wochititsa amafunsa mafunso amene ali munkhaniyo ndipo omvera amapereka mayankho ngati mmene timachitira pa Phunziro la Nsanja ya Olonda.
18 Kabuku ka Msonkhano wa Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu ka mwezi uliwonse kakangofika, wogwirizanitsa ntchito za akulu amakawerenga mofatsa kuti adziwe nkhani zimene zilimo kenako amapanga ndandanda ya omwe angakambe nkhanizo. Kapena angapemphe mkulu wina kuti apange ndandandayo. Mlungu uliwonse, mkulu aliyense amene ali ndi luso lophunzitsa ndipo anavomerezedwa ndi bungwe la akulu ndi amene amakhala tcheyamani wa msonkhanowo. Udindo wake ndi kuonetsetsa kuti msonkhano wayamba ndi kutha pa nthawi yake komanso kuyamikira ndi kupereka malangizo kwa anthu amene akamba nkhani za ophunzira.
19 Ngati nthawi zonse timakonzekera, kupezekapo ndiponso kutenga nawo mbali pa Msonkhano wa Utumiki Komanso Moyo Wathu, tidzadziwa bwino Malemba, kumvetsa mfundo za m’Baibulo komanso tidzaphunzira kulalikira uthenga wabwino molimba mtima ndiponso tidzakhala ndi luso pophunzitsa mu utumiki. Onse amene amapezeka pa msonkhanowu, ngakhale omwe sanabatizidwe, amapindula ndi mfundo zolimbikitsa zimene zimakambidwa komanso chifukwa chocheza ndi abale ndi alongo. Pokonzekera msonkhanowu mungagwiritse ntchito Watchtower Library, JW Library®, LAIBULALE YA PA INTANETI ya Watchtower™ (ngati ilipo m’chinenero chanu) kapena mungagwiritse ntchito laibulale ya pa Nyumba ya Ufumu. Laibulale ya pa Nyumba ya Ufumu imakhala ndi mabuku onse amene gulu linatulutsa, kuphatikizapo Watch Tower Publications Index, Buku la Mboni za Yehova Lofufuzira Nkhani, ndi mabuku ena othandiza pofufuza nkhani. Aliyense angathe kugwiritsa ntchito mabuku amenewa misonkhano isanayambe kapena itatha.
MISONKHANO YOKONZEKERA UTUMIKI
20 Pa nthawi zosiyanasiyana mkati mwa mlungu ndiponso kumapeto kwa mlungu, magulu a ofalitsa amasonkhana mwachidule kuti akonzekere utumiki wakumunda. Nthawi zambiri msonkhano umenewu umachitikira m’nyumba za abale kapena pamalo ena abwino. N’zothekanso kuchitira msonkhanowu pa Nyumba ya Ufumu. Kuchitira misonkhano yokonzekera utumiki m’malo osiyanasiyana kumathandiza kuti ofalitsa asavutike kupita kumsonkhanowo komanso kupita kumene akalalikire. Popeza ofalitsa ake amakhala ochepa, savuta kuwagawa moti amayamba kulalikira mwamsanga. Zimakhalanso zosavuta kwa woyang’anira kagulu kuthandiza mokwanira munthu aliyense wa m’gulu lake. Ngakhale kuti zimakhala zothandiza gulu lililonse likamakumana palokha, nthawi zina zingafunike kuti magulu angapo azikumana pamodzi. Mwachitsanzo, ngati ofalitsa amene amalowa mu utumiki mkati mwa mlungu amakhala ochepa, zingakhale bwino kuphatikiza timagulu tingapo kapena kukumana pamodzi mpingo wonse pa Nyumba ya Ufumu kapena pamalo ena. Kuchita zimenezi kungathandize kuti wofalitsa aliyense apeze woyenda naye. Mipingo ingaone ngati zili zothandiza kuti mpingo wonse uzisonkhana pamodzi pa Nyumba ya Ufumu pa masiku a holide. Angasankhenso kuti azisonkhana limodzi monga mpingo pambuyo pa Phunziro la Nsanja ya Olonda.
21 Ngati kagulu kalikonse kamakumana pakokha, woyang’anira kagulu ndi amene amachititsa msonkhano wokonzekera utumiki wakumunda. Nthawi zina woyang’anira kagulu angapemphe wothandiza wake kapena m’bale woyenerera kuti achititse msonkhanowo. Wochititsa msonkhanoyo ayenera kukambirana nawo mfundo zimene zingakhale zothandiza mu utumiki. Kenako pambuyo poti aliyense wauzidwa woyenda naye komanso wadziwa gawo lokalalikira, m’bale wina ayenera kupereka pemphero. Zikatero anthuwo ayenera kunyamuka nthawi yomweyo kupita kugawo limene akukalalikira. Misonkhano imeneyi iyenera kukhala ya 5 kapena 7 minitsi ndipo iyenera kufupikirapo ngati ikuchitika pambuyo pa misonkhano ya mpingo. Mfundo zofotokozedwa pa misonkhano imeneyi ziyenera kukhala zolimbikitsa komanso zothandiza anthu kudziwa zoyenera kuchita akalowa mu utumiki. Ofalitsa atsopano komanso anthu ena amene akufunikira thandizo angagawidwe kuti ayende ndi ofalitsa amene akhala akulalikira kwa nthawi yaitali n’cholinga choti aziwathandiza.
MMENE MISONKHANO IMACHITIKIRA M’MIPINGO YATSOPANO KAPENA YAING’ONO
22 Anthu ambiri akuphunzira choonadi ndipo zimenezi zachititsa kuti mipingo iwonjezeke. Nthawi zambiri woyang’anira dera amapempha kuti mpingo watsopano ukhazikitsidwe. Koma nthawi zina amaona kuti ndi bwino kungokhazikitsa timagulu tomwe timayang’aniridwa ndi mpingo wapafupi.
23 Mipingo ina ing’onoing’ono ingakhale ndi alongo okhaokha. Zikatero, mlongo amene akupemphera m’malo mwa mpingo kapena kuchititsa misonkhano ayenera kuvala chinachake kumutu mogwirizana ndi zimene Malemba amanena. (1 Akor. 11:3-16) Nthawi zambiri angachite zimenezi atakhala pansi moyang’anana ndi anthu. Alongo sakamba nkhani ngati mmene amachitira abale pamisonkhano. Iwo amangowerenga nkhaniyo n’kupereka ndemanga ndipo nthawi zina angakambirane nkhaniyo ndi alongo ena kapena angachite chitsanzo chosonyeza mfundo za mu nkhaniyo. Ofesi ya nthambi imapempha mlongo mmodzi kuti azilemberana makalata ndi ofesiyo komanso kuti azichititsa misonkhano. Kenako abale oyenerera akapezeka, ndi amene amasamalira ntchito zimenezi.
MISONKHANO YADERA
24 Chaka chilichonse, mipingo imene ili m’dera limodzi imachita misonkhano yadera iwiri yatsiku limodzi. Misonkhanoyi imatipatsa mpata ‘wofutukula mitima yathu’ pocheza ndi Akhristu anzathu. (2 Akor. 6:11-13) Gulu la Yehova limasankha mitu ya misonkhano yochokera m’Malemba komanso limakonza nkhani zosiyanasiyana zogwirizana ndi zofunika za anthu. Nkhanizi zimakambidwa m’njira zosiyanasiyana. Zina zimakambidwa ndi munthu mmodzi, zina zimakhala ndi zitsanzo, zina zimakhala ndi mbali yofunsa mafunso pamene zina zimakhala ndi mbali ya munthu akulankhula yekha. Malangizo a pa nthawi yake omwe amaperekedwa pa misonkhanoyi amalimbikitsa onse amene abwera. Pa misonkhanoyi pamakhalanso mwayi woti ophunzira atsopano abatizidwe posonyeza kuti anadzipereka kwa Yehova.
MISONKHANO YACHIGAWO
25 Chaka chilichonse timakhala ndi msonkhano wachigawo kamodzi pachaka. Nthawi zambiri msonkhano umenewu umakhala wa masiku atatu ndipo pamabwera anthu ochokera m’mipingo ya m’madera osiyanasiyana. Maofesi a nthambi amene amayang’anira magawo ang’onoang’ono angaone kuti n’zothandiza kuti mipingo yonse isonkhane malo amodzi. M’mayiko ena misonkhanoyi imachitika mosiyana ndi kwina chifukwa cha mmene zinthu zilili m’dzikomo kapena potsatira malangizo ochokera ku Bungwe Lolamulira. Nthawi zina m’mayiko ena mumachitika misonkhano yachigawo yapadera kapena ya mayiko ndipo pa misonkhano imeneyi pamabwera Mboni za Yehova zambiri zochokera m’mayiko osiyanasiyana. Kwa zaka zambiri njira imene imagwiritsidwa ntchito podziwitsa anthu za misonkhanoyi yathandiza kuti anthu ambiri amve uthenga wabwino wa Ufumu.
26 Kwa atumiki a Yehova, misonkhano imeneyi imakhala nthawi yosangalatsa kwambiri yolambirira limodzi Mulungu. Misonkhano ikuluikulu imeneyi imatipatsa mwayi womvetsa mfundo za choonadi. Pa misonkhano ina ngati imeneyi pamatulutsidwa mabuku atsopano oti tizigwiritsa ntchito pophunzira patokha, kumpingo kapena mu utumiki wakumunda. Pa misonkhanoyi pamakhalanso mwayi woti anthu atsopano abatizidwe. Chinthu china chimene chimapangitsa misonkhano ikuluikulu kukhala yapadera n’choti imasonyeza mmene tikuchitira mwauzimu. Imatsimikizira kuti anthu a Yehova akupezeka padziko lonse ndipo ndi ogwirizana komanso ali ndi chizindikiro chosonyeza kuti ndi ophunzira a Yesu Khristu.—Yoh. 13:35.
27 Timalimbikitsidwa kuchita zimene Yehova amafuna tikamayesetsa kusonkhana limodzi ndi anthu a Yehova pa misonkhano ya mpingo komanso ikuluikulu. Misonkhanoyi imatitetezanso kuti tisatengere makhalidwe a m’dzikoli omwe angasokoneze chikhulupiriro chathu. Imatipatsanso mwayi wotamanda ndi kulemekeza Yehova. (Sal. 35:18; Miy. 14:28) Tiyenera kuyamikira Yehova chifukwa chotipatsa misonkhano imeneyi yomwe imatilimbikitsa m’masiku otsiriza ano.
CHAKUDYA CHAMADZULO CHA AMBUYE
28 Kamodzi pa chaka, Mboni za Yehova padziko lonse zimasonkhana pamwambo wokumbukira imfa ya Yesu Khristu, womwe umadziwikanso kuti Chakudya Chamadzulo cha Ambuye. (1 Akor. 11:20, 23, 24) Kwa anthu a Yehova, umenewu ndi msonkhano wapadera kwambiri kuposa misonkhano yonse imene amakhala nayo pa chaka. Yesu Khristu anatipatsa lamulo lomveka bwino loti tizichita mwambo wa Chikumbutso.—Luka 22:19.
29 Deti la Chikumbutso limakhala logwirizana ndi deti la Pasika lotchulidwa m’Baibulo. (Eks. 12:2, 6; Mat. 26:17, 20, 26) Mwambo wa Pasika unkachitika kamodzi pa chaka pokumbukira kupulumutsidwa kwa Aisiraeli ku Iguputo m’chaka cha 1513 B.C.E. Pa nthawi imeneyo, Yehova anasankha tsiku la 14 la mwezi woyamba pa kalendala yawo kuti adye nsembe ya Pasika kenako n’kunyamuka kuchoka ku ukapolo ku Iguputo. (Eks. 12:1-51) Detilo limadziwika powerenga masiku 13 kuyambira patsiku limene mwezi waonekera ku Yerusalemu chakumapeto kwa mwezi wa March kapena kumayambiriro kwa April. Nthawi zambiri, mwambo wokumbukira imfa ya Yesu Khristu umachitika patsiku loyamba limene mwezi wathunthu waonekera.
30 Pa Mateyu 26:26-28 pali mawu a Yesu ofotokoza mmene mwambowu uyenera kuchitikira. Pa mwambowu zizindikiro zimene zimagwiritsidwa ntchito sizisintha n’kukhala thupi lenileni ndi magazi enieni a Khristu, zimangokhala zizindikiro chabe ndipo zimadyedwa ndi anthu amene adzalamulire ndi Yesu Khristu kumwamba. (Luka 22:28-30) Akhristu ena onse odzipereka komanso anthu achidwi amalimbikitsidwa kupezeka pa mwambo wa Chakudya Chamadzulo cha Ambuye. Akapezeka pamwambowu, amasonyeza kuti amayamikira zimene Yehova anachita potumiza Mwana wake Yesu Khristu kuti adzapulumutse anthu. Chikumbutso chikatsala pang’ono kuchitika, pamakhala nkhani yapadera yomwe imakonzedwa n’cholinga chothandiza anthu achidwi kuti adzapezeke pamwambowu komanso kuti apitirize kuphunzira Baibulo.
31 Mboni za Yehova zimayembekezera mwachidwi nthawi yoti zisonkhane pamodzi pamisonkhano yosiyanasiyana. Pamisonkhano imeneyi ‘timalimbikitsana pa chikondi ndi ntchito zabwino.’ (Aheb. 10:24) Kapolo wokhulupirika ndi wanzeru amakonza misonkhanoyi moganizira zimene tikufunikira pa moyo wathu wauzimu. Atumiki onse a Yehova komanso anthu achidwi, amalimbikitsidwa kuti ayenera kumapezeka nthawi zonse pa misonkhano imeneyi. Kuyamikira ndi mtima wonse zimene Yehova amatipatsa kudzera m’gulu lake, kumatithandiza kukhala ogwirizana kwambiri. Koposa zonse, pa misonkhanoyi timatamanda ndi kulemekeza Yehova.—Sal. 111:1.