‘Kuleredwa M’mawu Achikhulupiriro’
1 Kukhala ndi moyo wodzipereka kwa Mulungu kumafuna kuyesetsa kwambiri. (1 Tim. 4:7-10) Tikhoza kutopa ndi kubwerera m’mbuyo mosavuta ngati tingayese kuchita zimenezi mu mphamvu za ife eni. (Yes. 40:29-31) Njira imodzi imene tingapezere mphamvu kuchokera kwa Yehova ndiyo mwa ‘kuleredwa m’mawu a chikhulupiriro.’—1 Tim. 4:6.
2 Chakudya Chauzimu Chochuluka: Yehova akupereka chakudya chauzimu chochuluka kudzera m’Mawu ake ndiponso kudzera mwa “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru.” (Mat. 24:45) Kodi tikuchita mbali yathu kuti tipindule nacho? Kodi timawerenga Baibulo tsiku lililonse? Kodi tili ndi nthawi yochita phunziro laumwini ndi kusinkhasinkha? (Sal. 1:2, 3) Chakudya chopatsa thanzi choterechi chimatilimbikitsa ndi kutiteteza ku zinthu zowononga za dziko la Satanali. (1 Yoh. 5:19) Tikamadzaza maganizo athu ndi zinthu zabwino ndi kuzigwiritsa ntchito pa moyo wathu, Yehova adzakhala nafe.—Afil. 4:8, 9.
3 Yehova amatilimbitsanso kudzera m’misonkhano ya mpingo. (Aheb. 10:24, 25) Malangizo auzimu ndi macheza abwino amene amapezeka kumisonkhano imeneyi amatithandiza kuti tikhale olimba ngakhale pamene takumana ndi mayesero. (1 Pet. 5:9, 10) Mkristu wina wachinyamata anati: “Ndimakhala ndili kusukulu tsiku lonse lathunthu, ndipo ndimatopa. Koma misonkhano imakhala ngati chitsime cha madzi m’chipululu, kumene ndimatsitsimulidwa kuti ndikhale wokonzeka kupiriranso kusukulu tsiku lotsatira.” Ndithudi, timadalitsidwa chifukwa cha kuyesetsa kumene timachita kuti tikapezeke kumisonkhano.
4 Kulalikira Choonadi: Kulalikira kwa ena chinali ngati chakudya kwa Yesu. Kunam’patsa nyonga. (Yoh. 4:32-34) Mofananamo, tikamalankhula kwa ena za malonjezo osangalatsa a Mulungu, timamva bwino. Kukhala otanganidwa mu utumiki kumathandiza mtima ndi maganizo athu kukhala pa Ufumu ndi madalitso amene akubwera posachedwapa. Kunena zoona, zimenezi zimatitsitsimula.—Mat. 11:28-30.
5 Ndifedi odala kuti tikuthandizika ndi chakudya chauzimu chochuluka chimene Yehova akupereka kwa anthu ake masiku ano. Ndiyetu tiyeni tipitirizebe kufuula mosangalala kum’tamanda.—Yes. 65:13, 14.