“Iye Alimbitsa Olefuka”
1 Tonsefe timatopa nthawi zina. Sikuti timangotopa chifukwa cha ntchito yathu kapena zochita zathu zina, koma timatopanso chifukwa cha zovuta zina zimene timakumana nazo mu “nthawi yovuta yoikika” ino. (2 Tim. 3:1) Poti ndife atumiki a Yehova, kodi tingapeze bwanji mphamvu zotithandiza kuti tisafooke muutumiki wathu? Timatero podalira Yehovayo, amene ali “wolimba mphamvu.” (Yes. 40:26) Iye amadziwa zimene tikufunikira ndipo amafunitsitsa kutithandiza.—1 Pet. 5:7.
2 Njira za Yehova Zotithandizira: Yehova amatilimbikitsa pogwiritsa ntchito mzimu wake woyera, umene anagwiritsa ntchito polenga chilengedwe chonse. Mzimu umenewutu ndi mphamvu yoposa mphamvu zilizonse. Mzimu wa Mulungu umatithandiza ‘kutenganso mphamvu’ tikatopa. (Yes. 40:31) Dzifunseni kuti: ‘Kodi ndi liti pamene ndinapemphera kuti mzimu woyera undipatse mphamvu zokwaniritsira udindo wanga monga Mkhristu?’—Luka 11:11-13.
3 Powerenga ndi kusinkhasinkha Mawu ouziridwa ndi Mulungu tsiku ndi tsiku, ndiponso podya chakudya chauzimu mwa kuwerenga mabuku achikhristu mokhazikika, tidzakhala ngati mtengo wokula bwino, “wooka pa mitsinje ya madzi; wakupatsa chipatso chake pa nyengo yake, tsamba lake lomwe losafota.”—Sal. 1:2, 3.
4 Yehova amagwiritsanso ntchito Akhristu anzathu, kuti akhale ‘otilimbikitsa.’ (Akol. 4:10, 11) Iwowa amatilimbikitsa ku misonkhano pocheza nawo, ndiponso pomvera ndemanga ndi nkhani zawo. (Mac. 15:32) Akulu mumpingo ndiwo makamaka amatithandiza mwauzimu ndi kutitsitsimula.—Yes. 32:1, 2.
5 Utumiki: Ngati mwayamba kutopa, musaganize zosiya kulalikira. Kuchita nawo utumiki mokhazikika n’kosiyana ndi zochita zathu zambiri zotopetsa, chifukwa kumatitsitsimula. (Mat. 11:28-30) Kuuza ena uthenga wabwino kumatithandiza kuika maganizo athu pa Ufumu wa Mulungu ndi kuganizira kwambiri za madalitso osangalatsa a moyo wosatha.
6 Pali zambiri zoti tichite dongosolo loipali lisanawonongedwe. Tili ndi zifukwa zambiri zosabwerera m’mbuyo muutumiki wathu, “modalira mphamvu imene Mulungu amapereka.” (1 Pet. 4:11) Yehova adzatithandiza kumaliza ntchito yathu, chifukwa “Iye alimbitsa olefuka.”—Yes. 40:29.