Mzimu wa Yehova Uli Nafe
1 Ife Mboni za Yehova tili ndi ntchito yaikulu. Yesu anati: “Uthenga Wabwino uyenera uyambe kulalikidwa kwa anthu a mitundu yonse.” (Marko 13:10) Kuiyang’ana ntchitoyo ndi maso aumunthu, ingaoneke ngati yosatheka, koma ndi yotheka ndithu. Tili ndi mphamvu yaikulu m’chilengedwe chonse chino yomwe ikutichirikiza—mzimu wa Mulungu.—Mat. 19:26.
2 Umboni wa m’Zaka za Zana Loyamba: Ponena za iye mwini, Yesu anagwira mawu ulosi wa Yesaya nati: “Mzimu wa Ambuye, [“Yehova,” NW], uli pa ine . . . ndiuze anthu osauka Uthenga Wabwino.” (Luka 4:17, 18) Asanakwere kumwamba anawauza atumwi ake mofananamonso kuti iwo adzalandira mphamvu ya mzimu woyera kuti akachitire umboni mpaka “[ku]malekezero ake a dziko.” Pambuyo pake, Filipo anatsogozedwa ndi mzimu woyera kukalalikira mdindo wa ku Aitiopiya, mzimu woyera unatumiza Petro kwa kazembe wa Roma, ndipo unatumiza Paulo ndi Barnaba kukalalikira kwa anthu Amitundu. Ndani yemwe akanaganiza zoti anthu ngati amenewo akanamva choonadi? Koma anamvadi.—Mac. 1:8; 8:29-38; 10:19, 20, 44-48; 13:2-4, 46-48.
3 Umboni Wamakono: Buku la Chivumbulutso limasonyeza kuti mzimu woyera ukuchitapo kanthu pantchito yolalikira yalero, chifukwa limati: “Mzimu ndi mkwatibwi anena, Idzani. . . . Iye wofuna, atenge madzi a moyo kwaulere.” (Chiv. 22:17) Mzimuwo ndiwo ukusonkhezera gulu lamkwatibwi wa Kristu limodzi ndi anzawo a “nkhosa zina” kulalikira uthenga wabwino kwa anthu onse. (Yoh. 10:16) Tizikhala olimba mtima polalikira, tisamazengereze kufikira anthu onse, tikumadalira kuti mzimu wa Mulungu uzitithandiza. Yearbook ya 1998 ikupereka umboni wosakanika wakuti mzimu wa Mulungu ukali pa atumiki ake. Tangoonani zotsatira zake! Zaka ziŵiri zautumiki zapitazo, pa avareji, anthu oposa 1,000 ankabatizidwa tsiku lililonse.
4 Dziŵani kuti mzimu wa Mulungu udzakhalabe pa ife pamene tikulalikira uthenga wa Ufumu mpaka pamlingo umene Yehova akufuna. Kudziŵa zimenezi kuyenera kutilimbikitsa ndi kutisonkhezera kuyesetsadi pantchito yofunika ya Ufumu.—1 Tim. 4:10.