Mmene Tingakopere Ena
1 Mtumwi Paulo ankadziŵika monga mtumiki wodziŵa kukopa anthu. (Mac. 19:26) Ngakhale Mfumu Agripa anamuuza kuti: “Ndi kundikopa pang’ono ufuna kundiyesera Mkristu.” (Mac. 26:28) N’chifukwa chiyani utumiki wa Paulo unali wokopa kwambiri? Ankakamba za m’Malemba mogwira mtima, komanso nkhani zoyenerana ndi omvetsera ake.—Mac. 28:23.
2 Motsanzira Paulo, ifenso tiyenera kukhala okopa mu utumiki wathu. Tingachite motani zimenezi? Mwa kugwiritsa ntchito kuzindikira polankhula anthu komanso pomvetsera zimene akunena. (Miy. 16:23) Masitepe ofunika atatu adzatithandiza kuchita zimenezi.
3 Mvetserani Mwatcheru: Pamene munthuyo akulankhula, mvetserani kuti mupeze mfundo zimene mukugwirizana kuti makambirano anu agone pamenepo. Ngati akutsutsa, yesani kupeza chifukwa chake. Izi zidzakuthandizani kudziŵa zikhulupiriro zake zenizeni, chifukwa chake amakhulupirira zimenezo, ndiponso zimene zinam’khutiritsa kuti zimenezo n’zoona. (Miy. 18:13) M’funseni mwanzeru.
4 Funsani Mafunso: Munthuyo akati amakhulupirira Utatu wa Mulungu, m’funseni kuti: “Kodi kuyambira kale mwakhala mukukhulupirira Utatu wa Mulungu?” Kenako funsani kuti: “Kodi munafufuza bwinobwino zimene Baibulo limanena pankhaniyi?” Mungafunsenso kuti: “Mulungu akanakhala kuti ndi Utatu, kodi Baibulo silikananena zimenezi momveka bwino?” Mayankho ake adzakuthandizani kukambirana naye zimene Malemba amanena.
5 Gwiritsani Ntchito Mfundo Zogwira Mtima: Mboni ina inafunsa mayi wokhulupirira kuti Yesu ndi Mulungu motere: ‘Mutafuna kusonyeza kuti anthu aŵiri ndi ofanana, kodi mungagwiritse ntchito ubale uti pabanja?’ Anati: “Wa abale aŵiri.” Mboniyo inati: “Mwinanso mapasa ofanana. Koma Yesu potiphunzitsa kuona Mulungu monga Atate ndi iye monga Mwana, kodi amafuna kusonyezanji?” Mayi uja anazindikira mfundo yake kuti wina ali wamkulu ndiponso wamphamvu zedi. (Mat. 20:23; Yoh. 14:28; 20:17) Luso la kukopa linakhudza maganizo ndi mtima wa mayiyu.
6 Ndi zoona kuti si onse amene amamvetsera choonadi, ngakhale ulaliki wathu ukhale wogwira mtima ndi wolondola chotani. Komabe, monga Paulo, tikhale akhama pofunafuna oona mtima m’gawo lathu, kuwakopa kuvomereza uthenga wa Ufumu.—Mac. 19:8.