Ndandanda ya Misonkhano ya Utumiki
Mlungu Woyambira February 12
Mph. 10: Zilengezo za pampingo. Zilengezo zosankhidwa mu Utumiki Wathu wa Ufumu. Bokosi la Mafunso. Ikambidwe ndi wa m’Komiti ya Utumiki ya Mpingo. Gogomezani kuti wofuna ubatizo ayenera kukhala wofalitsa wosabatizidwa, wokonzeka kudzipatulira kwa Yehova kapena amene wachita kale zimenezi. Si bwino munthu wofuna kubatizidwa kudikira mpaka msonkhano utatsala pang’ono kuchitika kuti anene maganizo ake ofuna kubatizidwa.
Mph. 15: “M’lemekezeni Yehova ndi Ntchito Zabwino.” Kambani mawu oyamba m’mphindi yosakwana imodzi, ndiyeno kambiranani mwa mafunso ndi mayankho.
Mph. 20: “Mmene Tingakopere Ena.” Wochititsa Phunziro la Buku la Mpingo akambirane nkhaniyi komanso mfundo zimene wasankha mu Nsanja ya Olonda ya May 15, 1998 masamba 21-3 ndi mpainiya kapena wofalitsa wochita bwino. Apende bokosi la patsamba 23 lakuti, “Kufika Wophunzira Wanu Pamtima.” Asankhe chikhulupiriro chonyenga chofala m’gawolo, ndiyeno akambirane mmene angam’tsimikizire munthu zimene Baibulo likunena pankhaniyo.
Nyimbo Na. 208 ndi pemphero lomaliza.
Mlungu Woyambira February 19
Mph. 8: Zilengezo za pampingo. Lipoti la maakaunti.
Mph. 15: Zosoŵa za pampingo.
Mph. 22: “Bukitsani Dzina la Yehova ndi Zochita Zake.”a Mkulu afotokoze zinthu zapadera zimene mpingo ukukonza kuti udzachite zochuluka mu March ndi April, ndiponso ntchito yolimbikitsa anthu ambiri kuchita upainiya wothandiza. Khalani ndi ena amene anachita upainiya mu April chaka chatha kuti asimbe mmene anasangalalira. Gogomezani mmene tingathandizire wofalitsa aliyense woyeneretsedwa amene anazilala kuyambiranso utumiki komanso kuthandiza ana ndi ophunzira Baibulo ena kuyenerera kukhala ofalitsa osabatizidwa.—Onani Bokosi la Mafunso mu Utumiki Wathu wa Ufumu wa November 2000.
Nyimbo Na. 27 ndi pemphero lomaliza.
Mlungu Woyambira February 26
Mph. 8: Zilengezo za pampingo. Kumbutsani ofalitsa kupereka malipoti awo a muutumiki wakumunda a February.
Mph. 12: Zitsanzo za Ulaliki Pogaŵira Buku la Chidziŵitso. Kodi muli ndi ulaliki umene mungagwiritse ntchito pogaŵira buku la Chidziŵitso m’March? Mutayang’ana Utumiki Wathu wa Ufumu wa m’buyomo masamba akumapeto, mudzapeza malingaliro apaulendo woyamba, ambiri a iwo alinso ndi malingaliro apaulendo wobwereza. Pendani zitsanzo ziŵiri kapena zitatu za maulaliki ameneŵa. (December 1995; March, June, November 1996; June 1997; March 1998) Khalani ndi zitsanzo ziŵiri za maulaliki a m’kope la November 1996 oyambira mwachindunji maphunziro a Baibulo. Limbikitsani onse kuyesetsa kuyambitsa maphunziro a Baibulo atsopano.
Mph. 25: “Kuthandiza Ena pa Phunziro la Buku la Mpingo.” Ikambidwe ndi mkulu waluso pochititsa phunziro la buku.
Nyimbo Na. 64 ndi pemphero lomaliza.
Mlungu Woyambira March 5
Mph. 5: Zilengezo za pampingo.
Mph. 10: “Pulogalamu Yatsopano ya Msonkhano Wadera.” Mafunso ndi mayankho. Lengezani deti la msonkhano wadera ukudzawo, ndipo limbikitsani onse kudzakhalapo masiku onse aŵiriwo. Limbikitsani onse kuti achite khama kuitanira ophunzira Baibulo ku msonkhanowu. Kupezeka kwawo pamsonkhano kungawasonkhezere kumasonkhana ndi mpingo nthaŵi zonse.
Mph. 12: “Chitani Ntchito Mosangalala.”
Mph. 18: “Yehova Amapatsa Mphamvu.”b Funsani omvetsera mmene malembawo akugwirizanira ndi nkhaniyo.
Nyimbo Na. 108 ndi pemphero lomaliza.
[Mawu a M’munsi]
a Kambani mawu oyamba m’mphindi yosakwana imodzi, ndiyeno kambiranani mwa mafunso ndi mayankho.
b Kambani mawu oyamba m’mphindi yosakwana imodzi, ndiyeno kambiranani mwa mafunso ndi mayankho.