Zilengezo
◼ Mabuku ogaŵira mu February: Bulosha la Mulungu Amafunanji, kapena buku lililonse la masamba 192 limene mpingo uli nalo. March: Chidziŵitso Chotsogolera ku Moyo Wosatha. Tidzayesetsa kuyambitsa maphunziro a Baibulo apanyumba. April ndi May: Magazini a Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! Paulendo wobwereza mukapeza achidwi, aikeni pa anthu amene mumakawagaŵira magazini. Gaŵirani buku la Chidziŵitso kapena bulosha la Mulungu Amafunanji, n’cholinga choyambitsa maphunziro a Baibulo apanyumba.
◼ Woyang’anira wotsogolera kapena wina amene iye wam’sankha aŵerengere maakaunti a mpingo pa March 1, kapena mwamsanga pambuyo pa detilo. Akatha kuŵerengerako, lengezani kumpingo mukatha kupereka lipoti lotsatira la maakaunti.
◼ Mlembi ndi woyang’anira utumiki apende ntchito ya apainiya okhazikika onse. Ngati pali amene zikuwavuta kukwanitsa maola ofunikawo, akulu ayenera kukonza zowathandiza. Onani zina m’makalata a Sosaite apachaka a S-201. Onaninso ndime 12-20 m’mphatika ya Utumiki Wathu wa Ufumu wa October 1986.
◼ Polalikira m’gawo limene safola kaŵirikaŵiri, ofalitsa angagaŵire buku la Chidziŵitso kapena bulosha la Mulungu Amafunanji. Angagaŵire mabuku ena alionse ngati mwininyumba ali nazo kale zofalitsa tatchulazi. Ayenera kutenga mathirakiti amitundumitundu okasiya panyumba zimene sanapeze anthu kapena kupatsa anthu amene salandira mabuku athu. Ayenera kuyesetsa kubwerera kwa amene anachita chidwi, makamaka ngati amene akulalikira m’magawo ameneŵa ali apainiya apadera kapena ngati magawowo ali pafupi ndi mipingo yoyandikana nayo.
◼ Mipingo iyenera kuyamba kuoda ma Yearbook of Jehovah’s Witness a 2001 paoda yawo ya mabuku ya February. Ma Yearbook a 2001 adzakhalapo m’Chingelezi mokha. Mpaka pamene mabuku ameneŵa adzakhalapo ndi kutumizidwa, adzaonekera monga “Zoyembekezeredwa” pa mipambo yolongedzera katundu wa mipingo. Ma Yearbook a 2001 ndi zinthu zaoda yapadera, kusonyeza kuti mpingo ndiwo uyenera kufunsira mabukuŵa ngati wina wafunsira; mtumiki wa mabuku sayenera kuodera mpingo ameneŵa. Chotero, afunika kusunga bwino oda ya wofalitsa aliyense ya mabuku ameneŵa. (Chonde onani Malangizo a Watch Tower Ofunsira Mabuku, Gawo 3.)
◼ Zofalitsa Zatsopano Zimene Zilipo:
Ulosi wa Yesaya—Muuni wa Anthu Onse 1—Chingelezi
Mungathe Kukhala Bwenzi la Mulungu —Chicheŵa, Chingelezi
◼ Kaseti Yatsopano Imene Ilipo:
Kingdom Melodies No. 9 (csm-9) —Chingelezi
(Zapitirizidwa pa tsa. 8, danga 3 )
Zilengezo(Zachokera pa tsa. 2 )