Bukitsani Dzina la Yehova ndi Zochita Zake
1 “Yamikani Yehova, itanirani pa dzina lake; bukitsani mwa mitundu ya anthu zochita Iye. . . . Mitima yawo ya iwo ofunsira Yehova ikondwere.” (Sal. 105:1, 3) Wamasalmo amene analemba mawuŵa ankasangalala zedi kuuza ena za Yehova ndi “zochita” zake. Zochita zake ziti? Mosakayikira zokhudza ufumu waulemerero wa Mulungu ndi uthenga wabwino wa “chipulumutso chake.”—Sal. 96:2, 3; 145:11, 12.
2 Pamene tikuyandikira nyengo ya Chikumbutso cha 2001, tikufunika kukondwera n’zimene Yehova watichitira. Chifukwa chiyani? Mosakayikira, Chakudya Chamadzulo cha Ambuye ndi mwambo wapachaka waukulu kwambiri kwa Akristu onse oona. Palibe mwambo wonga umenewu tikanena za kufunika kwake, cholinga chake, kapena zimene umakwaniritsa. Imeneyi ndi nthaŵi yoti tonsefe tikumbukire zimene Yehova ndi Yesu anachita pokonza njira ya chipulumutso chathu. N’chifukwa chake kaŵirikaŵiri nyengo ya Chikumbutso timayembekezera kuchita zochuluka mu utumiki wakumunda, pobukitsa uthenga wabwino wa “chipulumutso”!
3 Kodi Mudzachita Upainiya Wothandiza? April wachaka chatha chiŵerengero chachikulu cha anthu 3,076 analembetsa upainiya wothandiza. Chaka chino kodi tingapatule miyezi ya March ndi April kukhala miyezi yapadera yochita zochuluka mu utumiki? Mwezi wa March uli ndi masiku a Loŵeruka asanu, ndipo April uli ndi masiku a Lamlungu asanu. Mwa kukonzekera kudzakhala mu utumiki maola onse pamapeto a mlungu, ofalitsa ambiri amene amagwira ntchito masiku onse a m’kati mwa mlungu aona kuti akhoza kuchita upainiya wothandiza. Kuti akwanitse maola 50 ofunika pamwezi, mpainiya wothandiza afunika avareji ya maola 12 pamlungu. Pendani bwinobwino zitsanzo za ndandanda m’bokosi la patsamba 4. Kodi pali imene ingayenerane ndi mikhalidwe yanu? Ngati palibe, mukhoza kupanga ndandanda yanu yokuyenerani kuti muchite upainiya wothandiza mu miyezi ya March ndi April.
4 Akulu ayenera kuyamba pakalipano kudzutsa chidwi ndi kulimbikitsa ofalitsa kudzachita zochuluka mu utumiki. Chaka chatha mpingo wina umene akulu ndi atumiki otumikira onse analembetsa upainiya wothandiza, ofalitsa 64 mwa 121 anachita upainiya mu April! Mpingo unasangalalanso kuti ofalitsa osabatizidwa sikisi anayamba kupereka malipoti mu March ndi April. Inde, ndi nthaŵi yabwino kwa ana ndi atsopano kufunsa akulu ngati akuyenerera kuyamba ntchito yochitira umboni poyera.
5 Khama Limadzetsa Madalitso: Mipingo imene imakhala n’zolinga zapadera ndiponso yakhama imapeza madalitso ambiri. Mipingo ina ingasamalire kwambiri kufola magawo amene safoledwafoledwa, njira zina zochitira umboni, kapena kuchitira umboni wa patelefoni yomwe ndi njira yabwino kwambiri kulankhulana ndi anthu osapezeka panyumba ndi a m’madera ovuta kufikako.
6 Kodi matenda kapena ukalamba ziyenera kulepheretsa munthu kuchita utumiki mokwanira? Osati nthaŵi zonse. Mwachitsanzo, mlongo wachikulire wazaka 86 amene ali ndi matenda a kansa anachita upainiya wothandiza mu April ngakhale kuti miyendo yake ndi yotupa. Umboni wa patelefoni unam’thandiza kuchita utumiki mokwanira, kuwonjezera kutamanda kwake Yehova. Izi zinam’limbikitsa ndiponso zinalimbikitsa mpingo.
7 Konzekerani Bwino Chikumbutso: Chaka chino Chikumbutso chili pa April 8. Popeza ndi Lamlungu, n’zotheka kudzakhalapo ambiri. Tikhoza kudzakhala ndi chiŵerengero chachikulu kuposa kale lonse ngati tichita mbali yathu (1) ifeyo kupezekapo (2) kuitanira ena kudzakhala nafe pa Chikumbutso. Kodi tidzaitane ndani?
8 Onani pamene mumalembapo zautumiki wakumunda mayina a anthu amene anasangalala ndi choonadi, ngakhale kuti simuwayenderayendera. Kutatsala milungu iŵiri kapena itatu kuti Chikumbutso chichitike, ayendereni anthu onseŵa kukawapatsa mapepala oitanira anthu ku Chikumbutso. Ngati mungathe, athandizeni zoyendera amene akufuna kukapezekapo.
9 M’mipingo ina, mapepala oitanira anthu ku Chikumbutso amatsala. Alembi a mipingo aonetsetse kuti apereka mapepalaŵa nthaŵi ilipo yambiri kuti mapepala onse awagaŵire. Mungataipe kapena kulemba bwinobwino nthaŵi ndi malo a Chikumbutso m’munsi mwa kapepalako. Kapena mungaperekenso mapepala oitanira anthu osonyeza adiresi ya Nyumba ya Ufumu ngati n’komwe mukachitire Chikumbutso. Mongokumbutsana, kaŵirikaŵiri perekani pamanja mapepala oitanira anthu ku Chikumbutso kwa eninyumba.
10 Kumbukirani Ozirala: Zimakhala zosangalatsa wophunzira Baibulo akadzipatulira kwa Yehova ndi kusonyeza zimenezi mwa kumizidwa m’madzi. Komabe, chaka chilichonse, ena mwa ife amasiya kusonkhana nafe, ndiponso amaleka kuuza ena dzina la Yehova ndi zochita zake. Tiyenera kuwadera nkhaŵa. Ngakhale kuti ambiri ozirala sanasiye choonadi, akhoza kukhala kuti analeka kulalikira chifukwa chokhumudwa, mavuto awo, kapena nkhaŵa zina za moyo. (Mat. 13:20-22) Amene afooka mwauzimu akufunika kuwathandiza kuti abwerere mu mpingo dongosolo la Satana lisanawameze. (1 Pet. 5:8) Nyengo ya Chikumbutso ino tiyesetse kuthandiza oyeneretsedwa onse ozirala kuyambiranso kulalikira uthenga wabwino.
11 Mlembi wa mpingo adziŵitse ochititsa maphunziro a buku za aliyense wozirala m’magulu awo. Komiti ya Utumiki ya Mpingo idzalinganiza maulendo aubusa kwa onse ozirala. Ngati aona kuti munthuyo akufunika phunziro la Baibulo, woyang’anira utumiki adzalinganiza thandizo lofunikiralo atakambirana ndi anzake a m’komiti ya utumiki za yemwe akuyenera kwambiri kukachititsa phunzirolo. Ngakhale kuti phunzirolo siliyenera kuchitika kwanthaŵi yaitali, wochititsayo angachitire lipoti maola, ulendo wobwereza ndi phunziro la Baibulo.
12 Chaka chatha mu April, mlongo wina mu ulaliki wa kunyumba ndi nyumba anagaŵira magazini pamsewu kwa mnyamata wina. Mnyamatayo anati mkazi wake ndi Mboni yozirala. Ndipo anafunsa komwe kunali Nyumba ya Ufumu napempha mlongoyo kuti adzaliyendere banjali kwawo. Banja lija linapezeka pamsonkhano wotsatira ndipo linavomera kuphunzira Baibulo.
13 Konzekerani Kudzachita Zochuluka! Wamasalmo yemwe anati tiyenera kubukitsa dzina la Yehova ndi zochita zake anatinso: “Myimbireni, myimbireni zom’lemekeza; fotokozerani zodabwiza zake zonse. Mudzitamandire ndi dzina lake loyera.” (Sal. 105:2, 3) Tiyeni tisonyeze kukonda kwathu dzina lalikulu la Yehova ndi ntchito zake ‘zodabwitsa’ mwa kuchita zochuluka mu utumiki, kuti nyengo ya Chikumbutso ino ikhale yopambana nyengo zina zonse!
[Bokosi patsamba 4]
Njira Zosiyanasiyana Zopezera Maola 12 pa Mlungu Pochita Upainiya Wothandiza
Tsiku Maola
Lolemba 1 2 − −
Lachiŵiri 1 − 3 −
Lachitatu 1 2 − 5
Lachinayi 1 − 3 −
Lachisanu 1 2 − −
Loŵeruka 5 4 3 5
Lamlungu 2 2 3 2
Onse Pamodzi: 12 12 12 12
Kodi apa pali ndandanda yokuyenerani? Ngati palibe, bwanji osapanga ndandanda yanu?