Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 2/01 tsamba 5-6
  • Kuthandiza Ena pa Phunziro la Buku la Mpingo

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kuthandiza Ena pa Phunziro la Buku la Mpingo
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—2001
Utumiki Wathu wa Ufumu—2001
km 2/01 tsamba 5-6

Kuthandiza Ena pa Phunziro la Buku la Mpingo

1 Polambira Yehova Akristu oyambirira ankakumana m’nyumba. (Aroma 16:3, 5; Filem. 1, 2) Lerolinonso, Maphunziro ambiri a Buku a Mpingo amachitikira m’nyumba za abale ndipo Yehova akudalitsabe makonzedwe ameneŵa. Kodi msonkhano umenewu mumauona bwanji? Kodi mukupindula nawo mokwanira, kapena mumauona kuti siwofunika monga misonkhano ina? Kuchepa kwa opezeka pa msonkhano umenewu m’mipingo ina kumasonyeza kuti ena amaganiza choncho. Nanga inuyo?

2 Onani mapindu ena ali m’munsiŵa amene tonse tingapeze pa phunziro la buku: (1) magulu ake amakhala a anthu ochepa, zimene zimathandiza kudziŵana bwino. (2) N’kosavuta anthu onse kuyankha momasuka popeza ndime zophunziridwa sizikhala zambiri ndipo pamakhala anthu ochepa; komanso, timapeza mayankho a zimene sitinamvetse pamene timachita phunziro laumwini. (3) Amakhala malo abwino apakati okonzekera utumiki wakumunda komwe amachita zimenezi m’kati mwa mlungu. (4) Ochititsa phunziro amakudziŵani bwino ndipo ndiwo angakuthandizeni mavuto anu, kukuphunzitsani utumiki wakumunda ndiponso kukuthandizani mafunso a m’Malemba.

3 Pa Phunziro la Buku la Mpingo, akulu angasamalire kwambiri kupita patsogolo mwauzimu kwa aliyense—zimene zingakhale zovuta pamisonkhano ikuluikulu. Wochititsa phunziro amayesetsa kudziŵana bwino ndi anthu a m’gulu lake, makamaka kuwaŵeta ndiponso kusamalira zosoŵa zawo zauzimu. (Miy. 27:23) Amayesetsa kugwira nawo ntchito mu utumiki wakumunda ndipo nthaŵi zina amawayendera m’makomo mwawo.

4 Nthaŵi zambiri phunziro limachitikira kufupi ndi kumene kumakhala anthu amene amapita kuphunziro limenelo. N’chifukwa chake kaŵirikaŵiri amakhala malo apakati okonzekera utumiki wakumunda. Kumene sizingatheke kuti malo a phunziro la buku akhalenso osonkhanira pokonzekera utumiki wakumunda, wochititsayo adzatsimikizira kuti walinganiza nthaŵi ndi malo ena abwino kumene gulu lake lizikakumana kaamba ka utumiki mlungu uliwonse. Izi zimam’patsa wochititsa phunziro mpata woyenda ndi anthu osiyanasiyana a m’gulu lake, choncho amapeza mwayi woona mmene iwo amachitira akafika pakhomo la munthu.

5 Sonyezani Chidwi: Kodi paphunziro lanu la buku mumaona kuti pali mzimu wonga wa banja? Onse akasonyeza chidwi mwa ena m’gululo zimathandiza kukondana. (Agal. 6:10) Mwachitsanzo, kodi mumadziŵa ngati ena sanabwere pamsonkhano ndiyeno n’kuwauza kuti munawasoŵa? Ngati wina m’banja palibe panthaŵi ya chakudya ndithudi ena m’banjamo amadziŵa. Ndipo onse amada nkhaŵa. Mkhalidwe umenewu paphunziro la buku umayanjanitsa abale ndipo umawalimbikitsa kusaphonya “chakudya.” Mukachita chidwi ndi aliyense m’gululo mudzathandiza kukulitsa mzimu wa “banja” umenewu.

6 Kodi pali njira zina zimene mungasonyezere chidwi mwa ena? China chimene mungachite ndicho kuyesetsa kulankhula ndi ena pamisonkhano, osati kungowapatsa moni yekha. Ena ndi amanyazi koma amafuna wolankhula naye ndipo amalankhula ngati wina wayamba kuwalankhula. Pali zambiri zimene tingachite. Wochititsa phunziro lanu la buku angakhale ndi njira zina. Bwanji osam’funsa?

7 Kodi mungatani ngati wina m’gulu lanu la phunziro la buku akuoneka kuti akuzilala kapena kuti ali ndi vuto? Uphungu wakuti “limbikitsani amantha mtima” udzakhala woyenera kwabasi. (1 Ates. 5:14) Ngati wina akudwala, zimam’limbikitsa anzake akapita kukamuona ndi kum’thandiza! Nthaŵi zambiri zimene zimafunika n’kungodziŵa kuti ena akudziŵa ndiponso akudera nkhaŵa. Makamaka, wochititsa phunziro la buku monga kholo ayenera kukhala tcheru kuona zizindikiro za kuzilala ndipo ayenera kupereka thandizo loyenera.

8 Kodi ndi Motani Mmene Mungathandizire?: Pali njira zina zimene mungathandizire phunziro la buku. Njira ina ndiyo chitsanzo chanu chabwino. Mwachitsanzo, kuvala mmene mungavalire popita ku misonkhano ku Nyumba ya Ufumu mumasonyeza ulemu. Mumapereka chitsanzo chabwino kwa awo amene ali ndi chizoloŵezi chovala motayirira. Kodi n’chizoloŵezi chanu kufika nthaŵi yabwino kuti musadodometse msonkhanowo?

9 N’zodziŵikiratu kuti phunziro limakhala losangalatsa ngati onse akonzekera bwino, mwina kudula mizera kunsi kwa mayankho ndi kumayankha m’mawu awoawo. Kuŵerengeratu malemba amene sanagwidwe mawu ndiyeno ndi kuwagwiritsa ntchito poyankha kungathandize kwambiri msonkhanowo. Enanso amapeza nthaŵi yofufuza nkhani yogwirizana ndi mfundo zofunika ndi kukakamba zimenezi paphunziro. Izi n’zabwino kwambiri. Zinthu zonsezi zimathandiza Phunziro la Buku la Mpingo kukhala losangalatsa ndi lolimbikitsa mwauzimu kwa onse opezekapo.

10 Amene amapezeka nthaŵi zonse pa phunziro la buku amakhulupirira kuti Yehova amalidalitsa. Ndi malo amene munthu angathandizidwe ndiponso angathandize ena kulimba mwauzimu. Ngati simupezeka pamsonkhanowu nthaŵi zonse, bwanji osasintha ndandanda yanu kuti muzisangalala ndi msonkhano wabwino umenewu womwe Yehova ndi gulu lake wakukonzerani?

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena