Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 3/10 tsamba 8
  • Zilengezo

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Zilengezo
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—2010
Utumiki Wathu wa Ufumu—2010
km 3/10 tsamba 8

Zilengezo

◼ Mabuku ogawira mu March: Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni? Ofalitsa ayesetse kuyambitsa phunziro la Baibulo kwa munthu aliyense amene am’gawira bukuli kapena aliyense amene ali nalo kale. April ndi May: Magazini a Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! Mukamapanga maulendo obwereza kwa anthu achidwi, kuphatikizapo anthu amene anapezeka pa Chikumbutso kapena misonkhano ina koma sasonkhana nthawi zonse pamisonkhano ya mpingo, muyesetse kugawira buku la Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni? n’cholinga choyambitsa phunziro la Baibulo. June: Gawirani buku la Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni?

◼ Magazini atsopano a Galamukani! ndiponso Nsanja ya Olonda akangofika, muziwagawa kwa ofalitsa kuti awawerengeretu asanakagawire mu utumiki. Zingakhale bwino kuti ofalitsa asamagawire magaziniwa, koma azidikira kuti mwezi wake ufike kaye.

◼ Mwambo wa Chikumbutso udzachitika pa March 30, 2010. Ndipo nyimbo zimene tidzaimbe pa mwambowu ndi nambala 8 ndi 5 kuchokera m’buku lanyimbo latsopano. Ngati mpingo wanu umasonkhana Lachiwiri, yesetsani kuti mudzasonkhane tsiku lina mkati mwa mlunguwo. Koma ngati m’Nyumba ya Ufumuyo mumasonkhana mipingo yambiri ndipo n’zosatheka kupeza tsiku lina loti muchite misonkhanoyo, ndiye kuti misonkhano iyenera kulephereka. Koma nkhani zina za mu Msonkhano wa Utumiki, zomwe zikukhudza kwambiri mpingo wanu, mungaziphatikize mumsonkhano wina wa Utumiki.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena