Zochitika mu Utumiki Wakumunda
Chaka chatha, Chikumbutso chinachitika m’mwezi wa March ndipo m’mwezi umenewo, abale ndi alongo 2, 992 anachita upainiya wothandiza. Chikumbutso cha chaka chino cha 2011 chichitika m’mwezi wa April. M’mwezi umenewu wokha, tili ndi mwayi wochita upainiya wothandiza wa maola 30. Choncho tikuyembekezera kuti abale ndi alongo ambiri aganizira mmene zinthu zilili pa moyo wawo ndipo achita zochuluka mu utumiki wakumunda pochita upainiya wothandiza m’mwezi wa April.