Ndandanda ya Mlungu wa May 9
MLUNGU WOYAMBIRA MAY 9
Nyimbo Na. 48 ndi Pemphero
□ Phunziro la Baibulo la Mpingo:
cf mutu 6, ndime 19-25 ndi bokosi patsamba 65 (Mph. 25)
□ Sukulu ya Utumiki wa Mulungu:
Kuwerenga Baibulo: Masalimo 1-10 (Mph. 10)
Na. 1: Salimo 7:1-17 (Osapitirira mph. 4)
Na. 2: Ngati Wina Anena Kuti: “Ndinavomereza Yesu Kukhala Mpulumutsi Wanga”—rs tsa. 434 ndime 2 (Mph. 5)
Na. 3: N’chifukwa Chiyani Yesu Anakana Kutchulidwa Kuti “Mphunzitsi Wabwino”?—Maliko 10:17, 18 (Mph. 5)
□ Msonkhano wa Utumiki:
Mph 5: Zilengezo.
Mph 10: Tiyenera Kumvera Mulungu Monga Wolamulira, Osati Anthu. (Mac. 5:29) Nkhani yokambirana yochokera mu Nsanja ya Olonda ya July 15, 2006 tsamba 8 ndi 9. Pemphani omvera kuti afotokoze madalitso amene apeza chifukwa cha kupirira mayesero.
Mph 10: Kodi Mungachite Upainiya Wothandiza M’miyezi Ikubwerayi? Nkhani yokambirana. Kambiranani mwachidule ziyeneretso za upainiya wothandiza zimene zili m’buku la Gulu, tsamba 112 mpaka 113. Pemphani amene anachitapo upainiya wothandiza pa nthawi ya holide ku sukulu kapena ku ntchito, kuti afotokoze madalitso amene anapeza.
Mph 10: “Onetsani Kuwala Kwanu.” Mafunso ndi mayankho. Pemphani omvera kuti afotokoze mmene khalidwe lawo labwino linathandizira kuti alalikire.
Nyimbo Na. 45 ndi Pemphero