Zitsanzo za Ulaliki
Zimene Munganene Poyambitsa Maphunziro a Baibulo Loweruka Loyambirira M’mwezi wa July
“Kodi mukuganiza kuti Mulungu amaona kuti mapemphero athu ndi ofunika kapena sakhala nawo chidwi kwenikweni?” Yembekezerani ayankhe. Kenako asonyezeni funso loyamba limene lili patsamba lomaliza la Nsanja ya Olonda ya July 1. Kambiranani ndime zimene zili pansi pa funso limeneli komanso lemba limodzi pa malemba amene ali kumapeto kwa ndimezo. Agawireni magaziniyo, ndipo konzani zoti mudzabwerenso kuti mudzakambirane funso lotsatira.
Nsanja ya Olonda July 1
“Popeza Mulungu ndi Wamphamvuyonse, kodi mukuganiza kuti ndi amene amachititsa zinthu zoipa zimene zimachitika padzikoli? [Yembekezerani ayankhe. Kenako werengani Yakobo 1:13.] Magaziniyi ikufotokoza chifukwa chake padzikoli pamachika mavuto osiyanasiyana. Ikufotokozanso zimene Mulungu adzachite kuti athetse mavuto onse padzikoli.”
Galamukani! July
“Anthufe timakumana ndi mavuto osiyanasiyana monga masoka achilengedwe, matenda aakulu kapena imfa ya munthu wa m’banja lathu. Kodi mukuganiza kuti tingatani tikakumana ndi mavuto ngati amenewa? [Yembekezerani ayankhe.] Anthu ambiri amaona kuti zoterezi zikachitika, mfundo za m’Baibulo zimawathandiza. [Werengani Aroma 15:4.] Magaziniyi ikufotokoza mmene mfundo za m’Baibulo zingatithandizire tikakumana ndi mavuto.”