Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 11/13 tsamba 4
  • Zitsanzo za Ulaliki

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Zitsanzo za Ulaliki
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—2013
  • Nkhani Yofanana
  • Zitsanzo za Ulaliki
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2012
  • Zitsanzo za Ulaliki
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2014
  • Zitsanzo za Ulaliki
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2011
  • Zitsanzo za Ulaliki
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2012
Onani Zambiri
Utumiki Wathu wa Ufumu—2013
km 11/13 tsamba 4

Zitsanzo za Ulaliki

Zimene Munganene Poyambitsa Maphunziro a Baibulo Loweruka Loyambirira M’mwezi wa December

“Anthu ambiri akudikirirabe kubweranso kwa Yesu. Ngati Yesu atabwera panopa, kodi mungafune atachita chiyani?” Yembekezani ayankhe. Musonyezeni nkhani imene ili patsamba lomaliza la Nsanja ya Olonda ya December 1, 2013, ndipo kambiranani ndime imene ili pansi pa funso loyamba komanso lemba limodzi pa malemba amene ali kumapeto kwa ndimeyo. Mugawireni magaziniyo ndipo konzani zoti mudzabwerenso kuti mudzakambirane funso lotsatira.

Nsanja ya Olonda December 1

“Masiku ano anthu amakhala otanganidwa kwambiri moti amaona kuti Mulungu si wofunikira pa moyo wawo. Kodi mukuganiza kuti Mulungu ndi wofunikira pa moyo wathu? [Yembekezani ayankhe.] Pa ulaliki wake wotchuka wapaphiri, Yesu ananena kuti Mulungu ndi wofunika kwambiri pa moyo wathu ngati tikufuna kukhala osangalala. [Werengani Mateyu 5:3.] Magaziniyi yatchula zifukwa zitatu zimene zikusonyeza kuti anthufe timafunikira Mulungu pa moyo wathu.”

Galamukani! December

“Anthu ambiri amanena zinthu zosiyanasiyana akamva kapena kuwerenga nkhani inayake m’nyuzipepala, pawailesi kapena pa TV. Kodi mukuona kuti nkhani zimene timamva kapena kuwerenga zimakhala zolondola komanso zoona? [Yembekezani ayankhe.] Baibulo limatichenjeza kuti tiyenera kukhala osamala kuti tisamangokhulupirira chilichonse chimene tamva. [Werengani Yobu 12:11.] Magaziniyi ili ndi mfundo zomwe zingatithandize kudziwa ngati zimene tikuwerenga kapena kumva zili zolondola kapena ayi.”

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena