Zitsanzo za Ulaliki
Zimene Munganene Poyambitsa Maphunziro a Baibulo Loweruka Loyambirira M’mwezi wa December
“Mwezi uno, anthu ambiri akuganizira za Yesu. Kodi inuyo mumaona kuti ndi chinthu chachikulu chiti chimene Yesu anachita? [Yembekezani ayankhe.] Taonani mutu wa nkhani iyi imene ili pa tsamba 16.” M’patseni mwininyumbayo magazini a Nsanja ya Olonda ya December 1 ndipo kambiranani nkhani imene ikupezeka pa kamutu kamodzi patsamba 16. Yesetsani kuwerenga ngakhale lemba limodzi lokha. Kenako gawirani magaziniyo ndipo mukonze zoti mudzabwerenso kudzakambirana yankho la funso lotsatira.
Nsanja ya Olonda December 1
“Anthu ambiri amaona kuti nthawi ino ndi yosangalatsa. Kodi mukuganiza kuti ndi chinthu chiti pa zinthu izi chomwe ndi chofunika kwambiri kuchita pa Khirisimasi? [Muonetseni zinthu zimene zili patsamba 3 kenako yembekezani ayankhe. Kenako pitani pa nkhani imene ili ndi mutu umene munthuyo wasankha ndipo muwerenge lemba limene lili pa mutu wa nkhaniyo.] Magazini iyi ikufotokoza zinthu zimene tingamachite nthawi zonse pokumbukira Yesu osati nthawi ya Khirisimasi yokha.”
Galamukani! December
“Masiku ano anthu ambiri amakhala ankhawa komanso opanikizika. Kodi inuyo mukuona kuti anthu akukhala osaleza mtima kwambiri masiku ano kuposa kale? [Yembekezani ayankhe.] Anthu ena amakhulupirira kuti tikukhala nthawi yovuta imene inaloseredwa palemba ili. [Werengani 2 Timoteyo 3:1.] Magazini iyi ikufotokoza chifukwa chake kusaleza mtima kuli koopsa komanso ikufotokoza zinthu zimene tingachite kuti tizikhala oleza mtima.”