Zitsanzo za Ulaliki
Zimene Munganene Poyambitsa Maphunziro a Baibulo Loweruka Loyambirira M’mwezi wa December
“Tabwera kuti tikambirane nanu mfundo zothandiza mabanja. Makolo ambiri amafuna kuti ana awo azikonda Mulungu. Ndiye kodi makolo ayenera kuphunzitsa ana awo kuti azikonda Mulungu, kapena anawo angaphunzire zimenezi paokha?” Yembekezerani ayankhe. Ndiyeno musonyezeni nkhani yomwe ili patsamba lomaliza la Nsanja ya Olonda ya December 1, ndipo kambiranani mfundo zomwe zili pa funso loyamba. Muwerenge lemba limodzi mwa malemba amene ali pamenepo. Kenako m’patseni magaziniyo ndipo mukonze zodzabweranso kuti mudzakambirane funso lotsatira.
Nsanja ya Olonda December 1
“Tikukambirana mwachidule ndi anthu nkhani yokhudza Mulungu. Anthu amakhulupirira zosiyanasiyana zokhudza Mulungu. Ena amaona kuti n’zotheka Mulungu kukhala mnzawo wapamtima pomwe ena amaona kuti n’zosatheka. Kodi inuyo mukuganiza bwanji? [Yembekezerani ayankhe.] Lemba ili likusonyeza kuti Mulungu amafuna kuti tikhale naye pa ubwenzi. [Werengani Yakobo 4:8a.] Magaziniyi ikufotokoza zinthu zitatu zomwe tingachite kuti Mulungu akhale mnzathu wapamtima.”
Galamukani! December
“Tikukambirana mwachidule ndi anthu zokhudza vuto la matenda a muubongo. Bungwe loona za umoyo padziko lonse limanena kuti matenda a muubongo monga kuvutika maganizo, amagwira munthu mmodzi pa anthu 4 alionse. Kodi inuyo mukuona kuti matendawa ndi ofaladi masiku ano? [Yembekezerani ayankhe.] Baibulo limanena kuti posachedwapa, matenda onse adzatha. [Werengani Chivumbulutso 21:3, 4.] Magaziniyi ikufotokoza mfundo zingapo zokhudza matendawa, zomwe aliyense ayenera kudziwa.”