Zitsanzo za Ulaliki
Zimene Munganene Poyambitsa Maphunziro a Baibulo Loweruka Loyambirira M’mwezi wa December
“Ndikukhulupirira kuti mungavomereze zoti munthu aliyense amafuna kukhala ndi mnzake. Kodi ndi khalidwe liti la mnzanu limene inuyo mumasangalala nalo kwambiri ? [Yembekezani ayankhe.] Taonani zimene magazini iyi ikufotokoza pa nkhani yoti tizisankha anzathu mosamala kwambiri.” Kenako m’patseni mwininyumbayo magazini ya Nsanja ya Olonda ya December 1 ndipo werengani ndi kukambirana nkhani imene ikupezeka pansi pa kamutu koyamba patsamba 16. Yesetsani kuwerenga ngakhale lemba limodzi lokha. Kenako gawirani magaziniyo ndipo mukonze zoti mudzabwerenso kudzakambirana yankho la funso lotsatira.
Nsanja ya Olonda December 1
“Kodi munayamba mwadzifunsapo kuti n’chifukwa chiyani masoka achilengedwe akhala akuchitika mobwerezabwereza masiku ano? [Yembekezani ayankhe.] N’zochititsa chidwi kuti Baibulo linaneneratu za nthawi imene kuzidzachitika kwambiri masoka achilengedwe. [Werengani Mateyu 24:7, 8.] Magazini iyi ikuyankha mafunso akuti: N’chifukwa chiyani masiku ano kukuchitika masoka achilengedwe ambiri? Kodi ndi chilango chochokera kwa Mulungu? Kodi tili ndi zifukwa zotani zokhulupirira kuti Mulungu athetsa masoka achilengedwe posachedwapa?”
Galamukani! December
Werengani 2 Timoteyo 3:16. Kenako nenani kuti: “Anthu ena amavomereza kuti Baibulo analiuzira ndi Mulungu, koma ena savomereza. Kodi inuyo mukuganiza bwanji? [Yembekezani ayankhe.] Ngakhale kuti anthu amasiyanasiyana maganizo pa nkhani imeneyi, anthu ambiri amavomereza kuti palibe buku limene lakumana ndi mavuto ambiri kuposa Baibulo. Magazini iyi ikufotokoza zimene anthu ena kwa zaka zambiri achita kuti awononge Baibulo komanso kuti anthu asakhale ndi mwayi woliwerenga. Magaziniyi ikufotokozanso zimene zinachitika kuti Baibulo lipitirize kupezeka.”