Ndandanda ya Mlungu wa July 7
MLUNGU WOYAMBIRA JULY 7
Nyimbo Na. 63 ndi Pemphero
Phunziro la Baibulo la Mpingo:
jr mutu 13 ndime 14-19 (Mph. 30)
Sukulu ya Utumiki wa Mulungu:
Kuwerenga Baibulo: Levitiko 17–20 (Mph. 10)
Na. 1: Levitiko 19:19-32 (Osapitirira mph. 4)
Na. 2: Chifukwa Chake Akhristu Odzozedwa ndi Mzimu, Kapena Kuti “Oyera Mtima,” Si Opanda Machimo—rs tsa. 334 ndime 3 (Mph. 5)
Na. 3: Zimene Baibulo Limanena pa Nkhani ya Phompho—re tsa. 287-288; rs tsa. 356-357 (Mph. 5)
Msonkhano wa Utumiki:
Mph. 10: Zimene Munganene Pogawira Magazini a July. Nkhani yokambirana. Yambani ndi kuchita chitsanzo cha mmene tingagawirire magaziniwo pogwiritsa ntchito zitsanzo za ulaliki zimene zili patsamba lino. Kenako kambiranani chitsanzo cha ulaliki chilichonse kuyambira poyambirira mpaka pamapeto. Pomaliza, limbikitsani ofalitsa onse kuti ayenera kuwerenga magaziniwo n’cholinga choti awadziwe bwino komanso alimbikitseni kuti adzagawire nawo magaziniwa.
Mph. 10: Zosowa za pampingo.
Mph. 10: Kodi Tinachita Zotani? Nkhani yokambirana ndipo ikambidwe ndi mlembi. Fotokozani zimene mpingo unachita pa nthawi ya Chikumbutso ndipo yamikirani mpingowo chifukwa chogwira ntchito mwakhama. Pemphani omvera kuti afotokoze zinthu zosangalatsa zimene anakumana nazo pamene ankagawira timapepala toitanira anthu ku Chikumbutso, kapena pamene ankachita upainiya wothandiza.
Nyimbo Na. 123 ndi Pemphero