Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 6/14 tsamba 7
  • Kubwereza za M’Sukulu ya Utumiki wa Mulungu

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kubwereza za M’Sukulu ya Utumiki wa Mulungu
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—2014
Utumiki Wathu wa Ufumu—2014
km 6/14 tsamba 7

Kubwereza za M’Sukulu ya Utumiki wa Mulungu

Mafunso otsatirawa tidzawakambirana pa Sukulu ya Utumiki wa Mulungu, ya mlungu woyambira June 30, 2014.

  1. N’chifukwa chiyani tinganene kuti mfundo ya pa Ekisodo 23:2 ndi yothandiza kwambiri posankha zosangalatsa? [May 5, w11 7/15 tsa. 10-11 ndime 3-7]

  2. N’chifukwa chiyani tinganene kuti kusatsatira lamulo loti ansembe azisamba m’manja ndi mapazi asanapereke nsembe kunali koopsa? Nanga ifeyo tikuphunzirapo chiyani pa nkhani imeneyi? (Eks. 30:18-21) [May 19, w96 7/1 tsa. 9 ndime 9]

  3. N’chifukwa chiyani Aroni sanalangidwe atapanga fano la mwana wa ng’ombe? (Eks. 32:1-8, 25-35) [May 19, w04 3/15 tsa. 27 ndime 4]

  4. Kodi mfundo yakuti Yehova analetsa Aisiraeli kukwatirana ndi anthu a mitundu ina ingathandize bwanji Mkhristu amene akufuna kukhala pa chibwenzi kapena kulowa m’banja? (Eks. 34:12-16) [May 26, w89 11/1 tsa. 20-21 ndime 11-13]

  5. Kodi nkhani ya Bezaleli ndi Oholiabu ingatilimbikitse bwanji? (Eks. 35:30-35) [May 26, w10 9/15 tsa. 10 ndime 13]

  6. Kodi “chizindikiro chopatulika cha kudzipereka” chimene mkulu wa ansembe ankavala chinkamukumbutsa chiyani? Nanga ife tikuphunzirapo chiyani pa nkhani ya kudzipereka? (Eks. 39:30) [June 2, w01 2/1 tsa. 14 ndime 2-3]

  7. Kodi Mkhristu aliyense ayenera kuchita chiyani akadziwa kuti Mkhristu wina wachita tchimo lalikulu? (Lev. 5:1) [June 9, w97 8/15 tsa. 27]

  8. Kodi nsembe zachiyanjano zimene Aisiraeli ankapereka zinali zofunika bwanji? Nanga ife tikuphunzirapo chiyani? (Lev. 7:31-33) [June 16, w12 1/15 tsa. 19 ndime 11-12]

  9. Kodi Nadabu ndi Abihu, omwe anali ana a Aroni, analakwa chiyani, nanga ife tikuphunzirapo chiyani? (Lev. 10:1, 2, 9) [June 23, w04 5/15 tsa. 22 ndime 7-9]

  10. N’chifukwa chiyani mkazi ankakhala “wodetsedwa” akabereka mwana? (Lev. 12:2, 5) [June 23, w04 5/15 tsa. 23 ndime 2]

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena