Zitsanzo za Ulaliki
Zimene Munganene Poyambitsa Maphunziro a Baibulo Loweruka Loyambirira M’mwezi wa August
“Nthawi zambiri masiku ano, anthu amajambula zithunzi za Yesu ngati mmene analili zaka 2,000 zapitazo. Anthuwa amamujambula ali mwana wa khanda modyera ziweto kapena ali munthu wamkulu atakhomedwa pamtengo wozunzikirapo. Kodi mukuganiza kuti Yesu akuchita chiyani panopa? [Yembekezani ayankhe.] Taonani zimene magazini iyi ikunena.” M’patseni mwininyumbayo magazini ya Nsanja ya Olonda ya August 1 ndipo kambiranani nkhani imene ikupezeka pansi pa kamutu koyamba patsamba 16. Yesetsani kuwerenga ngakhale lemba limodzi. Kenako gawirani magaziniyo ndipo mukonze zoti mudzabwerenso kudzakambirana yankho la funso lotsatira.
Nsanja ya Olonda August 1
“Anthu ambiri amakhulupirira kuti zozizwitsa zimachitika koma ena amakayikira. Kodi mukuganiza kuti zozizwitsa zimachitikadi? [Yembekezani ayankhe.] Lonjezo la m’Baibulo lopezeka palemba ili lonena za zozizwitsa zimene zidzachitike m’tsogolo, lathandiza anthu ambiri kukhala ndi chiyembekezo. [Werengani lemba limodzi pa malemba amene ali patsamba 9 ndi 10.] Magazini iyi ikuyankha mafunso atatu akuluakulu okhudza zozizwitsa, amene anthu ambiri amakhala nawo.”
Galamukani! August
“Masiku ano anthu amaopa kuyenda okha kukada. Kodi mukuganiza kuti pali chilichonse chimene chingachitike kuti zachiwawa zichepe m’dzikoli? [Yembekezani ayankhe.] Magaziniyi ikufotokoza zinthu zina zimene aliyense angachite kuti azikhala mwamtendere ndi anthu ena. Ikufotokozanso mmene ulosi wolimbikitsawu udzakwaniritsidwire.” Werengani Salimo 72:7.