Zochitika mu Utumiki Wakumunda
Tikuyamikira abale ndi alongo amene akuchita upainiya wapadera mwakhama kwambiri kuti apititse patsogolo ntchito yotuta m’gawo la nthambi yathu. Mwachitsanzo, kwa nthawi yaitali, mpingo wa Chitimba umene uli kumpoto kwa dziko la Malawi lino wakhala uli ndi ofalitsa asanu okha. Koma chifukwa chothandizidwa ndi apainiya apadera, tsopano mu mpingowu muli ofalitsa 27. Chimenechi ndi chitsanzo chabwino kwambiri kwa tonsefe cha kudzipereka kwa abale ndi alongo amene akuchita upainiya wapadera.