Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Baibulo
    Kukambitsirana za m’Malemba
    • ndi deti la kuchiyambiyambi kwa zaka za zana lachiŵiri C.E. Palinso makope ochuluka a matembenuzidwe oyambirira a zinenero zina.

      M’mawu oyamba a mavoliyamu ake asanu ndi aŵiri The Chester Beatty Biblical Papyri, Bwana Frederic Kenyon analemba kuti: “Chosankha choyamba ndi chofunika koposa chopezedwa m’kupendedwa kwake [gumbwa] chiri chokhutiritsa kotero kuti kumatsimikizira kusalakwa kwamalemba amene alipo. Palibe kusiyana kwakukulu kapena kodetsa nkhaŵa kumene kumasonyezedwa kaya m’Chipangano Chakale kapena Chatsopano. Mulibe mawu osiyidwa kapena owonjezeredwa odetsa nkhaŵa kwambiri, ndipo mulibe kusiyana kumene kumayambukira maumboni ofunika kapena ziphunzitso. Kusiyana kwa lemba kumayambukira nkhani zazing’ono monga ngati za mawu kapena mawu enieni ogwiritsiridwa ntchito . . . Koma chofunika chawo chachikulu ndicho kutsimikiza kwake, mwaumboni wakale koposa wopezeka panthaŵiyo, kukhulupirika kwa malembo athu amene alipo.”—(London, 1933), p. 15.

      Nzowona kuti matembenuzidwe ena a Baibulo amamamatira kwambiri ku zimene ziri m’zinenero zoyambirira koposa ena. Ochitira ndemanga amakono a Baibulo achita mopambanitsa kotero kuti nthaŵi zina amasintha tanthauzo la poyamba. Otembenuza ena alola zikhulupiriro zawo kuipitsa matembenuzidwe awo. Koma zofooka zimenezi zingathe kudziŵika mwa kuyerekezeredwa kwa matembenuzidwe osiyanasiyana.

      Ngati Wina Anena Kuti—

      ‘Sindimakhulupirira Baibulo’

      Mungayankhe Kuti: ‘Koma mumakhulupirira kuti Mulungu aliko, kodi sichoncho? . . . Kodi ndingafunse kuti nchiyani m’Baibulo chimene mumachiwona kukhala chovuta kuchivomereza?’

      Kapena munganene kuti: ‘Ndingafunse kuti, Kodi inu nthaŵi zonse mwalingalira motero? . . . Ndamva ena akunena zimenezo, ngakhale kuli kwakuti sanaphunzire Baibulo mosamalitsa. Koma popeza kuti Baibulo momvekera bwino limanena kuti liri uthenga wochokera kwa Mulungu mwiniyo ndi kuti akutilonjeza moyo wamuyaya ngati tikhulupirira ndi kukhala ndi moyo mogwirizana ndi zimene limanena, kodi simukuvomereza kuti kukakhala koyenerera kwambiri kulipenda kuti tidziŵe kuti kaya zimene limanena nzowona kapena ayi? (Gwiritsirani ntchito mawu a patsamba 54-57.)’

      ‘Baibulo limadzitsutsa’

      Mungayakhe kuti: ‘Pali anthu ena amene anandiuza zimenezo, koma palibe ndi mmodzi yemwe amene anayamba wandisonyeza chimene chiri kudzitsutsa kumeneko. Ndipo m’kuŵerenga Baibulo kwa ine mwini sindinapeze nkumodzi komwe. Kodi mungandipatse chitsanzo?’ Ndiyeno mwinamwake mungawonjezere kuti: ‘Zimene ndapeza nzakuti anthu ambiri sanapeze chabe mayankho a mafunso amene Baibulo linawachititsa kuwasinkhasinkha. Mwachitsanzo, kodi Kaini anapeza kuti mkazi wake? (Gwiritsirani ntchito mawu a patsamba 235.)’

      ‘Anthu analemba Baibulo’

      Mungayankhe kuti: ‘Nzowona. Pafupifupi 40 a iwo anakuchita. Koma linauziridwa ndi Mulungu.’ Ndiyeno mwinamwake wonjezerani kuti: (1) ‘Kodi zimenezo zitanthauzanji? Kuti Mulungu anatsogoza kulembedwako, mofanana ndi mmene mwini bizinesi amagwiritsirira ntchito mlembi kumlembera makalata.’ (2) ‘Lingaliro la kulandira mauthenga ochokera kwa munthu wa kutali m’mlengalenga siliyenera kutidabwitsa. Ngakhale anthu atumiza mauthenga ndi zithunzi kuchokera pamwezi. Kodi anakuchita motani? Mogwiritsira ntchito malamulo amene anayambitsidwa kalekale ndi Mulungu mwiniyo.’ (3) ‘Koma kodi ndimotani mmene tingakhalire otsimikizira kuti zimene ziri m’Baibulo nzochokeradi kwa Mulungu? Liri ndi chidziŵitso chimene sichikanachokera kumagwero aumunthu. Cha mtundu wanji? Malongosoledwe amtsogolo; ndipo amenewa nthaŵi zonse atsimikizira kukhala olondola kotheratu. (Mwachitsanzo, wonani tsamba 54-56, ndiponso tsamba 261-266, pamutu wakuti “Masiku Otsiriza.”)’

      ‘Aliyense ali ndi matanthauziridwe ake ake a Baibulo’

      Mungayankhe kuti: ‘Ndipo mwachiwonekere sionse amene ali olondola.’ Pamenepo mwinamwake mungawonjezere kuti: (1) ‘Kupotoza Malemba kuti ayenerane ndi maganizo athu kungachititse chivulazo chosatha. (2 Pet. 3:15, 16)’ (2) ‘Zinthu ziŵiri zingathe kutithandiza kumvetsetsa Baibulo molondola. Choyamba, pendani mawu apatsogolo ndi apambuyo (mavesi ozungulira) a mawu alionse. Kenako, yerekezerani malembawo ndi mawu ena m’Baibulo amene amanena za nkhani imodzimodziyo. Mwanjira imeneyo timalola Mawu a Mulungu mwiniyo kutsogoza kuganiza kwathu, ndipo kutanthauzira sikwathu koma kwake. Ndimo mmene mabukhu a Watch Tower amachitira.’ (Wonani tsamba 276, pamutu wakuti “Mboni za Yehova.”)

      ‘Siliri lopindulitsa m’tsiku lathu’

      Mungayankhe kuti: ‘Timakondwera ndi zinthu zopindulitsa kaamba ka tsiku lathu, kodi sichoncho?’ Ndiye mwinamwake wonjezerani kuti: (1) ‘Kodi mungavomereze kuti kuthetsa nkhondo kukakhala kopindulitsa? . . . Kodi simukuvomereza kuti ngati anthu ataphunzira kukhalira pamodzi mu mtendere ndi a mitundu ina, kumeneku kukakhala chiyambi chabwino? . . . Baibulo linaneneratu zimenezo kumene. (Yes. 2:2, 3) Monga chotulukapo cha kuphunzira Baibulo, zimenezi zikuchitika lerolino pakati pa Mboni za Yehova.’ (2) ‘Kanthu kenanso kakufunika—kuchotsedwa kwa anthu onse ndi mitundu imene imachititsa nkhondo. Kodi chinthu choterocho chidzachitikadi? Inde, Baibulo limalongosola mmene zidzachitikira. (Dan. 2:44; Sal. 37:10, 11)’

      Kapena munganene kuti: ‘Ndikuyamikira nkhaŵa yanu. Ngati bukhu lamalangizo linali losapindulitsa, tikakhala opusa kuligwiritsira ntchito, kodi sichoncho?’ Ndiyeno mwinamwake wonjezerani kuti: ‘Kodi mungavomereze kuti bukhu lopereka uphungu wabwino umene ungatikhozetse kukhala ndi moyo wabanja wachimwemwe nlopindulitsa? . . . Nthanthi ndi zizoloŵezi zonena za moyo wabanja zasintha nthaŵi zambiri, ndipo zotulukapo zimene timawona lerolino siziri zabwino. Koma awo amene amadziŵa ndi kugwiritsira ntchito zimene Baibulo limanena ali ndi mabanja okhazikika, achimwemwe. (Akol. 3:12-14, 18-21)’

      ‘Baibulo ndibukhu labwino, koma kulibe chinthu chonga chakuti chowonadi chenicheni’

      Mungayankhe kuti: ‘Nzowona kuti munthu aliyense akuwonekera kukhala ndi lingaliro losiyana. Ndipo ngakhale ngati munthu aganiza kuti walinganiza chinthu chake, kaŵirikaŵiri amapeza kuti pali chinthu chimodzi chimene sanalingalire. Koma pali munthu wina amene alibe kupereŵera kotero. Kodi ameneyo angakhale yani? . . . Inde, Mlengi wachilengedwe chonse.’ Pamenepo mwinamwake wonjezerani kuti: (1) ‘Ndicho chifukwa chake Yesu Kristu anati kwa iye: “Mawu anu ndichowonadi.” (Yoh. 17:17) Chowonadi chimenecho chiri m’Baibulo. (2 Tim. 3:16, 17)’ (2) ‘Mulungu samafuna kuti tipwayirepwayire mosadziŵa; iye wanena kuti chifuniro chake kwa ife nchakuti tifike pa chidziŵitso cholongosoka cha chowonadi. (1 Tim. 2:3, 4) Mwanjira yokhutiritsa kwambiri Baibulo limayankha funso longa lakuti . . . ’ (Kuthandiza anthu ena, inu choyamba mungafunikire kukambitsirana umboni wa kukhulupirira kukhalapo kwa Mulungu. Wonani tsamba 306-313, pamutu wakuti “Mulungu.”)

      ‘Baibulo ndibukhu la azungu’

      Mungayankhe kuti: ‘Nzowonadi kuti iwo asindikiza makope ambiri a Baibulo. Koma Baibulo silimanena kuti fuko lina ndilabwino kwambiri koposa lina.’ Ndiyeno mwinamwake wonjezerani kuti: (1) ‘Baibulo nlochokera kwa Mlengi wathu, ndipo iye ngwopanda tsankho. (Mac. 10:34, 35)’ (2) ‘Mawu a Mulungu amalonjeza mwaŵi wa kukhala ndi moyo kosatha pansi pano pansi pa Ufumu wake kwa anthu amitundu yonse ndi mafuko. (Chiv. 7:9, 10, 17)’

      Kapena munganene kuti: ‘Kutalitali! Mlengi wa anthu ndiye amene anasankha amuna amene akawauzira kulemba mabukhu 66 a Baibulo. Ndipo ngati anasankha kugwiritsira ntchito anthu akhungu loyera, limenelo linali thayo lake. Koma uthenga wa Baibulo sunali wa anthu oyera okha.’ Ndiyeno mwinamwake wonjezerani kuti: (1) ‘Wonani chimene Yesu ananena . . . (Yoh. 3:16) “Yense” amaphatikizapo anthu a khungu lamawonekedwe ali onse. Ndiponso, asanakwere kumwamba, Yesu ananena mawu otsazikira awa kwa ophunzira ake . . . (Mat. 28:19)’ (2) ‘Mokondweretsa, Machitidwe 13:1 amanena za munthu wina wotchedwa Nigeri, dzina limene limatanthauza kuti “wakuda.” Iye anali mmodzi wa aneneri ndi aphunzitsi ampingo wa Antiokeya, Siriya.’

      ‘Ndimakhulupirira kokha King James Version’

      Mungayankhe kuti: ‘Ngati lanu liri pafupi, ndingakonde kugaŵana nanu kanthu kena kamene ndakawona kukhala kolimbikitsa kwambiri.’

      Kapena munganene kuti: ‘Anthu ambiri amagwiritsira ntchito matembenuzidwe amenewo a Baibulo, ndipo ine mwinine ndiri nalo m’laibulale langa.’ Ndiyeno mwinamwake wonjezerani kuti: (1) ‘Kodi munadziŵa kuti pachiyambiyambi Baibulo linalembedwa m’chinenero Chachihebri, Chachiaramu, ndi Chigiriki? . . . Kodi inu mumaŵerenga zinenero zimenezo? . . . Chotero tiri okondwera kuti Baibulo latembenuzidwira m’Chicheŵa.’ (2) ‘Tchati ichi (“Mpambo wa Mabukhu a Baibulo,” mu NW) chimasonyeza kuti Genesis, bukhu loyamba la Baibulo, linamalizidwa mu 1513 B.C.E. Kodi munadziŵa, kuti pambuyo pa kulembedwa kwa Genesis, panapita zaka 2 900 Baibulo lonse lathunthu lisanatembenuziridwe m’Chingelezi? Ndipo zoposa zaka 200 zinapita matembenuzidwe a King James Version asanamalizidwe (1611 C.E.).’ (3) ‘Kuyambira zaka za zana la 17, Chingelezi chakhala ndi masinthidwe ambiri. Tawona zimenezo m’nthaŵi ya moyo wathu, kodi sichoncho? . . . Chotero tikuyamikira matembenuzidwe amakono amene amasonyeza mosamalitsa chowonadi choyambirira chimodzimodzicho m’chinenero chimene timalankhula makono.’

      ‘Muli ndi Baibulo lanu’

      Wonani mutu waukulu wakuti “New World Translation.”

  • Boma
    Kukambitsirana za m’Malemba
    • Boma

      Tanthauzo: Kakonzedwe ka anthu kopangira ndi kugwiritsira ntchito malamulo. Kaŵirikaŵiri maboma amadziŵikitsidwa mogwirizana ndi magwero ndi ukulu wa ulamuliro wawo. Yehova Mulungu ndiye Wolamulira Wachilengedwe chonse, amene amapereka ulamuliro pa ena mogwirizana ndi chifuniro chake ndi chifuno. Komabe, Satana Mdyerekezi, wopandukira ulamuliro wa Yehova wamkulu, ali ‘wolamulira wa dziko’—mololedwa ndi Mulungu kwa kanthaŵi. Baibulo limasonyeza dongosolo ladziko lonse la ulamuliro wandale zadziko kukhala chirombo ndipo limanena kuti “chinjoka [Satana Mdyerekezi] chinampatsa [chirombo] mphamvu yake, ndi mpando wake wachifumu, ndi ulamuliro waukulu.”—Yoh. 14:30; Chiv. 13:2; 1 Yoh. 5:19.

      Kodi nkotheka kwa anthu kukhazikitsa boma limene lidzabweretsadi chimwemwe chosatha?

      Kodi cholembedwa cha mbiri ya anthu chimasonyezanji?

      Mlal. 8:9: “Wina apweteka mzake pomlamulira.” (Zimenezi ziridi zowona ngakhale kuli kwakuti maboma ena ndi olamulira anayamba ndi chitsanzo chabwino.)

      “Chitaganya chirichonse chimene chinaliko potsirizira pake

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena