Boma
Tanthauzo: Kakonzedwe ka anthu kopangira ndi kugwiritsira ntchito malamulo. Kaŵirikaŵiri maboma amadziŵikitsidwa mogwirizana ndi magwero ndi ukulu wa ulamuliro wawo. Yehova Mulungu ndiye Wolamulira Wachilengedwe chonse, amene amapereka ulamuliro pa ena mogwirizana ndi chifuniro chake ndi chifuno. Komabe, Satana Mdyerekezi, wopandukira ulamuliro wa Yehova wamkulu, ali ‘wolamulira wa dziko’—mololedwa ndi Mulungu kwa kanthaŵi. Baibulo limasonyeza dongosolo ladziko lonse la ulamuliro wandale zadziko kukhala chirombo ndipo limanena kuti “chinjoka [Satana Mdyerekezi] chinampatsa [chirombo] mphamvu yake, ndi mpando wake wachifumu, ndi ulamuliro waukulu.”—Yoh. 14:30; Chiv. 13:2; 1 Yoh. 5:19.
Kodi nkotheka kwa anthu kukhazikitsa boma limene lidzabweretsadi chimwemwe chosatha?
Kodi cholembedwa cha mbiri ya anthu chimasonyezanji?
Mlal. 8:9: “Wina apweteka mzake pomlamulira.” (Zimenezi ziridi zowona ngakhale kuli kwakuti maboma ena ndi olamulira anayamba ndi chitsanzo chabwino.)
“Chitaganya chirichonse chimene chinaliko potsirizira pake chinatha. Mbiri iri ndi nkhani ya zoyesayesa zimene zinalephera, kapena zolinga zimene sizinakwaniritsidwe. . . . Chotero, monga wolemba mbiri, munthu ayenera kukhala ali ndi lingaliro la kusapeŵeka kwa tsoka.”—Henry Kissinger, wasayansi yandale zadziko ndi profesala pankhani zaboma, monga momwe kwagwidwira mawu mu The New York Times, October 13, 1974, p. 30B.
Kodi nchiyani chimene chimapinga zoyesayesa za anthu m’nkhani za boma?
Yer. 10:23: “Yehova, ndidziŵa kuti njira yamunthu siiri mwa iye mwini; sikuli kwa munthu woyenda kulongosola mapazi ake.” (Mulungu sanapereke chilolezo ku chilengedwe chake chaumunthu kuti chidziyambire njira yake yosadalira pa Mulungu.)
Gen. 8:21: “Ndingaliro ya mtima wamunthu iri yoipa kuyambira paunyamata wake.” (Siolamulira okha koma ndi olamulidwa omwe onsewo amabadwira mu uchimo, ndi zikhoterero zadyera.)
2 Tim. 3:1-4: “Masiku otsiriza zidzafika nthaŵi zoŵaŵitsa. Pakuti anthu adzakhala odzikonda okha, okonda ndalama, . . . osayanjanitsika, . . . otukumuka mtima.” (Mavuto oyang’anizana ndi anthu lerolino sangathetsedwe kotheratu ndi mtundu umodzi wokha; amafunikira kugwirizana kotheratu kwa mitundu yonse. Koma zikhumbo zadyera zimalepheretsa zimenezo ndipo zimalepheretsanso moipa kwambiri chichirikizo chowona chirichonse pakati pa magulu osiyanasiyana mkati mwa mitundu.)
Baibulo limavumbulanso kuti mphamvu zoposa anthu zikugwira ntchito m’zochitika za anthu. “Dziko lonse lapansi ligona mwa woipayo.” (1 Yoh. 5:19) “Tiri ndi nkhondo, osati yomenyana ndi mwazi ndi thupi, koma yomenyana . . . ndi olamulira adziko amdima uno, yomenyana ndi makamu a mizimu yoipa mmalo akumwamba.” (Aef. 6:12, NW) “Mawu ouziridwa ndi ziwanda . . . amapita kwa mafumu adziko lonse lapansi lokhalidwa ndi anthu, kuwasonkhanitsira pamodzi kunkhondo yatsiku lalikulu la Mulungu Wamphamvuyonse.”—Chiv. 16:14, NW.
Kodi anthu angapeze motani mpumulo wosatha ku chisalungamo cha boma ndi chitsenderezo?
Kodi kuika amuna ena m’malo antchito kudzathetsa vutolo?
Kodi siziwona kuti kaŵirikaŵiri kumene masankho ali aufulu amuna okhala mu ulamuliro amachotsedwa mwa masankho pambuyo pa zaka zoŵerengeka chabe? Chifukwa ninji? Ambiri samakhutira ndi ntchito yawo.
Sal. 146:3, 4: “Musamakhulupirira zinduna, kapena mwana wamunthu, amene mulibe chipulumutso mwa iye. Mpweya wake uchoka, abwerera kumka kunthaka yake; tsiku lomwelo zotsimikiza mtima zake zitayika.” (Chotero, maprogramu alionse a kuwongolera zinthu amene olamulira amayambitsa amasiyiridwa ena ndipo kaŵirikaŵiri amalekedwa.)
Mosasamala kanthu za amene wolamulirayo ali, iye adzakhalabe mbali yadziko lino limene likukhala m’mphamvu ya Satana.—1 Yoh 5:19.
Kodi chiukiro chachiwawa ndicho yankho?
Ngakhale ngati olamulira oipa angagubuduzidwe ndipo malamulo osalungama nachotsedwa, boma latsopano lidzapangidwabe ndi anthu opanda ungwiro ndipo lidzakhalabe mbali yadongosolo landale zadziko limene Baibulo limanena momvekera bwino kuti liri muulamuliro wa Satana.
Mat. 26:52: “Tabweza lupanga lako m’chimakemo, pakuti onse akugwira lupanga adzawonongeka ndi lupanga.” (Yesu ananena zimenezi kwa mmodzi wa atumwi ake panthaŵi imene ulamuliro waboma unali kugwiritsiridwa ntchito molakwa motsutsana ndi Mwana wa Mulungu mwiniyo. Pakuti ndinjira ina yoyenerera kwambiri yotani imene munthu akanamenyera nkhondo, ngati zimenezo zinali chinthu cholungama kuchichita?)
Miy. 24:21, 22: “Mwananga, opa Yehova ndi mfumu yomwe, osadudukira anthu osinthasintha. Pakuti tsoka lawo lidzawoneka modzidzimuka; ndipo ndani adziŵa chiwonongeko cha zaka zawo?”
Pamenepa, kodi nchiyani, chimene chiri chothetsera mavuto a chisalungamo ndi chitsenderezo?
Dan. 2:44: “Mulungu wakumwamba adzaika ufumu [boma] woti sudzawonongeka kunthaŵi zonse, ndi ulamuliro wake sudzasiyidwira mtundu wina wa anthu, koma udzaphwanya ndi kutha maufumu awo onse, nudzakhala chikhalire.”
Sal. 72:12-14: “Pakuti [mfumu yoikidwa ya Yehova, Yesu Kristu] adzapulumutsa waumphaŵi wofuulayo; ndi wozunzika amene alibe mthandizi. Adzachitira nsoni wosauka ndi waumphaŵi, nadzapulumutsa moyo wa aumphaŵi. Adzawombola moyo wawo ku chinyengo ndi chiwawa; ndipo mwazi wawo udzakhala wamtengo pamaso pake.” (Kudera nkhaŵa kwake ndi anthu oterewa pamene anali padziko lapansi—kuwachiritsa kwake, kudyetsa makamu, ngakhale kupereka moyo wake kaamba ka iwo—kumasonyeza kuti adzakhala wolamulira wonenedweratuyo mu ulosi.)
Wonaninso tsamba 376-380, pamutu wakuti “Ufumu.”
Kodi nchifukwa ninji tiyenera kulingalira mwamphamvu zimene Baibulo limanena ponena za mtsogolo mwa boma?
Olamulira aumunthu sakupereka zimene mtundu wa anthu ukufuna mofulumira
Talingalirani zinthuzi zimene anthu kulikonse amafuna, zimene maboma aumunthu sakupereka koma zimene Mulungu walonjeza: (1) Moyo m’dziko lopanda chiwopsezo chankhondo.—Yes. 2:4; Sal. 46:9, 10. (2) Chakudya chokwanira aliyense.—Sal. 72:16. (3) Nyumba zabwino zokwanira aliyense.—Yes. 65:21. (4) Ntchito yokhutiritsa aliyense woyifuna, kotero kuti akhoze kudzichirikiza iwo eni ndi mabanja awo.—Yes. 65:22. (5) Moyo umene uli wosadodometsedwa ndi matenda ndi nthenda.—Chiv. 21:3, 4. (6) Chiweruzo cholungama, kupanda tsankhu lachipembedzo, laufuko, lachuma, ndi lautundu.—Yes. 9:7; 11:3-5. (7) Kukhala ndi chisungiko, popanda upandu kwa munthuyo kapena chuma zochokera kwa apandu.—Mika 4:4; Miy. 2:22. (8) Dziko m’limene mikhalidwe yofunika koposa imaphatikizapo chikondi, chifundo, kudera nkhaŵa ndi munthu mnzako, ndi kulankhula chowonadi.—Sal. 85:10, 11; Agal. 5:22, 23.
Kwa zaka zikwi zambiri, olamulira andale zadziko akhala akulonjeza anthu awo mikhalidwe yabwinopo. Nzotulukapo zotani? Ngakhale kuli kwakuti anthu m’maiko ambiri ali ndi chuma chakuthupi chochulukirapo, iwo saali achimwemwe kwambiri, ndipo mavuto oyang’anizana nawo ngocholoŵana kwambiri koposa ndi kale lonse.
Maulosi a Baibulo atsimikizira kukhala odalirika kotheratu
Zaka zana limodzi pasadakhale Mawu a Mulungu adaneneratu mkhalidwe wa Babulo wa ulamuliro wa dziko, ndiponso mmene potsirizira pake mphamvu yake ikawonongedwera, limodzinso ndi chenicheni chakuti, atakhala bwinja, likulu lake silikakhalidwanso konse. (Yes. 13:17-22) Pafupifupi zaka mazana aŵiri pasadakhale, ngakhale Koresi asanabadwe, Baibulo linamneneratu mwa kutchula dzina lake kuphatikizapo ntchito yake m’zochitika za mitundu yonse. (Yes. 44:28; 45:1, 2) Amedi ndi Aperisi asanafikire kukhala ulamuliro wa dziko, mphamvu yake, mpangidwe wake wa uŵiri, ndi mmene akathera zonse zinanenedweratu. Zoposa zaka mazana aŵiri pasadakhale zochita za ulamuliro wa dziko wa Girisi motsogozedwa ndi mfumu yake yoyamba zidanenedweratu, kudzanso kwa pambuyo pa kugaŵanika kwa ulamulirowo kukhala mbali zinayi.—Dan. 8:1-8, 20-22.
Baibulo lidaneneratu mwatsatanetsatane mikhalidwe yadziko ya tsiku lathu, ndipo linatichenjeza kuti maboma onse a anthu adzathedwa ndi Mulungu ndi kuti Ufumu wa Mulungu kupyolera mwa Mwana wake, Yesu Kristu, udzalamulira pa anthu onse.—Dan. 2:44; 7:13, 14.
Kodi siiri njira yanzeru kulabadira magwero achidziŵitso amene atsimikizira kukhala odalirika nthaŵi zonse?
Boma lolamulidwa ndi Mulungu ndiro njira yotsimikizirika yokha yothetsera mavuto a anthu
Mavuto amene afunikira kuthetsedwa afunikira mphamvu, maluso, ndi mikhalidwe imene palibe anthu amene ali nayo. Mulungu angakhoze kuwonjola anthu ku chisonkhezero cha Mdyerekezi ndi ziwanda zake, ndipo Iye walonjeza kutero, koma palibe munthu amene angatero. Mulungu wachita makonzedwe a kuchita zimene sayansi ya zamankhwala sikanatha konse kukwaniritsa—kuchotsa tchimo, motero kuthetsa matenda ndi imfa ndi kupangitsa kukhala kothekera kwa anthu kukhala amene iwo akufunadi kukhala. Mlengi ali ndi chidziŵitso chofunikacho (cha dziko lapansi ndi njira zonse za kusintha kwa moyo) kuthetsa mavuto a kulima chakudya ndi kutetezera kuipitsidwa kwaupanduko, koma kaŵirikaŵiri zoyesayesa za anthu zimapanga mavuto owonjezereka. Mawu a Mulungu akusanduliza kale anthu kotero kuti awo amene akulabadira malangizo ake amakhala anthu achifundo, achikondi okhala ndi makhalidwe abwino apamwamba, chitaganya cha anthu amene amakana kunyamula zida zankhondo motsutsana ndi munthu mnzawo ndi amene amakhala mu mtendere weniweni ndi ubale ngakhale kuli kwakuti akuchokera kumitundu yonse, mafuko, ndi timagulu tazinenero.
Kodi ndiliti pamene Ufumu wa Mulungu udzachotsa dongosolo la dziko liripoli? Wonani mutu waukulu wakuti “Madeti” ndi “Masiku Otsiriza.”