Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g92 11/8 tsamba 12-18
  • Dziko Latsopano Lokhutiritsa kwa Onse

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Dziko Latsopano Lokhutiritsa kwa Onse
  • Galamukani!—1992
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Zothetsera Mavuto Zapanthaŵi Imodzi
  • Mavuto Ena Akonzedwa
  • Siloto la Ziyembekezo Zongoyerekezera
  • Dziko Latsopano Lidzakukhutiritsani
  • Ulamuliro Wotsatirapo wa Dziko Lonse Lapansi
    Boma Lathu la Dziko Likudza’lo—Ufumu wa Mulungu
  • Kukhala Nzika ya Boma la Mulungu
    Mungathe Kukhala ndi Moyo Kosatha m’Paradaiso pa Dziko Lapansi
  • Boma la Mulungu la Mtendere
    Mungathe Kukhala ndi Moyo Kosatha m’Paradaiso pa Dziko Lapansi
  • Boma
    Kukambitsirana za m’Malemba
Onani Zambiri
Galamukani!—1992
g92 11/8 tsamba 12-18

Dziko Latsopano Lokhutiritsa kwa Onse

MULIMONSE mmene kungakhalire kovuta kukhulupirira, dziko latsopano liridi pafupi. Lidzafika panthaŵi yake kudzapulumutsa dziko lathu lapansili kukhoza kwake kuchirikiza moyo kusanawonongedwe kotheratu. Ndipo dziko lapansili lidzachotsa maupandu onse owopseza kukhalapo kwa munthu. Kodi lidzachita zimenezi motani?

Pambuyo pa kusonya kukuwawitsa kwa mkhalidwe wadziko, wolemba mbiri yakale Arnold J. Toynbee zaka zambiri zapitazo anafunsa kuti: “Kodi tidzachitanji kuti tipulumuke?” Poyankha funso la iyemwini, anati: “M’ndale zadziko, pangani dongosolo lovomerezedwa ndi lalamulo lachigwirizano la boma ladziko.”

Komabe, ngakhale kuti liri “dongosolo lachigwirizano,” dziko latsopano lirinkudzalo silidzakhala “m’ndale zadziko.” Silidzaphatikizapo demokrase kapena mtundu wina uliwonse wa mpangidwe wandale zadziko zopangidwa ndi anthu. Dziko latsopano limeneli lidzakwaniritsa zonulirapo zake chifukwa chakuti boma limodzi lokha ndilo limene lidzalilamulira. M’zochitika zochititsa nthumanzi zotsatizanatsatizana, boma lapadziko lonse limeneli lidzathetsa mofulumira mavuto onse oyang’anizana ndi mtundu wa anthu lerolino. Motani? Mwa kuchotsa nakatande wa mavuto amenewa ndi zopinga zimene kaŵirikaŵiri kwambiri zimalepheretsa zoyesayesa za kuwakonza.

Kwenikweni, kodi zimenezo zikakwaniritsidwa motani? Kodi anthu opanda ungwiro sakalamulirabe, anthu amene atsimikizira kukhala oipa ndi osakhoza kuthetsa mavuto a anthu? Eya, tangoyerekezerani ngati panali olamulira angwiro a boma ladziko limeneli, okhala ndi zabwino za nzika zawo mopanda dyera m’mitima yawo. Ndiyeno talingalirani mmene mavutowo akathetsedwera.

Zothetsera Mavuto Zapanthaŵi Imodzi

Pokhala boma la padziko lonse likakhala ndi olamulira angwiro, sipakakhalanso mtundu uliwonse wokhala ndi mtundu wakewake wa boma. Atsogoleri aboma, akazembe, ndi andale zadziko ena sakachitanso ulamuliro pa maiko ambiriwo, mafuko, ndi mitundu ya anthu. Malikulu ambiri amomwemo ndi a mitundu, limodzi ndi nyumba zawo ndi nyumba zachifumu, sizikafunikanso. Zimenezi zikathetsa kusungidwa kodya ndalama kwa nyumba zokwera mtengozo, limodzi ndi ndalama zolipilira akuluakulu aboma pokafika kumisonkhanoyo, misonkhano ya makomiti, ndi misonkhano yadziko ndi misonkhano ya maiko onse. Amene akakhala atachokanso ndiwo magulu a anthu onse olamulira boma owawanya, limodzi ndi achiŵiri awo ambirimbiri, alembi, makalaliki, limodzi ndi malamulo awo ochedwetsa zinthu.

Mtendere ukakhala chinthu chenicheni chifukwa chakuti utundu wogaŵanitsa ukakhala utachoka, utalowedwa m’malo ndi ulamuliro wogwirizana wa padziko lonse. Magulu ankhondo, ankhondo yapamadzi, ndi ankhondo yamumlengalenga, limodzi ndi zida zawo zonse, akazembe ankhondo apamwamba, ndi maofesala wamba, sakafunikiranso kutetezera ulamuliro wa dziko lirilonse. Ndiponso sipakakhala madongosolo alionse a azondi. Pansi pa boma lapadziko lonse lokhala ndi olamulira angwiro, sipakakhala malonda wamba kapena katangale kumene zida zankhondo zikatha kugulidwa kapena kugulitsidwa; ndiponso sipakakhala malo okanganirana. Anthu onse a padziko lapansi akakhala gulu limodzi la ubale wosagaŵanika. Chifukwa chake, utundu ukazimiririka.

Talingalirani mapindu owonjezereka amene akapezeka kwa anthu olamulidwa ndi boma limodzi losagaŵanika lokhala ndi olamulira angwiro. Eni mabizinesi amphamvu, onga opanga zida zankhondo, sakakhala ndi chisonkhezero chirichonse pa atsogoleri andale zadziko kotero kuti akatha kupitirizabe kupanga ndi kugulitsa zida zawo zowonongazo. Sipakakhala onyengerera aukatswiri alionse kuti anyengerere akuluakulu aboma pamalamulo ena kapena oyembekezeredwa kukhala malamulo okhudza zokomera malo amomwemo okha; sipakakhalanso nakatindi wosalamulirika wa madipatimenti aboma ambirimbiri apadera ogwira ntchito zosiyana ndi chifuno chawo, othera ndalama zambirimbiri pantchito zosathandiza zimene zimapindulitsa ochepa chabe; sipakakhalanso mavuto a kulephera kuchita mogwirizana ndi malamulo othetsa kuipitsidwa kwa mpweya kaamba ka zifukwa zamalonda zadyera (kuti mapindu akhale aakulube); sipakakhala kudodometsedwa kwa malamulo amene amatetezera mitundu ya zamoyo zimene ziri pangozi ya kusolotsedwa ndi zolinga zamphamvu mwapadera.

Mavuto Ena Akonzedwa

Boma ladziko langwiro loterolo silikalekelera chisalungamo. Litatenga ulamuliro, likatsimikizira kuti machitidwe aupandu asamaliridwa m’njira yoyenera, yogwirizana ndi chiweruzo cholungama. Chotero, nzikazo sizikakhala ndi mantha akuti ambanda aupandu owonjezereka akapitirizabe kuchita mbandazo.

Ndipo bwanji za dongosolo lapadziko lonse lapansi la magulu ogwira ntchito ya upandu wolinganizidwa ndi machitachita ocholowana ogulitsa anamgoneka? Boma ladziko langwiro likathetsa psiti zonsezi. Malamulo amaiko oletsa kupereka oswa malamulo kwa olamulira oyenerera sakakhalanso pobisalira apandu a m’maiko onse amenewo. Kugwiritsira ntchito mwaluntha zoperewera za malamulo amomwemo ndi kugwirizana kwawo ndi andale zadziko osonkhezerawo kochitidwa ndi akuswa malamulo amenewa kukakhala chinthu chakale. Mchitidwe umodzi wa kuthetsa upandu ukachotseranso dziko lapansi mavuto ena ambiri a anthu, onga kutchova juga, kumenyana kwa timagulu totsutsana, zithunzithunzi zosonyeza umaliseche, uchiwerewere, ndi kuzembetsa zinthu. Ndikukonzedwa kogwira mtima ndi kosungitsa chuma kotani nanga!

Inde, zothetsa nzeru zonse zocholowana, zalukanelukane, ndi zovuta zimene zikuthetsa nzeru maganizo akuthwa koposa a anthu lerolino zikathetsedwa kotheratu m’dziko latsopano loterolo. Ndipo chirichonse chikathetsedwa kosatha—kotheratu. Mibadwo yapambuyo sikafunikira kuvutikanso nazo.

Siloto la Ziyembekezo Zongoyerekezera

‘Komatu,’ inu mungafunse kuti, ‘kodi olamulira angwiro adzachokera kuti kudzalamulira dziko latsopano loterolo?’ Adzagaŵiridwa ndi Mlengi wa anthu! Kodi zimenezi zikuwonekera kukhala zosakhulupiririka konse? Eya, tangolingalirani: Ngati munali ndi mphamvu ya kutero, kodi simukathetsa mikhalidwe yonse padziko lapansi imene imapangitsa nsautso yaikulu yotere? Ndithudi mukatero! Pamenepa, kodi tiyenera kulingalira, kuti Mlengi wathu adzachita zochepera?

Chenicheni nchakuti, Mlengi wathu wachikondi akulinganiza kulenga dziko latsopano, ndipo njira yolibweretsera ndiyo boma ladziko lolungama. Limeneli ndilo limene Mwana wake, Yesu Kristu, anaphunzitsa anthu kupempherera mwamawu akuti: “Ufumu wanu udze. Kufuna kwanu kuchitidwe, monga kumwamba chomwecho pansi pano.”—Mateyu 6:10.

Ufumu umenewo ndiboma lenileni, boma ladziko. Mfumu yake, Yesu Kristu, ‘adzakhala ndi nzika kuchokera kunyanja kufikira kunyanja ndi kuchokera ku Mtsinje kufikira malekezero a dziko lapansi.’ (Salmo 72:8) Ndipo mwamsanga lidzalowa mmalo mwa maboma onse a anthu, monga momwe Mawu a Mulungu amalonjezera pamene amati: “Ndipo masiku a mafumu aja Mulungu wa kumwamba adzaika ufumu [boma lolamulidwa ndi Mfumu ya Mulungu, Yesu Kristu] woti sudzawonongeka ku nthaŵi zonse, ndi ulamuliro wake sudzasiyidwira mtundu wina wa anthu, koma udzaphwanya ndi kutha maufumu awo onse [alerolinowa], nudzakhala chikhalire.”—Danieli 2:44.

Chifukwa chakuti boma ladziko lokhazikitsidwa ndi Mulungu wa kumwamba limeneli lidzalamulidwa ndi olamulira osakhala aumunthu, lidzachita zabwino zonse zimene olamulira aumunthu ali osakhoza kuchita. Baibulo limafotokoza boma la Mulungu kukhala ulamuliro wakumwamba wolamulidwa ndi munthu mmodzi umene udzakhala ndi Mfumuyo, Yesu Kristu, akumathandizidwa ndi antchito okwanira 144,000 amene ali anthu auzimu. Olamulira onsewa adzakhala anthu odalirika amene anasonyeza umphumphu wosasweka mkati mwa moyo wawo padziko lapansi asanaukitsidwire kumoyo wa kumwamba. Onsewo adzakhala okhoza bwino kopambana kugwirira ntchito zokomera mtundu wa anthu chifukwa chakuti anakhalapo ndi zosowa za anthu pamene anakhala ndi moyo padziko lapansi.—Chivumbulutso 14:1-3.

Taganizani za mavuto amene zimenezi zimathetsa. Chifukwa cha kukhala osakhoza kufa, olamulira auzimu amenewa sadzatopa kapena kufa. (1 Akorinto 15:50, 53) Ndipo sangaipitsidwe ndi mayesero a kukhotetsa chiweruzo kapena kuchita tsankho atalandira ziphuphu. Ndi iko komwe, kodi nchiyani chimene munthu angapereke mtseri monga chiphuphu kwa munthu wauzimu wosakhoza kufa? Kodi zingakhale ndalama, bokosi la mowa wokwera mtengo, ulendo womka kuchisumbu chokongola, kapena matikiti olowera m’chiwonetsero kapena m’konsati? Zinthu zakuthupi zimenezi zingakope thupi ndi mwazi koma osati zolengedwa zauzimu zimenezi. Chotero anthu olamulidwa ndi olamulira amenewa sadzavutika ndi kuipa kwa boma kumene kuli kofala kwambiri lerolino.

Dziko Latsopano Lidzakukhutiritsani

Kodi ndinu munthu wachikulire? Taganizirani za chidziŵitso chonse, maluso, ndi zokumana nazo zimene mwapeza m’kupita kwazaka. Koma kodi mwawona kuti ngakhale kuti maganizo anu ndi malingaliro zingakhale zabwino kwambiri, pali kufooka kwapang’onopang’ono ndi kosalekeza kwa thanzi lanu lakuthupi? Thupi lanu silimalabadiranso kuzifunsiro zanu zamaganizo monga momwe linkachitira kale. Inde, kulimba kwathupi lanu kukuguga, nyonga yanu ikufwifwa, ndipo kupirira kwanu kukucheperachepera. Maso anu ndi makutu zikunyonyosoka ndipo minofu yanu ikutha mphamvu mowonjezereka pamene zopweteka zikufikira kukhala zakaŵirikaŵiri mowonjezereka.

Koma tayesani kuyerekezera nzeru yopezedwa mkati mwa zaka zambiri za moyo m’thupi losalala ngakhale labwinopo koposa limene munali nalo pamene munali wazaka za m’ma 20—inde, kukhoza kwanu kwakuthupi kukhala kwabwino mofanana ndi maganizo anu. Taganizani za zinthu zambiri zimene mukanachita m’thanzi lanu labwino! Eya, pokhala ndi thupi labwino chotero likumalabadira kumaganizo anu auchikulire, mukapeza kuti ntchito iriyonse imene mukachita ikakhala yosangalatsa kwambiri. Chidziŵitso chanu chikakukhozetsani kuchita zinthu mogwira mtima koposerapo, zimene zikawonjezera kwambiri chikhutiro chanu. Ndipo ngati muli wachichepere, taganizani kusangalatsa kwa kusungabe mkhalidwe wathupi wauchichepere ndi wanyonga pamene mukupeza nzeru ndi luntha ndi chidziŵitso kosatha.

Tsopano, wonjezerani pa zimenezi, ndi kulingalira za anzanu ndi mabwenzi anu, atsamwali ndi achibale, onsewo kukhala mumkhalidwe umodzimodziwu. Tayerekezerani zimene nonsenu mukanachita m’ntchito za kukonza, kumanga, kapena kusema. Ha, ndiziyembekezo zabwino kwambiri chotani nanga zimene zimenezi zikakhala kwa anthu amaluso, monga akatswiri ojambula, oimba, olinganiza, okongoletsa malo, olima minda, ndi akatswiri olima zomera! Ntchito zawo zikakhala zodabwitsa. Zojambula zokongola, nyumba, madimba, mapaki—inde, kupanga ziwiya zoimbira zabwino ndi luso la kukhoza kuzichita ziri kokha zochepazo.

Chimodzi cha zolinga za boma la dziko latsopano limeneli ndicho kutukulira mtundu wa anthu kuungwiro wakuthupi. Kukhoza kwanu kwa kuwona, kumva, ndi malingaliro ena zikagwira ntchito pamlingo wapamwamba. Kwautali wotani? Eya, ngati boma laumunthu linakulonjezani mankhwala amene anatsimikizira kukonzedwanso kwa theka la kugwira ntchito kwa thupi lanu lonse kwachaka chimodzi mukumalipilira ndalama zochepa chabe, kodi simukakhala woyamba kufuna kuwapeza? Boma ladziko latsopano limeneli likutsimikizira kutukulira kuungwiro wonse kwaulere—osati kwachaka chimodzi, zaka zisanu kapena zaka makumi asanu, koma kuumuyaya wonse.

Musatsutse mukumati chiyembekezo chimenechi chimene chiri pafupi kusangalalidwa ndi anthu padziko lapansi linoli nchosakhulupiririka. Talingalirani, patsamba 15-18, za ena a madalitso amene okonda Mulungu adzasangalala nawo.

[Bokosi/Zithunzi pamasamba 15-18]

Zimene Dziko Latsopano Lidzabweretsa

Kuthetsedwa kwa Nkhondo

“Iwo adzasula malupanga awo akhale zolimira, ndi nthungo zawo zikhale anangwape; mtundu sudzanyamula lupanga kumenyana ndi mtundu wina, ndipo sadzaphunziranso nkhondo.”—Yesaya 2:4.

Mapeto a Upandu ndi Chiwawa

“Koma oipa adzalikhidwa m’dziko.”—Miyambo 2:22.

Nyumba Zabwino ndi Ntchito Yosangalatsa kwa Aliyense

“Ndipo iwo adzamanga nyumba ndi kukhalamo . . . Iwo sadzamanga, ndi wina kukhalamo; iwo sadzawoka, ndi wina kudya.”—Yesaya 65:21, 22.

Dzinthu Dzabwino Dzochuluka Dzoti Onse Adye

“M’dzikomo mudzakhala dzinthu dzochuluka pamwamba pa mapiri.”—Salmo 72:16.

Mtendere Pakati pa Anthu ndi Zinyama

“Mmbulu udzakhala pamodzi ndi mwana wa nkhosa, ndipo nyalugwe adzagona pansi ndi mwana wa mbuzi; . . . ndipo mwana wamng’ono adzazitsogolera.”—Yesaya 11:6.

Sipadzakhalanso Matenda, Ukalamba, Kapena Imfa

“Ndipo adzawapukutira misozi yonse kuichotsa pamaso pawo; ndipo sipadzakhalanso imfa; ndipo sipadzakhalanso maliro, kapena kulira, kapena chowawitsa; zoyambazo zapita.”—Chivumbulutso 21:4.

Chiukiriro cha Okondedwa Akufa

“Ikudza nthaŵi, imene onse ali m’manda adzamva mawu [a Yesu], nadzatulukira.”—Yohane 5:28, 29.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena