Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • go mutu 1 tsamba 4-17
  • Ulamuliro Wotsatirapo wa Dziko Lonse Lapansi

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Ulamuliro Wotsatirapo wa Dziko Lonse Lapansi
  • Boma Lathu la Dziko Likudza’lo—Ufumu wa Mulungu
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • THANZI LANGWIRO LOSANGALALIRA NDI MOYO
  • MALO A BOMA LA DZIKO LONSE
  • Kukhala Nzika ya Boma la Mulungu
    Mungathe Kukhala ndi Moyo Kosatha m’Paradaiso pa Dziko Lapansi
  • Dziko Latsopano Lokhutiritsa kwa Onse
    Galamukani!—1992
  • Boma la Mulungu la Mtendere
    Mungathe Kukhala ndi Moyo Kosatha m’Paradaiso pa Dziko Lapansi
  • M’mene Tingasangalalire ndi Boma la Dziko Kosatha
    Boma Lathu la Dziko Likudza’lo—Ufumu wa Mulungu
Boma Lathu la Dziko Likudza’lo—Ufumu wa Mulungu
go mutu 1 tsamba 4-17

Mutu 1

Ulamuliro Wotsatirapo wa Dziko Lonse Lapansi

1. Kodi okonda ulamuliro wolungama amakondweretsedwa kwambiri ndi lingaliro lotani? Chifukwa ninji?

OKONDA ulamuliro wolungama amakondweretsedwa akangoulingalira. Tsiku la boma la dziko lonse lolonjezedwa’lo likuyandikira. M’kati mwa mbadwo wathu woyanjidwa boma limene’lo lidzatuluka ngati dzuwa ku thambo lopanda mitambo kukuta dziko lapansi ndi kuunika kwake kosangalatsa, kuyambitsa nthawi ya kakhalidwe kosangalatsa kwa anthu onse. Chimene chikuunikiridwa chiyenera kukondweretsa maso athu.

2. Kodi n’chiani chimene chimasangalatsa maso athu ponena za mkhalidwe wa maunansi a anthu?

2 Kaonekedwe kosandulizidwa kakuwala pamaso pathu. Maunansi a anthu pa nthawi ina anali obvuta kwambiri. Koma taonani! Kodi n’chiani chimene chikuchitika pansi pa boma la dziko lonse lofunidwa kwambiri’lo pamene likulamulira? Kuli konse umodzi wa banja lonse laumunthu ukubvomerezedwa kuti ulipo ndi kusungidwa moona mtima kotheratu ndi mwachimwemwe. Ali yense ali bwenzi kwa munthu wina ali yense. Zomangira za unansi wa banja zikumvedwa mpaka m’kati mweni-weni mwa moyo wa munthu ali yense. Limodzi ndi unansi wosangalatsa umene’wu, pali mkhalidwe wabwino kwambiri wa kukhala wothandiza mokondweretsedwa kwenikweni ndi thanzi la ena. Upfuko wogawanitsa sukuonjezereka’nso. Iwo onse apanga pfuko limodzi la anthu, okhala ndi makolo amodzi-modzi, onse akumakhala ochokera ku magwero amodzi.

3. Kodi n’chifukwa ninji kuli kwakuti iwo onse amamvana polankhula?

3 Mvetserani! Nzika zonse za boma la dziko lonse zikumvana. Izo zikulankhula chinenero chimodzi cha pa dziko lonse! Eya, kumene’ko kuli ngati kubwerera ku chitsanzo choyambirira cha chinenero cha banja laumunthu! Kale’lo mpaka kudzafika ku zaka zokwanira mazana makumi anai kudza limodzi zapita’zo anthu onse analankhula chinenero chimodzi. Anthu onse anali ndi mpambo umodzi wa mau, kupangitsa kukhala kothekera kwa iwo kumvana chinenero. Kumeneku kunapangitsa kukhala kosabvuta kwa iwo kugwirira ntchito pamodzi m’ntchito iri yonse ya onse. Ndiyeno, mwadzidzidzi, panachitika kusokonezedwa kwa chinenero. Zinenero zambiri zinabuka! Zinenero zazing’ono za m’malo osiyana-si-yana zinabuka. O zimene’zi zinadzetsa kugawanika kotani nanga! Zinenero zautundu zinakhala chuma chochitiridwa nsanje ndi choumiriridwa kuti chiyenera kusungidwa. Chimene’chi ndicho kanthu kena kamene boma la dziko lonse lokha lingakayendetse mwachipambano. Chidzasungidwa!

4. Kodi iwo ali nzika za chiani, ndipo kodi chinenero chao n’chiani?

4 Boma la dziko lonse likuchotsa zopinga zonse za chinenero pakati pa nzika zake. Kunyadira chinenero kwautundu kukufafanizidwa. Kusiyana kwautundu kwatha! Palibe ali yense amene ali nzika ya mtundu uwu kapena uwo. Iwo onse ali nzika za dziko lonse, inde, nzika za dziko latsopano limodzi. Chinenero chimodzi chimene iwo onse akulankhula momvana chiri chinenero chozindikiridwa ndi kugwiritsiridwa ntchito ndi boma la dziko lonse’lo, chinenero cha boma. Ndicho chinenero choyambirira cha mtundu wa anthu, chimene ali yense pa dziko lapansi analankhula kwa zaka zoyambirira mazana khumi ndi asanu ndi atatu za kukhalapo kwa munthu. Chinenero choyambirira chimene’cho chinapititsidwa patsogolo kwambiri sichinafe konse, pakuti anthu apang’ono anapitirizabe kuchigwiritsira ntchito, chikumasungidwa’nso ndi bukhu lalikulu kopambana pa dziko lapansi.

5. Kodi pali masinthidwe otani kwa awo amene ayenera kuyenda ulendo wa kutali ndi kwao?

5 Umodzi wa chinenero umapangitsa kukhala kosabvuta kuyenda ku maiko akutali. Kodi ntchito ya munthu kapena ukatswiri wake imam’funikiritsa kuyenda kumka ku mbali zina za dziko lapansi za kutali ndi kwao? Ha, ndi kodabwitsa chotani nanga m’mene kuliri, ha, ndi kosabvuta chotani nanga m’mene kuliri kwa iye kukhala wopanda kufunikira kwina kwa kukhala ndi chiphaso choyendera (passport)! Iye safunikira kukhala ndi chikalata chosonyeza kuti alibe nthenda; iye safunikira kuoloka malire a mitundu yonse ndi kudzera pa malire ndi pa makasitomu ofufuza. Palibe msonkho wa katundu wolowa. Palibe mitengo ya kusinthana ndalama yodera nayo nkhawa ndi kuiwerengera, pokhala popanda ndalama zosiyana – siyana zogwiritsiridwa ntchito m’zigawo zokhala mu ulamuliro wautundu papitapo. Kuti munthu apewe kutsatira malamulo olowera kapena kutulukira limodzi ndi zikalata za chilolezo (visas), kale’lo anayenera kuchoka pa dziko lapansi. Koma kodi ndani amene amafuna kuchita zimene’zo? Komabe, boma la dziko lonse likudzetsa kusintha kwa mtundu wotero.

6. Bwanji ponena za boma la dziko lonse ndi malamulo osagwirizana pano ndi apo?

6 Komabe, ndithudi, payenera kukhala malamulo ndi malangizo osiyana kaamba ka malo osiyana—siyana pa dziko lapansi. Ai, kutali–tali! Zinali choncho pamene kunali mabungwe opanga malamulo a mzinda, boma laling’ono, boma kapena chigawo ndi mtundu. Pa nthawi imene’yo kugulitsidwa kwa anthu onse ndi kumwedwa kwa zakumwa zoledzeretsa kunali kosabvomerezedwa ndi lamulo m’boma laling’ono limodzi, koma m’boma laling’ono lochita nalo malire munalibe kuletsa. M’dziko lina kuitanitsidwa kuchokera kunja kwa mankhwala ena obvulaza kunali koletsedwa kwambiri, koma mu lina kubzalidwa kwa zomera zina ndi kupangidwa kwa mankhwala obvulaza ndi kugulitsa ndi kutumiza kunja mankhwala otero’wo zinali ntchito zololedwa ndi lamulo ndipo zinadzetsa phindu la ndalama ku boma limene linazipangitsa kukhala zololedwa ndi lamulo. M’dziko lina lolamulidwa ndi chikhulupiriro china chachipembedzo kunali koyenera kotheratu kwa munthu kukhala ndi akazi awiri kapena ambiri, koma m’dziko lina mwamuna angaimbidwe mlandu m’makhothi ndi kulangidwa chifukwa cha kukhala chabe wamitala. Malamulo anasiyana m’dziko ndi dziko, ndipo ogwira ntchito za malamulo, maloya, oimira mlandu ndi aphungu anachuluka. Koma tsopano m’dongosolo latsopano lolamulidwa ndi boma la dziko lonse, pali mpambo umodzi wokha wa malamulo pa dziko lonse lapansi.

7. Kodi n’chiani chimene chiyenera kunenedwa ponena za “mankhwala” operekedwa pa nthawi’yo?

7 Chinthu china chiri’nso choonekera bwino m’boma latsopano la dziko lonse limene’lo. Thanzi lonse la anthu likuonekera kukhala likukonzeka moonjezereka-onjezereka nthawi zonse. Palibe kulakwitsa pa chimene’chi. Thanzi la nzika zomvera za boma la dziko lonse likuongokera’di. Eya, zopweteka ndi zowawa zikutha, makwinya akufafanizika pa nkhope zodera nkhawa kapena zotopa ndi nthawi pa nthawi ina’zo. Ngakhale awo opindika msana chifukwa cha kufooka ndi ukalamba akuongoka pang’ono-pang’ono ndi kuyenda ataongoka mokongola. Konse-konse kuli zizindikiro zakuti anthu okalamba akubwerera ku masiku a ubwana wao. Mwachionekere, ali yense akusangalala ndi mwai wa kukhala ndi moyo, ndipo tsiku latsopano liri lonse limalandiridwa ndi chithokozo kaamba ka tsiku lina la moyo. Kufooka kwa thupi sikukuonjezeka’nso pamene nthawi ikupita. Mphamvu za thupi zikuonjezeka, ndipo matupi sakutha’nso mphamvu. “Mankhwala” ali onse amene boma la dziko lonse’lo likuwapereka, chithandizo chake cha mankhwala chikutulutsa zodabwitsa. Potsirizira pake lidzapereka ungwiro waumunthu.

8. Kodi kaonekedwe kosinthidwa ka dziko lapansi kamasonyezanji ponena za kulamuliridwa kwa mkhalidwe wakunja?

8 Ngakhale malo okhala achilengedwe a mtundu wa anthu akukonzeka moonjezereka-onjezereka. Zolengedwa zonse zikuchititsidwa kukhala ngati zatsopano kachiwiri’nso. Dziko lonse lapansi likukhala malo a kukongola kwa pa dziko lonse lapansi. Boma la dziko lonse’lo liri ndi ofesi yodziwa bwino kwambiri yonena za m’mene kunja kudzachera imene simalakwa. Iro liri ndi ulamuliro wotheratu pa machedwe a kunja. Palibe mbali iri yonse ya dziko lapansi kumene kukuchokera lipoti liri lonse la chirala kapena kubvumba kwa mvula ya pwata-pwata koononga, kapena mikuntho, anamondwe ndi zimphepo. Mphamvu zonse zachilengedwe zikuchititsidwa kukhala zosapambanitsa kaamba ka kupangitsa dziko lonse lapansi kukhala malo okhalamo amtendere. Palibe kusowa chakudya kuli konse, pakuti dziko lapansi likubala zinthu zochuluka kwambiri. Zosowa za anthu m’njira ya chakudya zikukwaniritsidwa bwino lomwe, ndipo zonse’zi zikuthandizira kuongokera kwa thanzi la anthu. Kusaopa kusowa kukukula kwambiri. Mzimu wa unansi ukusonkhezera onse kukhala oolowa manja, ku kuthandizana ndi kugawana. Onse olankhula chinenero chimodzi, onse omaona zomangira za thithithi za unansi wa banja, onse akumakhala nzika zinzao zogonjera ku boma la dziko lonse, onse akugwirizana pamodzi m’kupanga malo ao okhala a dziko lapansi kukhala malo okongola monga momwe kungathekere m’limene angakhaliremo pamodzi kosatha.

THANZI LANGWIRO LOSANGALALIRA NDI MOYO

9. Kodi ndi kusalingana kwakuthupi kotani kuemne kudzakhalapo choyamba ponena za kusangalala kwa munthu ndi moyo?

9 M’malo mwakuti lipereke kulingana kwa nzika zake zonse kaamba ka kusangalala ndi moyo kwakuthupi, boma la dziko lonse likuchita ntchito yokonza matupi ndi maganizo a nzika zake zonse zokhulupirika. Kodi pali ali yense wa ife amene samakhala ndi kanthu kena kolakwika kwa iye? Ponena za thupi ndi maganizo, ena ali oipa kwambiri koposa ena. Ganizirani za awo amene anataya chiwalo chimodzi kapena zambiri za thupi. Ganizirani za awo amene ali ndi ziwalo zao koma amene kupyolera mwa manjenje sakupeza chisangalalo ku kuzigwiritsira ntchito. Ganizirani za awo amene ziwalo zao za m’kati zafooketsedwa kotero kuti matupi ao sakugwira ntchito mwachibadwa. Kutenga kotheratu kuyendetsa zochitika za anthu kwa boma la dziko lonse kukapeza anthu akubvutikabe ndi nthenda zonyansa. Ena ali ndi maso amene samaona kweni-kweni, ena ali ndi makutu koma amakhala osamva, ena ali ndi chiwalo cholankhulira koma sangachigwiritsire ntchito kulankhula ndi ena amene angathe kumva kulankhula komvekera bwino. Yerekezerani kusalingana konse kwa thupi kumene kuli kotsimikizirika kukhalapo poyamba ponena za kukhala kwa ali yense ndi zisangalalo ndi madalitso okwanira a kukhala ndi moyo pansi pa boma lokhazikitwsidwa la pa dziko lonse!

10. Kodi ndi motani m’mene kukhoza kukwaniritsa zosowa za thanzi za anthu onse kukusonyezedwera?

10 Ha, ndi wamphamvu chotani nanga m’mene ulamuliro watsopano umene’wu udzadzisonyezera kukhala wokhoza kukwaniritsa zofunika za mkhalidwe’wo! Ha, ndi chitandizo chachikulu chotani nanga chimene uwo ukupanga ku kupanda ungwiro kwa anthu chimene chikupangitsa kukhala ndi moyo kwangwiro kwa nzika zake zonse zodzipereka! Wopunduka akuyenda, inde, akuluphalumpha mosangalala. Mikono ndi miyendo yoduka ikubwezeretsedwa modabwitsa. Osaona akuona, osamva akumva osalankhula akulankhula ndi kuyimba mosangalala. Kaonekedwe kosakondweretsa ka thupi ndi nkhope kakutha. Ponena za kaonekedwe kao ndiwo mbadwo wa mtundu wa anthu umene boma’lo moyenerera lingaunyadire. Pamenepa, ndi kodabwitsa chotani nanga, m’mene kuliri kuti palibe zipatala zopezeka, palibe malo okhala amisala, palibe malo obindikiritsira odwala kumene anthu odwala nthenda zoopsya zopatsana amakaikidwa!

11. Kodi ndi motani m’mene nthawi iriri yoyenera kaamba ka mbadwo wosangalala motero ndi zinthu zotero’zo?

11 Aha, inde, moyo udzakhala woyenera kukhala nawo pa nthawi imene’yo! Koma kodi n’chifukwa ninji mbadwo wa mtundu wa anthu umene unangokhalapo pa nthawi ina m’mbiri ya anthu ungakhale woyanjidwa kwambiri ndi mwai wa mtengo wapatali wa kukhala mu ungwiro waumunthu m’malo okhala abwino kwambiri a pa dziko lapansi? Bwanji ponena za mibadwo ya papitapo? Bwanji ponena za achibale eni-eni amene afa ndi matenda kapena mikhalidwe ina, inde, makolo a nzika zamoyo zonse’zi za boma la dziko lonse? Iwo akukumbukiridwabe ndi olandira madalitso a dongosolo latsopano lolungama okhala ndi moyo amene’wa. Mofananamo boma la dziko lonse likukumbukira awo amene abwerera ku pfumbi la pansi ku limene munthu woyamba anatengedwako poyamba.

12. Kodi ndi motani m’mene boma la dziko lonse lidzadzisonyezera kukhala lozindikira akufa?

12 Boma la dziko lonse’lo silimafuna miyala ya pamanda iri yonse, manda achifumu kapena zosonyeza pa manda ziri zonse kuti zitikumbutse za awo amene anatengedwa mopanda chifundo ndi mdani wa mtundu wonse wa anthu, Imfa. Iro liri boma osati lopindulitsa nzika zokha zamoyo, koma’nso anthu akufa osawerengeka, amene poyerekezera awo amene ali chikhalirebe ndi moyo ali kachigawo kakang’ono chabe. Iro liri ndi zifuno zabwino kwambiri kaamba ka akufa. Iro lakhomereza m’mitima ya amoyo chiyembekezo cha kulandira’nso amoyo mu ulamuliro wa boma la dziko lonse awo amene anagona m’tulo ta imfa m’pfumbi la pansi. Iro liri chire kupereka zilangizo kwa nzika zake zamoyo kuzipangitsa kupanga kukonzekera kosangalala, kwachikondi ndi makonzedwe kaamba ka kubwerera’nso kwa akufa. Boma la dziko lonse likufuna kuti dziko lonse lapansi lidzazidwe bwino lomwe ndi nzika, ndipo chiukiriro cha anthu akufa ndicho njira yaikulu yochitira ntchito yodabwitsa ya boma imene’yi. Polingalira mphamvu yake yoposa ya anthu, palibe bvuto limene iro lidzakhala nalo ndi chinthu chotero’cho monga ngati chiukiriro cha mikhole yonse ya imfa.

13. Kodi ndi funso lotani lonena za chipembedzo limene chiukiriro chimalisonkhezera?

13 Komabe, bwanji, ponena za zikhulupiriro zonse zachipembedzo, malingaliro ndi mikhalidwe imene anthu oukitsidwa’wo adzabwera’nso nazo? M’kati mwa nthawi ya moyo wao wakale wa pa dziko lapansi, chipembedzo chinakhala mphamvu yogawanitsa kopambana yobvutitsa mtundu wa anthu. Chifukwa cha chiyambi cha chipembedzo cha anthu oukitsidwa’wo, kodi kubwerera’nso kwao ku moyo sikudzachititsa kugawanika kwa dziko koopsya, kukumadzutsa’nso kusankhana kwachipembedzo, maudani ndi mikangano ya mtundu wachiwawa?

14. Kodi n’chifukwa ninji chiukiriro chidzakonza lingaliro lachipembedzo la anthu oukitsidwa kwa akufa?

14 Eya, pamene tikuyang’ana pa nkhope ya dziko lapansi mu ulamuliro wa boma’lo, tikudzifunsa kuti: ‘Ziri kuti nyumba zachipembedzo zosongoka ndi za zimphuli zazitali, machalichi akulu, machalichi, misikiti, tiakachisi, mafano achipembedzo okongola ndi zifanizo?’ Izo zachotsedwa! Ziwalo za m’badwo wa lero lino zimene ziri chikhalirebe ndi moyo zikuchita bwino lomwe mu umodzi popanda zoonjezereka zachipembedzo zonse’zo. Mpangidwe wao wa kulambira umagwirizana ndi choonadi cheni-cheni. Chipembedzo ndi kachitidwe kao ndizo zimene boma la dziko lonse’lo limadzibvomereza, pakuti zimene’zi ziri zopanda nthano zonse zopangidwa ndi anthu nthanthi ndi nthano zongopeka ndi chinyengo. Ponena za akufa oukitsidwa’wo, O ndi ogwiritsidwa mwala chotani nanga m’mene adzakhalira, maka-maka awo amene pa imfa anayembekezera kudzipeza atakhala angelo kumwamba kapena monga mizimu yozindikira m’malawi a moto a purigatoriyo kapena helo wa chizunzo chamuyaya, kapena akusamuka kapena ali mu mkhalidwe Wakugwidwa ndi mzimu! Kuukitsidwira ku moyo pa dziko lapansi ndithudi kudzakhala chiongolero champhamvu ku kulingalira ndi chidziwitso chao chachipembedzo.

15. Kodi ndi motani m’mene anthu oukitsidwa’wo adzatheketsedwera kulambira moyenera?

15 Anthu oukitsidwa’wo adzaphunzira kuti boma la dziko lonse ndiro lija la choonadi, losalekerera cholakwa chachipembedzo. Chotero, iwo tsopano adzaphunzitsidwa choonadi ndipo osati kanthu kena koma choonadi. Mogwirizana pfuko lonse laumunthu lidzakhala lokhoza kulambira ndi choonadi ndipo’nso moona mtima kotheratu.

16. Kodi n’chifukwa ninji sitikuona ali onse akuyenda-yenda monga ansembe kapena atsogoleri achipembedzo?

16 Taona kale kusakhalapo kwa nyumba za mtundu wakale zimene zinaperekedwa ku chipembedzo chosagwirizana ndi choonadi. Chimodzimodzi’nso, tsopano sitikuona amuna ndi akazi akuyenda-yenda atabvala zobvala zodabwitsa monga wansembe kapena kagulu ka atsogoleri achipembedzo, omafuna kuchitiridwa mwapadera ndi kuchitiridwa zabwino. Awo amene akuukitsidwa kuchokera kwa akufa sadzabwezeredwa ku ntchito zao zakale zachipembedzo, limodzi ndi kuyambiridwa’nso kwa chisokonezo ndi mkangano wachipembedzo. Amene adzakhala atatha adzakhala malo ao antchito olemekezeka’wo amene anawakweza pa anthu wamba amene iwo anawakhalira ndi malo a ntchito m’mphala zachipembedzo. Chipulumutso cha munthu wamba, mwamuna wamba, mkazi ndi mwana chinali kulingaliridwa kukhala chodalira pa mautumiki a anthu olemekezeka amene’wo. Koma tsopano boma la dziko lonse lapatsidwa ulamuliro wa kusamalira chipulumutso chamuyaya cha nzika zake za pa dziko lapansi m’thanzi lokwanira ndi chimwemwe pa dziko lapansi Laparadaiso. Kukhoza kwa boma’lo kuchotsa zofooka za thupi ndipo ngakhale kuukitsa akufa kukutsimikizira cheni-cheni chimene’cho. N’kwachibadwa kwa anthu kulambira kanthu kena, ndipo boma la dziko lonse likukwaniritsa chifuno chimene’cho mwa kuphunzitsa nzika zake kulambira koyera kumene kuli kochirikiza moyo.

MALO A BOMA LA DZIKO LONSE

17. Mosasamala kanthu za malo ake, kodi ndi motani m’mene boma’lo limatsimikizirira kukhala leni-leni?

17 Pofikira pa tsopano lino tingakhale tikudabwa, kuti, Kodi n’kuti pa dziko lapansi kumene kuli malikulu a boma la dziko lonse limene’li? Kuli konse kumene tingayang’ane pa dziko lapansi, sitikuwapeza. Ayenera kukhala kwina kwake. Inde, koma osati pano pa dziko lapansi. Ndipo moyenerera choncho! Boma la dziko lonse limene lingachite zinthu zazikulu zopindulitsa kosatha kwa nzika zake zotero’zo liri lapamwamba kwambiri koposa mtundu wina uli wonse wa boma laumunthu limene lalamulirapo pa dziko lapansi. Kuyerekezera kumene’ku kuli chikhalirebe choncho m’nyengo yathu ya sayansi yamakono, luso la zopanga-panga, mankhwala opititsidwa patsogolo, ulimi wochititidwa ndi makina ndi mphamvu ya nyuklea. Boma la dziko lonse limene likatamandidwa chifukwa cha ntchito zonse zodabwitsa zolongosoledwa poyambapo limasonyeza kuti liri ndi mphamvu yoposa yaumunthu, inde, maluso auzimu. Iro likudzisonyeza kukhala loposa boma lopangidwa ndi anthu. Pano pa dziko lapansi, pakati pa anthu, chifukwa cha chimene’cho sindiwo malo ofuna-funako malo ake. Malo ake ayenera kukhala apamwamba kwambiri koposa pa dziko lapansi. Ayenera kukhala pamwamba pathu, kumwamba. Ndicho chifukwa chake ali osaoneka kwa ife pano pa dziko lapansi. Koma mwa zabwino zonse zimene iro limachitira nzika zake za pa dziko lapansi, limadzisonyeza kukhala leni-leni, lokhalako’di!

18. Kodi kukhala kwake lakumwamba kuli ndi chiyambukiro chotani pa nzika zake?

18 Cheni-cheni nchakuti boma la dziko lonse’lo liri lokwezeka’di kopambana pa nzika zake za pa dziko lapansi chimatumikira kuonjezera kulilemekeza kwa munthu. Malamulo ake amalingaliridwa mwamphamvu ndi munthu wa pa dziko lapansi. Kuyenera kwa ulamuliro wake pa dziko lonse lapansi kukuzindikiridwa, chifukwa cha chimene’cho kugonjeredwa m’njira yodzichepetsa. Nzeru yake ikuonedwa kukhala yapamwamba kwambiri koposa ya ulamuliro uli wonse wa pa dziko lapansi m’mbiri yaumunthu. Iro liri ndi chikondwerero chopanda dyera mwa nzika zake za pa dziko lapansi. Chotero kuyendetsa kwake zochitika za anthu kuli kwabwino kwambiri koposa kochitidwa ndi boma liri lonse la padziko lapansi m’kati mwa zaka zikwi zisanu ndi chimodzi zapita’zo za mbiri ya anthu.

19. (a) Kodi n’chifukwa ninji a pa dziko lapansife tikuzungulira Mlengi wa chilengedwe chonse? (b) Kodi n’chifukwa ninji angatikhazikitsire boma la dziko lonse?

19 Tsono, kodi kuyenera kuonekera kukhala kodabwitsa kuti boma la dziko lonse’lo liri lakumwamba? Ai; pakuti tiyenera kukumbukira kuti munthu sindiye mfumu ya zonse zimene amafufuza. Planeti la munthu Dziko Lapansi sindiro pa phata la chilengedwe chonse, koma Mlengi wake wakumwamba ndiye. Monga planeti, iro limazungulira pa phata looneka, ndiko kuti, dzuwa, limene liri kutali mamailo okwanira mamiliyoni makumi asanu ndi anai mphambu atatu. Dziko lathu lapansi’li ndi dzuwa lake ziri mbali ya Mlalang’amba ndipo, monga zotero, zikuzungulira mwapang’ono-pang’ono pa malo ake ozungulirapo a khamu la nyenyezi lalikulu limodzi-modzi’li lopangidwa ndi nyenyezi zowala kwambiri mabiliyoni ochuluka. Pamenepa, moyenerera, ife amene tikukhala pa dziko lapansi timapezeka’nso tikuzungulira Mlengi wathu wakumwamba wa dziko lathu lapansi’li, wa maplaneti athu ozungulira dzuwa, wa Mlalang’amba wathu wa nyenyezi zambiri, inde, wa makamu onse a nyenyezi amene ali odziwika kwa openda nyenyezi amakono mwa njira ya makina oonera zinthu zakutali amphamvu kopambana. Ngakhale m’lingaliro lakuthupi ife okhala pa dziko lapansi laling’ono’lo tikulamulidwa ndi kutsogozedwa ndi malamulo akuthupi a chilengedwe chaponse-ponse. Nanga, n’chifukwa ninji ali yense ayenera kukaikira, kuti Wopanga malamulo onse akuthupi amene’wo amene amachititsa chilengedwe chachikulu kwambiri’cho kukhala chogwirizana modabwitsa ndi cha umodzi motero ali wokhoza kukhazikitsa boma labwino kopambana kaamba ka mtundu wonse wa anthu?

20. (a) Kodi n’chifukwa ninji kuli kofunika kuti ulamuliro wotsatirapo wa munthu ukhale boma la dziko lonse umene’wo? (b) Kodi n’chiani chimene chiri chifuno chake chachikulu?

20 Ulamuliro wotsatirapo wa dziko lonse lapansi ukanapanda kukhala boma la dziko lonse lokhazikitsidwa ndi Mlengi wa makamu onse a nyenyezi zakumwamba ndi wa ife pa dziko lapansi panso, banja lonse laumunthu likanakhala loyenera kufafanizidwa kwamuyaya. Ulamuliro wotsatirapo ufunikira kukhala, uyenera kukhala’di, uja wa Mlengi wa chilengedwe chonse, kapena apo phuluzi chiri chonse chidzatitayikira. Ha, ndi okondwa chotani nanga m’mene tingakhalire kuti udzatsimikizira kukhala Boma lolonjezedwa kwa nthawi yaitali lochokera kwa Iye! Boma liri lonse limene linakhalapo linali ndi chifuno kaamba ka kukhazikitsidwa ndi kugwira ntchito kwake. Boma la dziko lonse likudza’lo, nalo’nso, liri ndi chifuno, chifuno chaulemerero kopambana zifuno zonse. Choyamba lidzatsimikizira kwa munthu pa dziko lapansi kuti pali Mulungu waluntha, wa nzeru zonse, wa mphamvu zonse, wa chilungamo chonse ndi wachikondi mwangwiro, Mlengi ndi Mfumu ya chilengedwe chonse. Umboni wa chimene’cho, kutsimikiziridwa kwa zimene’zo, n’zofunika kopambana, pakuti zinthu zonse kuli konse, zamoyo ndi zopanda moyo, zooneka ndi zosaoneka, zimadalira pa Iye; izo zinakhalako ndipo zikusungidwa ndi Iye.

21. Kodi n’chiani chimene chiri chifuno chachiwiri cha boma limene’li, ndipo chifukwa ninji?

21 Chifuno chachiwiri cha boma la dziko lonse likudza’lo ndicho kulanditsa mtundu wa anthu ku chotulukapo chotsirizira cha kuipa konse, ndiko kuti, imfa, inde, chionongeko chosatha. Osati kuti anthu ang’onofe tiri ofunika kwambiri kwa Mulungu, sikuti iye sizikanamuyendera bwino popanda ife pa dziko lapansi. Iye akanatha kukhala mosabvuta, koma sakufuna kutero. Chifukwa ninji? Zonse’zo chifukwa chakuti iye amakonda tonsefe monga zolengedwa zake, ntchito ya manja ake, ndipo anatipanga kuti tikhale achimwemwe kotheratu mwa iye monga Atate wathu wakumwamba ndi kukhala ulemu kwa iye.

22. Chotero, kodi ife tiri okondweretsedwa kudziwa chiani, limodzi ndi phindu lotani?

22 Kodi zimene’zo siziyenera kutipangitsa kufuna boma la dziko lonse la Mulungu kukhala ulamuliro wotsatirapo wa dziko lonse lapansi? Tonsefe amene mitima yathu sinaumitsidwe ndi kuipidwa ndi kuipa konse kwa chitaganya cha anthu ochimwa tiyenera kukondwera mu mtima mpaka kufika pa kunena kuti Inde! Ife amene mitima yathu ikulabadirabe zisonyezero za chisomo cha chikondi chaumulungu tidzakhala okondweretsedwa kwambiri kudziwa zitsimikiziristo zochokera kwa Iye zimene tiri nazo kaamba ka kum’yembekezera kudzetsa boma la dziko lonse lolungama limene’li. Ndipo’nso, kodi n’chifukwa ninji, Iye adzachita zimene’zi m’kati mwa mbadwo wathu? N’zotsimikizirika’di kuti kulandira kwathu chidziwitso chimene’chi chonena za Iye ndi chifuno chake chaufulu kudzathandizira kupeza kwathu moyo wosatha mu unansi wodalitsidwa ndi boma la dziko lonse likudza’lo.

[Chithunzi patsamba 4]

IGUPTO

ASURI

BABULO

AMEDI NDI APERISI

GRISI

ROMA

BRITAIN NDI AMEREKA

MITUNDU YOGWIRIZANA

UFUMU WA MULUNGU

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena