Mutu 15
Kukhala Nzika ya Boma la Mulungu
1, 2. Kodi nchiyani chimene chikufunika kuti mukhale nzika ya boma la Mulungu?
KODI MUKUFUNA kukhala ndi moyo kosatha padziko lapansi pa boma la Mulungu? Munthu aliyense woganiza bwino akayankha kuti, Inde! Mapindu odabwitsa adzalandiridwa. Koma kuti muwalandire inu simungangotukula dzanja lanu ndi kuti: ‘Ndikufuna kukhala nzika ya boma la Mulungu.’ Zambiri zikufunika.
2 Mwa chitsanzo, tinene kuti munafuna kukhala nzika ya dziko lina. Kuti mutero, mukafunikira kukwaniritsa zofunika zoperekedwa ndi olamulira a boma la dziko limenelo. Koma musanachite zimenezi, mukanafunikira kuphunzira chimene zofunika zimenezi ziri. M’njira yofananayo, mufunikira kuphunzira chimene Mulungu amafuna kwa awo amene akufuna kukhala nzika za boma lake. Ndiyeno mufunukira kukwaniritsa zofunika zimenezi.
CHIDZIWITSO CHIKUFUNIKA
3. Kodi chofunika chimodzi cha kukhala nzika ya boma la Mulungu nchiyani?
3 Chofunika chachikulu kwambiri cha kukhala nzika ya boma la Mulungu ndicho kupezedwa kwa chidziwitso cha “chinenero” chake. Ndithudi kumeneku nkoyenera. Maboma ena aanthu amafunanso kuti nzika zatsopano zikhale zokhoza kulankhula chinenero cha dziko lawo. Chabwino, pamenepa, kodi ndi“chinenero” chotani chimene awo amene adzalandira moyo pansi pa boma la Mulungu ayenera kuphunzira?
4. Kodi “chinenero choyera” chimene anthu a Mulungu ayenera kuphunzira nchiyani?
4 Wonani zimene Yehova akunena ponena za zimenezi m’Mawu ake, Baibulo: “Pakuti pamenepo ndidzapereka kwa anthu kusinthira ku chinenero choyera, kuti iwo onse aitanire pa dzina la Yehova, kuti amtumikire mogwirizana.” (Zefaniya 3:9, NW) “Chinenero choyera” chimenechi ndicho chowonadi cha Mulungu chopezeka m’Baibulo. Kwenikweni, ndicho chowonadi chonena za boma Laufumu la Mulungu. Motero kuti mukhale nzika ya boma la Mulungu, muyenera kuphunzira “chinenero” chimenechi mwa kulandira chidziwitso cha Yehova ndi kakonzedwe kake Kaufumu.—Akolose 1:9, 10; Miyambo 2:1-5.
5. (a) Kodi tiyenera kudziwanji ponena za boma la Mulungu? (b) Kodi tikufunikira chidziwitso chotani kuti tipeze moyo wosatha?
5 Lerolino maboma ena aanthu amafuna kuti awo amene akulandira unzika adziwe kanthu kena ponena za mbiri ya boma lawo, kuphatikizapo zenizeni zonena za kugwira kwake ntchito. Momwemonso, inu muyenera kudziwa zinthu zoterozo ponena za boma la Mulungu ngati muti mukhakke nzika yake. Chidziwitso chimenechi chingatsogolere ku moyo wamuyaya. M’pemphero kwa Atate wake, Yesu anati: “Izi zitanthauza moyo wosatha, kulandira kwawo chidziwitso cha inu, Mulungu wowona yekha, ndi cha iye amene munamtuma, Yesu Kristu.”—Yohane 17:3, NW.
6. (a) Kodi ndimafunso ena otani amene nzika za boma la Mulungu ziyenera kukhala zokhoza kuyankha? (b) Kodi mungawayankhe?
6 Ngati mwaphunzira mitu yapitayo ya bukhu lino, pofika tsopano muyenera kukhala mutalandira chochuluka cha chidziwitso chofunika kwambiri chimenechi. Kodi mwatero? Kodi mungasonyeze kuti mwatero, mwa kuyankha mafunso onga otsatirapowo: Kodi ndiliti pamene Mulungu choyamba anatchula chifuno chake cha boma Laufumu? Kodi ndani amene anali ena a atumiki a Mulungu amene anayembekezera kudzakhala nzika zake zapadziko lapansi? Kodi boma la Mulungu lidzakhala ndi olamulira, kapena mafumu, angati? Kodi mafumu amenewa adzalamulira ali kuti? Kodi ndani anali oyambirira kusankhidwa kukhala mafumu m’boma la Mulungu? Kodi ndimotani mmene Yesu anasonyezera kuti iye akakhala mfumu yabwino? Komabe, kuti mukhale nzika ya boma la Mulungu, zambiri zikufunika koposa chabe kukhala ndi chidziwitso chonena za ilo.
KHALIDWE LOLUNGAMA LIKUFUNIKA
7. Ponena za maboma aanthu, kodi zofunika za unzika zimasiyana motani?
7 Maboma lerolino amafuna kuti nzika zatsopano zikwaniritse muyezo wina wa khalidwe. Mwa chitsanzo, iwo anganene kuti mwamuna angakhale ndi mkazi mmodzi yekha ndipo mkazi mwamuna mmodzi yekha. Komabe maboma enanso ali ndi malamulo osiyana. Iwo amalola nzika zawo kukhala ndi akazi ambiri. Kodi ndikhalidwe lotani limene likuyembekezeredwa kwa anthu amene akufuna kukhala nzika za boma la Mulungu? Kodi nchiyani chimene Mulungu amanena kuti nchabwino ponena za ukwati?
8. (a) Kodi muyezo wa Mulungu wa ukwati ndiwotani? (b) Kodi chigololo nchiyani, ndipo kodi Mulungu amanenanji ponena za icho?
8 Pachiyambi Yehova anakhazikitsa muyeso wa ukwati pamene anapatsa Adamu mkazi mmodzi yekha. Mulungu anati: “Mwamuna adzasiya atate wake ndi amake nadzadziphatika kwa mkazi wake: ndipo adzakhala thupi limodzi.” (Genesis 2:21-24) Yesu anafotokoza kuti umenewu ndiwo muyezo woyenera kwa Akristu. (Mateyu 19:4-6) Popeza kuti okwatirana akhale “thupi limodzi,” iwo amanyoza ukwati ngati iwo agonana ndi munthu winanso. Kachitidwe kameneka kamatchedwa chigololo, ndipo Mulungu amanena kuti adzalanga achigololo.—Ahebri 13:4; Malaki 3:5.
9. (a) Kodi lingaliro la Mulungu nlotani ponena za anthu ogonana pamene iwo sanakwatirane? (b) Kodi dama nchiyani?
9 Ndiponso, amuna ndi akazi ambiri amakhalira limodzi ndi kukhala malo amodzi, koma iwo samakwatirana. Komabe, Mulungu sanatanthauze kuti unansi wathithithi umenewu pakati pa mwamuna ndi mkazi ukhale pa maziko oyesa. Motero kukhalira limodzi osakwatirana ndiko tchimo lochimwira Mulungu, amene anapanga kakonzedwe kaukwati. Limatchedwa dama. Dama ndilo kugonana ndi munthu aliyense amene sunakwatirane naye. Ndipo Baibulo limati: “Ichi ndichifuniro cha Mulungu,. . . kuti mudzipatule kudama.” (1 Atesalonika 4:3-5) Chotero, pamenepa, kugonana kwa mbeta ndi aliyense nkolakwa.
10. Kodi ndimachitidwe ena otani akugonana amene ali otsutsidwa ndi malamulo a Mulungu?
10 Lerolino amuna ndi akazi ambiri amachita machitidwe akugonana ndi anthu ofanana nawo—amuna ndi amuna anzawo ndipo akazi ndi akazi anzawo. Anthu oterowo amatchedwa ogonana okhaokha. Nthawi zina akazi ogonana okhaokha amatchedwa m’Chingelezi Lesbians. Koma Mawu a Mulungu amanena kuti zimene iwo akuchita nzolakwa, kuti ndizo ‘zamanyazi.’ (Aroma 1:26, 27) Ndiponso, nkotsutsana ndi lamulo la Mulungu kwa munthu kugonana ndi nyama. (Levitiko 18:23) Aliyense amene akufuna kukhala ndi moyo pansi pa boma la Mulungu afunikira kutalikirana ndi machitidwe oipa amenewa.
11. (a) Kodi lingaliro la Mulungu nlotani ponena za kugwiritsiridwa nchito kwa zakumwa zoledzeretsa? (b) Awo amene akufuna kukhala nzika za boma la Mulungu ayenera kutalikirana ndi machitidwe otani amene ali ovulaza ku thanzi?
11 Kumwedwa kwa vinyo, mowa kapena kachasu kosapambanitsa sikotsutsana ndi lamulo la Mulungu. Kunena zowona, Baibulo limasonyeza kuti vinyo pang’ono angakhale bwino kaamba ka thanzi la munthu. (Salmo 104:15; 1 Timoteo 5:23) Koma nkotsutsana ndi lamulo la Mulungu kuledzera, kapena kuchita nawo mapwando aphokoso pa amene anthu amachita khalidwe loipa. (Aefeso 5:18; 1 Petro 4:3, 4) Kuphatikiza pa kugwiritsira ntchito zakumwa zoledzeretsa kuti aledzere kapena “kusangalala,” anthu ambiri lerolino amagwiritsira ntchito mankhwala osiyanasiyana kaamba ka chifuno chimodzimodzichi. Ndiponso, kaamba ka chikondwerero iwo angasute chamba kapena fodya, pamenenso ena angatafune mtedza wa betel kapena masamba a koka. Koma zinthu zimenezi zimaipitsa matupi awo ndi kuwononga thanzi lawo. Motero ngati mufuna kukhala nzika ya boma la Mulungu, muyenera kutalikirana ndi zinthu zovulaza zimenezi.—2 Akorinto 7:1.
12. (a) Kodi machitidwe ena osawona mtima ndiotani amene ali otsutsidwa ndi malamulo a Mulungu? (b) Kodi ndi motani mmene munthu amene amachita machitidwe amenewa angapezere chiyanjo cha Mulungu?
12 Nkwachiwonekere kuti maboma aanthu samafuna apandu kukhala nzika zatsopano. Ndipo Yehova ali ndi miyezo yokwererapodi. Iye amafuna kuti ife “tidzisungire mowona mtima m’zinthu zonse.” (Ahebri 13:18, NW) Ngati anthu sasunga malamulo a Mulungu, sadzaloledwa kukhala muufumu wake. Lerolino anthu kawirikawiri amayerekezera kukhala owona mtima, koma iwo amaswa malamulo ambiri. Komabe, Mulungu angawone zinthu zonse. Palibe angamgwire kumaso. (Ahebri 4:13; Miyambo 15:3; Agalatiya 6:7, 8) Motero Yehova adzatsimikizira kuti anthu amene akuswa malamulo ake, monga ngati malamulo aja oletsa kunama ndi kuba, sadzakhala nzika za boma lake. (Aefeso 4:25, 28; Chivumbulutso 21:8) Komabe Mulungu ngwodekha ndi wokhulupirika. Motero ngati wochita choipa aleka machitidwe ake oipa natembenukira ku kuchita zabwino, Mulungu adzamlandira.—Yesaya 55:7.
13.Kodi atumiki a Mulungu ayenera kukhala ndi lingaliro lotani ku malamulo a maboma aanthu?
13 Koma bwanji ponena za kusunga malamulo a maboma aanthu? Malinga ngati maboma aanthu alipo, Mulungu amafuna kuti atumiki ake agonjere “maulamuliro aakulu” amenewa. Misonkho iyenera kuperekedwa kwa iwo, ngakhale kuli kwakuti misonkhoyo njaikulu ndipo munthu sangavomerezane ndi njira mu imene ndalama zamsonkho zimagwiritsidwira ntchito. Ndiponso, malamulo a boma ayenera kumveredwa. (Aroma 13:1, 7; Tito 3:1) Chopatulidwapo chokha ku zimenezi chikakhala pamene kumvera lamulo kukachititsa munthu kusamvera lamulo la Mulungu. Zitatero, monga momwe Petro ndi atumwi ena ananenera, “Tiyenera kumvera Mulungu monga wolamulira koposa anthu.”—Machitidwe 5:29, NW.
14. Kodi tingasonyeze motani kuti tiri ndi lingaliro la Mulungu la mtengo wa moyo?
14 Mulungu amaika mtengo waukulu pa moyo. Awoa amene akufuna kukhala nzika za boma lake ayenera kuzindikira zimenezi. Mwachiwonekere, mbanda njotsutsidwa ndi lamulo la Mulungu. Koma udani kawirikawiri umatsogolera ku mbanda, ndipo ngakhale ngati munthu wina apitiriza kuda munthu mnzake iye sangakhale nzika ya boma la Mulungu. (1 Yohane 3:15) Chifukwa cha chimenecho, nkofunika kwambiri, kugwiritsira ntchito chimene chikunenedwa m’Baibulo pa Yesaya 2:4 ponena za kusanyamula zida zankhondo kukapha anansi athu. Mawu a Mulungu amsonyeza kuti ngakhale moyo wa mwana wosabadwa m’mimba mwa amayi wake ngwamtengo wapatali kwa Yehova. (Eksodo 21:22, 23; Salmo 127:3) Ndipo komabe kutaya mimba mamiliyoni ambiri kumachitidwa chaka chirichonse. Kupha moyo kumeneku nkotsutsidwa ndi lamulo la Mulungu, chifukwa chakuti munthuyo m’mimba mwa amayi wake ndimunthu wamoyo ndipo sayenera kuphedwa.
15. Kodi ndimalamulo otani a Mfumu ya Mulungu amene nzika zonse Zaufumu ziyenera kumvera?
15 Komabe, ponena za awo amene akakhala nzika za boma la Mulungu, zambiri zikufunika koposa chabe kusachita chimene chiri cholakwa kapena choipa. Iwo ayeneranso kupanga kuyesayesa kwenikweni kuchitira ena zinthu zokoma mtima ndi zopanda dyera. Iwo ayenera kutsatira lamulo laumulungu loperekedwa ndi Mfumuyo, Yesu Kristu: “Chifukwa chake zinthu zirizonse mukafuna kuti anthu achitire inu, inunso muwachitire iwo zotero.” (Mateyu 7:12) Kristu anapereka chitsanzo m’kusonyeza chikondi kwa ena. Iye anaperekadi moyo wake kaamba ka anthu, nalamulira atsatiri ake kuti: “Mukondane wina ndi mnzake; monga ndakonda inu.” (Yohane 13:34; 1 Yohane 3:16) Ndiwo mtundu umenewu wa chikondi chopanda mpeni kumphasa ndi nkhawa kaamba ka ena umene udzapangitsa kukhala ndi moyo kukhala chikondwerero chenicheni mkati mwa ulamuliro wa ufumu wa Mulungu.—Yakobo 2:8.
16, 17. (a) Kodi pali zifukwa zabwino zotani zopangira masinthidwe m’moyo wathu kuti tikwaniritse zofuna za Mulungu? (b) Kodi nchifukwa ninji tingakhalire otsimikiza kuti tingapange masinthidwe alionse ofunika?
16 Baibulo limasonyeza kuti anthu ayenera kupanga masinthidwe m’moyo wawo kuti akwaniritse zofunika za kukhala nzika za boma la Mulungu. (Aefeso 4:20-24) Kodi mukuyesayesa kupanga masinthidwe amenewa? Ndithudi nkoyenerera kuyesayesa kulikonse kutero! Kodi nchifukwa ninji ziri choncho? Sikudzatanthauza kuti inu mudzangokhala ndi moyo wabwino kwa zaka zoworengeka mkati mwa boma lina laanthu. Ayi, koma mudzalandira moyo wosatha m’thanzi langwiro padziko lapansi laparadaiso pansi pa boma lolamuliridwa ndi Mulungu!
17 Ngakhale tsopano, mwa kukwaniritsa zofuna za Mulungu, mudzakhala ndi moyo wosangalala kwambiri. Koma mungafunikire kupanga masinthidwe. Eya, anthu ambirimbiri, amene anali audani kapena aumbombo asintha. Ndiponso, adama, achigololo, ogonana okhaokha, zidakwa, mbanda, mbala, omwerekera ndi mankhwala ndi ogwiritsira ntchito fodya asintha kakhalidwe kawo. Iwo atero mwa kuyesayesa kwenikweni ndi mwa chithandizo cha Mulungu. (1 Akorinto 6:9-11; Akolose 3:5-9) Motero ngati muli ndi masinthidwe ovuta oti mupange kuti mukwaniritse zofuna za Mulungu, musaleke. Mungawachite!
KUKHULUPIRIKA KU BOMA LA MULUNGU
18. Kodi ndim’njira yapadera yotani imene Mulungu amatiyembekezera kusonyeza chichirikizo chathu chokhulupirika kaamba ka ufumu wake?
18 Zakuti Yehova Mulungu akafuna nzika zake kuchirikiza boma lake Laufumu mokhulupirika siziyenera kukhala zodabwitsa. Maboma aanthu amafuna chinthu chimodzimodzicho kwa nzika zawo. Koma kodi ndi m’njira yapadera yotani imene Mulungu amayembekezera chichirikizo chokhulupirika kuti chiperekedwe? Mwa njira ya kunyamula zida zankhondo kwa nzika zake kukamenyera ufumu wake? Ayi. M’malo mwake, mofanana ndi Yesu Kristu ndi atsatiri ake oyambirira, iwo ayenera kukhala alengezi kapena abukitsi aufumu wa Mulungu okhulupirika. (Mateyu 4:17; 10:5-7; 24:14) Ndichifuniro cha Yehova kuti aliyense akadziwe chimene ufumu wake uli ndi mmene udzathetsera mavuto aanthu. Kodi mwauza achibale, mabwenzi ndi ena zinthu zimene mwaphunzira m’Mawu a Mulungu? Ndichifuniro cha Mulungu kuti mutero.—Aroma 10:10; 1 Petro 3:15.
19. (a) Kodi nchifukwa ninji tingayembekezere chitsutso pamene tilankhula ndi ena ponena za ufumu wa Mulungu? (b) Kodi muyenera kuyankha mafunso otani?
19 Kristu ndi atsatiri ake oyambirira anafunikira kulimba mtima kuti alankhule ndi ena za Ufumu, pakuti kawirikawiri iwo anapezana ndi chitsutso. (Machitidwe 5:41, 42) Zirinso chomwecho lerolino. Dziko lolamuliridwa ndi Mdyerekezi lino silikufuna kuti mbiri yabwino ya Ufumu ilalikidwe. Motero mafunso ndiwo: Kodi mukuima pati? Kodi mudzapereka chichirikizo chokhulupirika ku ufumu wa Mulungu? Chifuniro chake nchakuti umboni waukulu Waufumu uperekedwe mapeto asanadze. Kodi mudzakhala ndi mbali m’kuupereka?
[Chithunzi patsamba 128]
Awo amene akukhala nzika za boma la Mulungu ayenera kulidziwa
[Zithunzi patsamba 131]
Nzika za boma la Mulungu ziyenera kupewa machitidwe otsutsidwa ndi Mulungu
[Chithunzi patsamba 133]
Nzika za boma la Mulungu ziyenera kuuza ena za ilo