Mutu 12
M’mene Tingasangalalire ndi Boma la Dziko Kosatha
1. Pansi pa “Miyamba yatsopano” kodi n’chiani chimene chidzaphuka pa dziko lapansi?
BOMA LA DZIKO lolamulidwa ndi Mlengi wa kumwamba ndi dziko lapansi lidzakhala kanthu kosangalala nako kosatha. Iro lidzakhalapo kwa nthawi zonse ndipo lidzasamalira kosatha zochita za mtundu wa anthu bwino lomwe. Mitambo ya mkuntho wa ‘nthawi ya nsautso” yaikulu kopambana ya mtundu wa anthu itakanganuka, boma la dziko la Yehova Mulung lokhala m’manja mwa Kristu limene’li lidzakhala “miyamba yatsopano” imene idzakuta mokondweretsa dziko lonse lapansi. Pa dziko lapansi chitaganya chatsopano ndi cholungama cha anthu chidzabuka chimene chidzalabadira mogwirizana ku “miyamba yatsopano” ya boma. Njira yomkera ku Paradaiso idzakhala itatsegulidwa!
2. Kodi ndi funso lotani limene tingadzifunse ponena za kukhala mboni zoona ndi maso?
2 Tangoziganizirani: Payenera kukhala mboni zoona ndi maso za kukhazikitsidwa kwa miyamba yatsopano” mu imene mudzakhala chilungamo. Kodi mboni zoona ndi maso zimene’zi zidzaphatikizamo ife? Tingadzifunse moyenerera funso limene’lo, pakuti Baibulo limatitsimikizira kuti padzakhala opulumuka opanda chiwerengero chochulidwa amene adzakhala ali pano pa dziko lapansi kuti adzatamande ndi chisangalalo kuyambitsidwa konse pa dziko lapansi lopanda anthu. Kuyambira pa chiyambi pomwe pa ulamuliro wao wolungama iwo adzakhala nzika zofunitsitsa za pano pa dziko lapansi loyeretsedwa. Mwa kukoma mtima kosakuyenerera kwa Mlengi wa “miyamba yatsopano ndi dziko lapansi latsopano,” otsalira a abale” auzimu a Kristu ndi “khamu lalikulu” losawerengeka la awo amene anathandiza ndi kuchirikiza “abale” a Kristu adzakhala ndi chokumana nacho chotero’cho chofanana ndi cha mtumwi Yohane. Maso ao adzatsegulidwa, monga momwe anachitira a Yohane, poona masomphenya za amene iye anati: “Ndipo ndinaona m’mwamba mwatsopano ndi dziko [lapansi] latsopano; pakuti m’mwamba moyamba ndi dziko [lapansi] loyamba zidachoka, ndipo kulibe’nso nyanja.”—Chibvumbulutso 21:1; Yesaya 65:17.
3. Kodi ndi m’njira yotani kudzakhala kwakuti “kulibe’nso nyanja”?
3 Chiani? Kodi nyanja zathu zisanu ndi ziwiri zidzachititsidwa kuphwera m’kati mwa “tsiku la Yehova” lamoto’lo ndi kusakhalako’nso? Mosangalatsa ai! Yohane akunena za “nyanja” yophiphiritsira. Chifukwa cha chimene’cho, pamenepa, m’nthawi yokwanira, otsalira ndi “khamu lalikulu” la opulumuka anzao adzayang’ana pa dziko lapansi latsopano’lo, sadzaona pa dziko lapansi loyeretsedwa’lo kuli konse kupanda mpumulo kuli konse, kusakhutira, chitaganya chachipolowe chosonyeza kutsutsa boma la dziko lokhazikitsidwa la Mulungu. “Dziko la anthu opanda umulungu” lidzakhala litaumitsidwa, litafafanizidwa, kuchotsedwa m’kati mwa “chisautso chachikulu” chimene chidzakhala chitangotha kumene. “Nyanja” yotero’yo ya madzi oipitsidwa ndi okhala ndi litsiro sidzapulumuka tsiku la chiweruzo pa limene mkwiyo wa Yehova ukutsanulidwa ngati moto.—Chibvumbulutso 8:8, 9;10:2; 13:1; 16:3; 17:15; 2 Petro 2:5, NW; Yesaya 17:12; 57:20.
4. Kodi n’chinthu china chiani chimene chiyenera kuchotsedwa kuphatikiza pa “nyanja”?
4 Zinthu zaphokoso zimene’zo pa dziko lapansi zimene zakhala zikubangula motsutsa boma la dziko la Mulungu lokhala m’manja mwa kristu silidzakhala gulu lokha lotsutsa limene lidzachititsidwa kuleka kugwira ntchito. Gulu lina lotsutsa, lamphamvu’di kwambiri, lidzachotsedwa pafupi ndi dziko lathu lapansi’li. Kodi ndani amene ali otsirizira’wa? Chinjoka chophiphiritsira, Satana Mdierekezi, ndi angelo ake onse auchiwanda. Pambuyo pa nkhondo kumwamba imene inatsatirapo pa kubadwa kwa ufumu wa Mulungu Waumesiya pa mapeto a Nthawi za Akunja mu 1914, “wolamulira wa ziwanda” amene’yo, limodzi ndi magulu ake ankhondo a angelo auchiwanda, anagwetsedwa kuchokera kumwamba. Iwo anaponyeredwa kufupi ndi dziko lathu lapansi’li, kuti atsekerezedwe m’menemo kwa “kanthawi.” Mopsyera mtima kwambiri wom’ponya wake ndi kuletsedwa kwamuyaya kubwerera kumwamba, Chinjoka chauzimu chimene’chi, mofanana ndi Ng’ona yaikulu, chabvundula “nyanja” ya mtundu wa anthu wopanda mpumulo motsutsana ndi ufumu wa Mulungu wobadwa chatsopano’wo wokhala m’manja mwa Kristu ndi kulamuliro kwake kwa zaka chikwi.—Chibvumbulutso 12:3-13; Yobu 41;1-32.
5, 6. (a) Kodi ndi liti ndipo ndi motani m’mene Satana ndi angelo auchiwanda adzatontholetsedwera? (b) Kodi “khamu lalikulu lidzapfuula mochirikiza chiani?
5 Chinjoka’cho, Satana Mdierekezi, ataona kuti atumiki ake a pa dziko lapansi agonjetsedwa mu “nkhondo ya tsiku lalikulu la Mulungu Wamphamvuyonse” pa Harmagedo, iye ndi magulu ake ankhondo osaoneka adzafika pa mapeto a “kanthawi’ kao. Ndiyeno chiani? M’kuoneratu kolosera kwa nyengo ya pambuyo pa nkhondo, mtumwi Yohane anaona kuti gulu lonse la ziwanda likuchotsedwa pafupi ndi dziko lathu lapansi’li ndi kuikidwa m’ndende, kumangidwa unyolo, m’phompho, pansi pa chizindikiro chimene sichinayenera kudulidwa kwa zaka chikwi. M’njira yotheratu imene’yi kumwamba ndi dziko lapansi lomwe zikuchotseredwa otsutsa onse oipa a boma la dziko la Yehova lokhala m’manja mwa Kristu. (Chibvumbulutso 16:14, 16, NW; 19:19) mpaka 20:3) Ha, ndi mkhalidwe woyenera chotani nanga umene tsopano wafunga kuli konse! Ha, ndi wosangalatsa chotani nanga m’mene moyo udzakhalira kwa ife ngati tidzitsimikizira kukhala mbali ya “khamu lalikulu” la opulumuka “chisautso chachikulu!” Satana Mdierekezi ndi onse amene amam’tsanzira m’kutokosa ulamuliro woyenera wa Mulungu wa kumwamba ndi dziko lapansi adzakhala atatontholetsedwa ndi kuchotsedwa. Mochirikiza ndi mtima wonse ulamuliro wa Yehova “khamu lalikulu” lidzaimirira pamaso pa mpando wake wachifumu ndi kupfuula kuti:
6 Chipulumutso kwa Mulungu wathu wakukhala pa mpando wachifumu, ndi kwa Mwanawankhosa.”—Chibvumbulutso 7:9, 10, 14, 15.
BOMA LA DZIKO LOPATSA MOYO
7. Chivumbulutso 21:2-5 chimasonyeza kuti boma la Mulungu likupatsa chiani mtundu wa anthu?
7 Chipulumutso kutuluka mu “chisautso chachikulu” chiri kanthu kena, kakakulu kopambana’di, koma moyo wamuyaya m’thanzi labwino ndi chisangalalo ndi china’nso, chachikulu koposa-posatu. Phindu lotsirizira’li ndiro limene boma la dziko laumulungu’lo lidzapatsa anthu okhala pa dziko lapansi. M’mau okongola kwambiri, mtumwi Yohane akutiuza za zimene’zi. Atatha kunena kuti pamenepo “kulibe’nso nyanja,” iye akuti, “ndipo ndinaona mzinda woyera’wo, Yerusalemu Watsopano, ulikutsika Kumwamba kwa Mulungu, wokonzeka ngati mkwatibwi wokometseredwamwamuna wake. Ndipo ndinamva mau akulu ochokera ku mpando wachifumu, [chifukwa cha chimene’cho mau a Mulungu], ndi kunena Taonani, chihema cha Mulungu [osati mpando wachifumu wa Mulungu] chiri mwa anthu; ndipo adzakhalitsa nao, ndi iwo adzakhala anthu ake, ndi Mulungu yekha adzakhala nao, Mulungu wao; ndipo adzawapukutira misozi yonse kuichotsa pamaso pao; ndipo sipadzakhala’nso imfa; ndipo sipadzakhala’nso malira, kapena kulira, kapena chowawitsa; zoyamba’zo [kuphitikizapo miyamba ndi dziko lapansi zakale] zapita. Ndipo Iye wakukhala pa mpando wachifumu [Mulungu] anati, Taonani, ndichita zonse zikhale zatsopano.”—Chibvumbulutso 21:2-5.
8. Kodi Yerusalemu Watsopano amaimira chiani ndipo kodi akudzetsera chiani anthu?
8 Mau’wo, “mzinda woyera’wo, Yerusalemu Watsopano,” amasonyeza boma, mongofanana ndi Yerusalemu wakale m’masiku a Mfumu Davide ndi mwana wake, Mfumu Solomo, anasonyeza boma, mafumu amene’wa akumanenedwa kukhala akukhala pa “mpando wachifumu wa Yehova” monga oimira ake. (1 Mbiri 29:23) Kodi boma lina liri lonse kufikira tsopano lakhala lokhoza kupatsa anthu pa dziko lapansi chimene Yerusalemu Watsopano adzapereka, kupukuta misozi yochititsidwa ndi masoka ndi zopweteketsa mtima, kuchotsedwa kwa imfa, kulira maliro, kulira ndi zowawa za mtima? Mkhalidwe wonse wa kulira maliro wa mtundu wa anthu kufikira tsopano ukuyankha kuti Ai! Koma Yerusalemu Watsopano angathe ndipo adzapereka madalitso amene’wo chifukwa chakuti ndiye boma lochokera kwa Mulungu. Mwana wokondedwa wa Mulungu, Yesu Kristu, analawa imfa yansembe kaamba ka mtundu wonse wa anthu kuchotsa pa ife kosatha imfa yacholowa. Kuti zimene’zo zichitike iye ayenera kulamulira kwa zaka chikwi.—1 Timoteo 2:5, 6; Ahebri 2:9; 1 Akorinto 15:24-27.
9. Kodi Yerusalemu Watsopano adzapangika ndi chiani?
9 Boma siliri chinthu choyenda chokha, chinthu choyambitsidwa kuyenda ndi kumayenda popanda wochiyendetsa. Kuti ligwire ntchito, limafunikira olamulira kapena akulu-akulu a boma. Pamenepo, kodi ndani, amene adzapanga Yerusalemu Watsopano woperekedwa ndi Mulungu’yo? Mngelo wa Mulungu analongosolera mtumwi Yohane kuti Yerusalemu Watsopano’yo ndiye “mkwatibwi, mkazi wa Mwanawankhosa.” Zimene’zo zimasonyeza kuti ndiye mpingo wa ophunzira 144,000 ndi olowa nyumba limodzi ndi Yesu Kristu Mwanawankhosa’yo, onse Aisrayeli auzimu. (Chibvumbulutso 21:9-14; 7:4-8; 14:1-4; 19:7,8; 2 Akorinto 11:2) Komabe, chifukwa chakuti kagulu ka Yerusalemu watsopano kakunenedwa kukhala mkwatibwi, mkazi, kagulu kamene’ka sikakunenedwa pano kukhala kakulamulira, koma ndiye Mkwati wake amene akulamulira.
10. Kodi ndi m’njira yotani Mulungu ndi Yesu akukhalira pa mpando wachifumu mu “mzinda’wo”?
10 Monga momwe’di “mpando wachifumu wa Yehova” unaliri mu Yerusalemu wakale wa pa dziko lapansi ndipo Mfumu Davide ndi mafumu olowa m’malo mwake anakhala pa mpando wachifumu umene’wo monga oimira ooneka a Yehova, chotero nkhani’yo pano iri yolingana ndi Yerusalemu Watsopano’yo. Timawerenga kuti: “Mpando wachifumu wa Mulungu ndi wa Mwanawankhosa udzakhala momwemo.” Ndiko kuchokera ku mpando wachifumu umene’wu kumene “mtsinje wa madzi a moyo ukutuluka kaamba ka moyo wamuyaya wa nzika za ufumu wa Mulungu wokhala m’manja mwa Kristu. (Chibvumbulutso 22:1,3) Chifukwa cha chimene’cho, mu Yerusalemu Watsopano Mwanawankhosa Yesu Kristu akukhala pa “mpando wachifumu wa Yehova” monga Mfumu Yaumesiya yoikidwa ndi Iye. Mbadwa yachifumu ya Mfumu Davide imene’yi ndi Solomo iri yaikulu koposa makolo ake amene’wa, pakuti ufumu wake uli wakumwamba ndipo udzakhala boma la dziko: “Adzachita ufumu kuchokera kunyanja kufikira kunyanja, ndi kuchokera ku Mtsinje [wa Firate] kufikira malekezero a dziko lapansi.” (Salmo 72:8) Ulamuliro wake udzakhala wa pa dziko lonse.—Zekariya 9:9, 10; Salmo 110:1, 2.
11. (a) Kodi ndi liti pamene kagulu ka Mkwatibwi kadzatsirizidwa ndipo motani? (b) Kodi Wolamulira wa Dziko, Yesu, akukhala chiani kwa nzika zake, ndipo pa maziko otani?
11 Pa nthawi yosasonyezedwa, otsalira a olowa nyumba anzake a Kristu adzachoka pa dziko lapansi ndipo, mwa njira ya “chiukiriro choyamba,” iwo adzagwirizana ndi Mkwati wao wakumwamba ndipo motero kagulu konse ka olowa nyumba 144,000 kadzatsirizidwa. (Chibvumbulutso 20:4, 6, NW) Koma “khamu lalikulu” la anzao onga anamwali lidzapitirizabe kukhala pano pa dziko lapansi monga nzika za Wolamulira wa Dziko, Yesu Kristu. (Salmo 45:14) Ngakhale kuli kwakuti adzakhala wolamulira wa dziko, iye adzakhala atate wao. Kwa nzika zake zokhulupirika iye adzakhala Atate wao Wosatha, pakuti iye anafera iwo onse kuti akakhale Wopatsa Moyo wao wosatha. Monga “Adamu wotsiriza,” iye anapangidwa kukhala “mzimu wopatsa moyo” kaamba ka iwo.—1 Akorinto 15:45; Yesaya 9:6, NW.
12. Kodi “khamu lalikulu” lidzadzigwiritsira ntchito ku chiani? Kuti?
12 Kukunenedwa ponena za “khamu lalikulu” kuti “iwo achapa miinjiro yao ndi kuiyeretsa m’mwazi wa Mwanawankhosa.” Chifukwa cha chimene’cho “Mwanawankhosa wa Mulungu” wa nsembe amene’yu amachita monga Mkulu wa Ansembe wa Mulungu pa kachisi wake Wauzimu. Pamenepa, moyenerera, kodi n’chiani chimene chiri chinthu choyambirira chimene “khamu lalikulu” la anthu ‘obvala miinjiro yoyera’wo’ lidzachita ‘litatuluka m’chisautso chachikulu’? Mofanana ndi Nowa ndi banja lake chitangopita Chigumula “khamu lalikulu” likudzipereka ku kulambiridwa kwa Yehova. “Chifukwa chake ali ku mpando wachifumu wa Mulungu; ndipo am’tumikira Iye usana ndi usiku m’kachisi mwake.” (Chibvumbulutso 7:9, 10, 14, 15; Yohane 1:29, 36) Iwo amadziwa kuti, pansi pa boma la dziko la Mulungu lokhala m’manja mwa Kristu, palibe mpangidwe wa kulambira umene udzaloledwa koma chipembedzo chimodzi choona, kulambiridwa koyera kwa Mulungu mmodzi wamoyo ndi woona, Yehova. Chimene’chi chidzakhala chipembedzo chimodzi chokha cha “dziko lapansi latsopano.” Chidzakhala magwero ogwirizanitsa kwa onse.
13. Kodi ndani pa dziko lapansi amene adzakhala ndi phande m’kupanga dziko lonse lapansi kukhala Paradaiso?
13 Kodi “khamu lalikulu” lopulumuka’lo lidzakhala anthu okha ogwiritsiridwa ntchito kusintha mpira wathu’wu dziko lapansi kukhala Paradaiso wokongola kopambana? Ai, koma anthu akufa oomboledwa, pambuyo pa chiukiriro chao, adzakhala ndi phande m’ntchito yosangalatsa imene’yi. Amene’wa adzaphatikizapo munthu womvera chisoni amene anafera pambali pa Yesu.—Luka 23:43, NW.
14. Kodi ndani amene adzagwiritsira ntchito “zofungulira za imfa ndi Hade”? Kaamba ka yani?
14 “Zofungulira za imfa ndi Hade [manda a onse a mtundu wa anthu]” ziyenera kugwiritsiridwa ntchito. Yesu Kristu wakhala nazo chiyambire pa chiukiriro chake. O, zosangalatsa, iye adzazigwiritsira ntchito kuukitsira awo onse amene nsembe yake ya dipo ikuwaphatikizamo! Ntchito zimene anthu oukitsidwa amene’wa akuchita m’kati mwa kulamulira kwake kwa zaka chikwi zidzakhala maziko a kuweruzidwa kwao. Awo otsimikizira kukhala osamvera mwadala ndi osakhoza kukonzeka adzataya kuyenera konse kwa moyo. Iwo adzalandira chilango cha imfa ku imene sadzaukitsidwa.—Chibvumbulutso 1:18; 20:11-15; Machitidwe 24:15; Yohane 5:28, 29.
15. Kodi ndi motani m’mene kuyeretseda kwa chilengedwe chonse kudzatsirizidwira?
15 Kuyeretsedwa kwa chilengedwa chonse potsirizira pake kudzatsirizidwa ndi kuonongedwa kwa Satana Mdierekezi ndi ziwanda zake, oyambitsa kuipa. (Chibvumbulutso 20:7-10; Genesis 3:15) Ha, ndi dalitso lotani nanga ku dziko lathu lapansi’li! Chochikongoletsa chidzakhala pa nthawi imene’yo dziko limodzi lolamulidwa ndi boma limodzi lokonda mokhulupirika ulamuliro woyenera wa Mulungu.
16, 17. Kodi kuyamikira kukoma mtima kwa Mulungu kumatisonkhezera kuchitanji?
16 O, ndi chiyembekezo chodalitsidwa chotani nanga chimene chiri pamaso pathu mothandizidwa ndi Mau a Mulungu! Mosaleka chimasonkhezera mitima yathu. O, pamenepa, tikuti mukulandiridwa ndi manja awiri, inu boma la dziko loyembekezeredwa kwa nthawi yaitali. “Chizindikiro” cha kuyandikira kwanu chaoneka patsogolo pathu ndipo chikukhala ndi tanthauzo moonjezereka-onjezereka. Chimene chiri choti ife n’kuchifikira mosabvuta ndicho makonzedwe achikondi akuti ife tisangalale ndi moyo wamuyaya pa dziko lapansi Laparadaiso pansi pa ulamuliro wanu woyenera. Mitima yathu, yochititsidwa kutentha ndi chiyamikiro, imatisonkhezera kulandira mwai wamtengo wapatali wotero’wo.
17 Tikuthokoza Mlengi wanu, Yehova, Wolenga kumwamba ndi dziko lapansi, tikudziwa tsopano zimene tingachite ‘m’chaka chino cha chiyanjo cha Yehova.’ (Yesaya 61:2; 49:8; 2 Akorinto 6:1, 2) Tiri ndi mwai wa kukhala ophunzira odzipereka ndi obatizidwa a Woimira Wamkulu wa Yehova kaamba ka kudalitsa mtundu wa anthu. (Mateyu 28:19, 20) Motsatira mapazi ake tidzapita patsogolo, tikumalengeza mosangalala kuli konse “mbiri yabwino imene’yi ya ufumu,” kufikira adani onse atagonjera ku chipambano chanu chaulemerero, O inu boma lathu la dziko likudza’lo, ufumu wa Mulungu.