Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • hs mutu 9 tsamba 163-183
  • Dongosolo latsopano Limene Likuchirikizidwa ndi Mzimu Woyera

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Dongosolo latsopano Limene Likuchirikizidwa ndi Mzimu Woyera
  • Mzimu Woyera—Mphamvu Yochirikiza Dongosolo Latsopano Likudza’lo!
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • CHIUKIRIRO CHATSOPANO
  • MZIMU UMACHIRIKIZA MFUMU YA MU MZERA WA DAVIDE
  • “DZIKO LAPANSI LATSOPANO”
  • ZIYEMBEKEZO ZA DONGOSOLO LATSOPANO!
  • M’mene Tingasangalalire ndi Boma la Dziko Kosatha
    Boma Lathu la Dziko Likudza’lo—Ufumu wa Mulungu
  • “Mzimu wa Moyo Wochokera kwa Mulungu Unawalowera”
    Mzimu Woyera—Mphamvu Yochirikiza Dongosolo Latsopano Likudza’lo!
  • Chiyembekezo cha Chiukiriro N’champhamvu
    Nsanja ya Olonda—2000
  • Zolengedwa Zatsopano Zipangidwa!
    Nsanja ya Olonda—1993
Onani Zambiri
Mzimu Woyera—Mphamvu Yochirikiza Dongosolo Latsopano Likudza’lo!
hs mutu 9 tsamba 163-183

Mutu 9

Dongosolo latsopano Limene Likuchirikizidwa ndi Mzimu Woyera

1. Mosasalala kanthu za Mlaliki 1:9, kodi n’chifukwa ninji dongosolo likudza’lo lochirikizidwa ndi mzimu woyera lidzakhala kanthu kena katsopano kwenikweni?

PAMENE tinena za dongosolo latsopano lirinkudza limene likuchirikizidwa ndi mzimu woyera, tinganene’di kuti: “Taonani; liri latsopano.” Ngakhale Mfumu yanzeru Solomo sidzakhala yokhoza kugwiritsirapo ntchito mau ake ofotokozedwa kuti: “Palibe kanthu katsopapo pansi pano.” (Mlakiki 1:9, 10) Mau a Solomo’wo atsimikizira kukhala oona kufikira tsopano ponena za mkhalidwe wa moyo wa mwamuna ndi mkazi ndi ponena za kubuka ndi kugwa kwa mabona opangidwa ndi anthu. Koma dongosolo la zinthu limene Mlengi wa kumwamba ndi dziko lapansi adzalidzetsa posachedwapa lidzakhala’di kanthu kena katsopano, kanthu kena kamene sikanaonedwe ndi kale lonse m’mbiri yonse ya anthu.

2. Kodi n’chifukwa ninji kuyenera kuyembekezeredwa kuti mzimu woyera udzakhala kutseri kwa dongosolo latsopano lolonjezedwa’lo?

2 Mzimu woyera udzakhala kutseri kwa dongosolo latsopano likudza’lo. Ndipo kodi ungalekerenji? Unali kutseri kwa kulembedwa kwa Baibulo Loyera, ndipo bukhu louziridwa limene’li ladzazidwa bwino lomwe ndi mbiri yabwino yonena za dongosolo latsopano lamtendere kaamba ka mtundu wa anthu wotopa ndi mabvuto’wo. Pamene potsirisira pake lidzetsedwa m’kati mwa mbadwo uno, onse olowa m’kusangalala nalo mokondwera adzanena kuti: “Iri ndi latsopano!” Mulungu wamphamvuyonse, Yehova, adzakwaniritsa lonjezo lake ku mtundu wa anthu lakuti: “Taonani, ndichita zonse zikhale zatsopano.—Chibvumbulutso 21:5.

3. (a) Kodi ndi zinthu zatsopano ziti zimene bukhu la Chibvumbulutso limazinena? (b) Kodi n’chifukwa ninji dongosolo latsopano la Mulungu silidzakhala kuikira chigamba?

3 Chibvumbulutso, bukhu lotsirira la Baibulo, limanene za zinthu zatsopano, “dzina latsopano,” “nyimbo yatsopano,” “m’mwamba mwatsopano ndi dziko [lapansi] latsopano,” ndi “Yerusalemu watsopano.” (Chibvumbulutso 2:17; 3:12; 5:9; 14:3; 21:1, 2) Zimene’zi ziri zinthu zosangalatsa zozilingalira ndi kuzilankhula. Ndipo pamene munthu azindikira mkhallidwe wa zinthu zatsopano zimene zasungidwira mtundu wa anthu, kumam’sonkhezera ‘kuyimbira Yehova nyimbo yatsopano.’ (Salmo 96:1; 98:1; 144:9; 149:1) Dongosolo lake latsopano silidzakhala chinthu choikiridwa chigamba, kukonzedwa kwa dongosolo lakale la mtundu wa anthu, kuyesa kusunga zochuluka monga momwe kungathekere za dongosolo lakale’li ndi kuonjezera chabe zokometsera zatsopano, motero kugwiritsira ntchito dongosolo lakale la anthu monga maziko. Zimene’zi sizidzagwira ntchito konse. Yesu Kristu iye mwini anati:

“Palibe munthu ang’amba chigamba cha maraya atsopano, nachiphatika pa maraya akale; chifukwa ngati atero, angong’ambitsa atsopano’wo, ndi chigamba cha atsopano’wo sichidzayenerana ndi akale’wo. Ndipo palibe munthu atsanulira vinyo watsopano m’matumba akale; chifukwa ngati atero, vinyo watsopano’yo adzaphulitsa matumba, ndipo amene’yo adzatayika, ndi matumba adzaonongeka. Koma kuyenera kutsanulira vinyo watsopano m’matumba atsopano.”—Luka 5:36-38.

4. Kodi n’chifukwa ninji Yerusalemu wakale womangidwa’nso sadzakhala ndi mbali m’Dongosolo Latsopano

4 Mogwirizana ndi fanizo limene’li, chimene Mulungu waneneratu kaamba ka mtundu wa anthu chidzakhala chatsopano kweni-kweni. Yerusalemu wakale m’Middle East sadzakhalamo ngati kanthu. Pamene Mulungu anapereka chiweruzo chake chachitsutso m’chaka cha 70 C.E., iye anachititsa Yerusalemu wa m’nthawi ya Yesu kuonongedwa. Yerusalemu amene wamangidwa kuyambira pa nthawi imne’yo sanamangidwe molamulidwa ndi Iye kapena’nso ndi anthu ake obvomerezeka (Yohane 4:21) Yerusalemu Watsopano ndiye chinthu’cho! Umene’wu sudzakhala mzinda wa kamangidwe ka pano pa dziko lapansi, pa malo a Yesusalemu wakale. Yerusalemu Watsopano adzakhala wakaumwamba. Zokha zimene tiyenera kuchita ndicho kupenda kulongosoledwa kwake monga momwe kwaperekedwera m’Chibvumbulutso 21:9 kufikira 22:3, ndipo tidzaona kuti, chifukwa cha maukulu ndi mbali zake, sangayenererane konse ndi malo a Yerusalemu wakale. Kalongosoledwe kouziridwa’ko, Yesusalemu Yerusalemu Watsopano akuchedwa “mkwatibwi, mkazi wa Mwanawankhosa.”

5. Kodi Yerusalemu watsopano akuyerekezeredwa ndi yani, ndipo kodi ndi motani m’mene kumene’ku kukufananira ndi kanenedwe ka Zekariya 9:9?

5 “Ndipo ndinaona,” akutero mtumwi Yohane, “mzinda woyera’wo, Yerusalemu wotsopano, ulikutsika Kumwamba kwa Mulungu, wokonzeka ngati mkwatibwi wokometsedwera mwamuna wake.” (Chibvumbulutso 21:2) Monga momwe’di pano Yerusalemu Watsopano’yo akuyerekezeredwera ndi mkazi, mkwatibwi, mkazi wokwatiwa, mofananamo Yerusalemu wakale anayerekezeredwa ndi mkazi. Mwa chitsanzo, pamene Yesu anakwera kulowa m’Yerusalemu pa Nisan 9 (March 27, 33 C.E., monga ngati kuti anali woyembekezeredwa: kukhala mfumu wokwera kumka ku kulongedwa kwake ufumu, ulosi wa Zekariya 9:9 unakwaniritsidwa: “Kondwera kwambiri, mwana wamkazi wa Ziyoni; pfuula mwana wamkazi wa Yerusalemu; taona, Mfumu yako ikudza kwa iwe; . . . wokwera pa buru, ndi mwana wamphongo wa buru.”—Mateyu 21:4, 5.

6. Kodi ndi motani m’mene Yerusalemu watsopano adzakhalira poyerekezeredwa ndi mzinda wakale ponena za kukongola, ndipo kodi ndi motani m’mene akutsikira kuchokera kumwamba nwa Mulungu?

6 Yerusalemu wa pa dziko lapansi wakale anali kuchedwa “mudzi wochedwa wokongola.” (Maliro 2:15; Salmo 48:1, 2; 50:2) Komabe, m’kukongola ndi ulemerero, sangalingane ndi Yerusalemu Watsopano wakumwamba. Mzinda waulemerero watsopano umene’wu ukutsika kuchokera “Kumwamba kwa Mulungu.” M’njira yotani? M’chakuti bungwe la boma latsopano limene’li likuchokera kwa Mulungu ndipo likufutukulira mphamvu ndi ulamuliro wake pansi pano kuchokera kumwamba kudza pa dziko lapansi, kaamba ka ubwino wa nthawi onse wa mtundu wa anthu.—Chibvumbulutso 21:2.

7. Kodi mzinda woyera’wo, Yerusalemu Watsopano. uli “mkazi wa Mwanawankhosa”m’jira yotani?

7 Kodi mzinda woyera’wo uli “mkwatibwi, mkazi wa Mwanawankhosa” m’njira yotani? M’chakuti uwo ndi wopangidwa ndi mpingo wa ophunzira a Kristu odzozedwa, olowa nyumba limodzi naye mu ufumu Waumesiya (Aefeso 5:25-27; 2 Akorinto 11:2; Chibvumbulutso 19:7, 8; 22:17) Ponena za ali yense wa amene’wa Yesu wolemekezedwa’yo anati: “Ndidzalemba pa iye dzina la Mulungu wanga, ndi dzina la Mzinda wa Mulungu wanga, la Yerusalemu watsopano, wotsika m’Mwamba, kuchokera kwa Mulungu wanga; ndi dzina langa latsopano” (Chibvumbulutso 3:12) Ziwalo za “mkwatibwi” ziri Aisrayeli auzimu, okhala m’pangano latsopano, ndipo iwo alipo okwanira 144,000. Yesu Kristu akuwamanga pa iye mwini monga “thanthwe,” ndipo atumwi ake khumi ndi awiri amayalidwa monga miyala ya maziko achiwiri pa iye.—Mateyu 16:18; Chibvumbulutso 7:4-8; 14:1-5; 21:14.

8. Kodi n’chifukwa ninji olowa nyumba a Kristu 144,000 adzakhala gulu la olamulira limene liri latsopano kotheratu?

8 Olowa nyumba 144,000 limodzi ndi Mkwati wakumwamba Yesu Kristu sadzaphatikizamo a ndale za dziko audziko, ngakhale’nso mafumu a ndale za dziko ndi achipembedzo amene alamulira m’Chikristu cha Dziko. Iwo ali kabungwe ka olamulira kapadera kakumwamba, kanthu kena katsopano kwenikweni. Posakhala’nso a mkhalidwa waumunthu, iwo ali ndi ‘mkhalidwe waumulungu.’ Iwo ali “wolengedwa watsopano.” (2 Petro 1:4; 2 Akorinto 5:17) Iwo akwaniritsa ziyeneretso za kukhala wophunzira pa dziko lapansi kuti alowe mu ufumu wakumwamba. Iwo ‘anabadwa’nso, ‘kubadwa mwa madzi ndi mzimu,’ “sanabadwa ndi mwazi, kapena ndi chifuniro cha thupi, kapena ndi chifuniro cha munthu, koma cha Mulungu.” (Yohane 1:12,13; 3:3, 5) Mu Aroma 6:5, 8 ophunzira obadwa ndi mzimu a Kristu amawerenga kuti: “Ngati ife tinakhala olumikizidwa ndi Iye m’chifanizidwe cha imfa yake, kotero’nso tidzakhala m’chifanizidwe cha kuuka kwake. Koma ngati ife tinafa ndi Kristu, tikhulupirira kuti tidzakhala’nso amoyo ndi iye.”

9. Kodi chiukiriro cha Kristu chinali cha mtundu wotani, chiukiriro m’chimene’nso olowa nyumba ake 144,000 ayenera kugwirizana naye?

9 Kodi n’chiani chimene chiri ‘chifanizidwe cha kuuka kwake? Eya, kodi Kristu anaukitsidwa motani? Mu 1 Petro 3:18, NW tikuuzidwa kuti: “Kristu adafa kamodzi kwatha ponena za machimo, munthu wolungama kaamba ka osalungama, kuti akakutsogolereni kwa Mulungu, iye akumaphedwa m’thupi lanyama, koma akumakhalitsidwa ndi moyo mu mzimu.”

10. (a) Kodi n’chiani chimene chinali chifuno cha Mulungu m’kukonzera’ thupi lanyama Mwana wake Yesu pa dziko lapansi? (b) Kuti Yesu akhale’nso ndi moyo pambuyo pa kuphedwa n’thupi ponena za machimo, kodi ndi motani m’mene iye ayenera kuukitsidwira?

10 Mwa kutumiza Mwana wake m’chifanefane cha thupi lochimwa, Mulungu anachepetsa Mwana wake, nam’panga kukhala ‘wotsika pang’ono kwa angelo.’ (Aroma 8:3; Ahebri 2:7-9; Salmo 8:5) Koma Mulungu sanalinganize kuti Mwana wake wobadwa yekha akhalebe cholengedwa cha thupi ndi mwazi kosatha, wotsika kwa angelo akumwamba. Mulungu analinganiza kum’lemekeza kwambiri koposa angelo kaamba ka kukhulupirika kwake kufikira imfa ya thupi. Chotero thupi langwiro laumunthu limene Mulungu mozizwitsa ‘anakonzera’Yesu pa dziko lapansi linali thupi limene Yesu anapereka kwa Mulungu kamozi kwatha mu nsembe. Linaperekedwa kwa mtundu wa anthu kuti ulidye monga mkate; monga momwe’di Yesu ananenera kuti: “Mkate umene ndidzapatsa Ine, ndiwo thupi langa, ukhale moyo wa dziko.” (Ahebri 10:1-10; Yohane 6:51) Chotero, pambuyo pa ‘kuphedwa kwake n’thupi,” Yesu anayenera kuukitsidwira ku moyo kachiwiri’nso, anayenera ‘kukhalitsidwa moyo mu mzimu,’ monga Mwana wauzimu, wa kumwamba wa Mulungu.

11. Kuti ophunzira obadwa ndi mzimu a Kristu akhale m’chifanefane cha chiukiriro chake, kodi iwo ayenera kukhala ‘atakhalitsidwa moyo’ m’chiani, ndipo kodi ndi motani m’mene chimene’chi chimagwirizanira ndi 1 Akorinto 15:42-54?

11 Mofanana ndi Yesu Kristu, ophunzira ake odzozedwa ndi mzimu ayenera kukhala “okhulupirika kufikira imfa” m’thupi. (Chibvumbulutso 2:10) Kwa iwo kuti agwirizane naye “m’chifanefane cha chiukiriro chake,” iwo’nso, mofanana ndi iye, ayenera “kukhalitsidwa amoyo mu mzimu,” monga zolengedwa zauzimu. Mu 1 Akorinto 15:42-54, timawerenga ponena za mtundu wao wa chiukiriro kuti:

“Lifesedwa m’chibvundi, liukitsidwa m’chisabvundi; lifesedwa m’nyozo, liukitsidwa mumphamvu; lifesedwa thupi lachibadwidwe, liukitsidwa thupi lauzimu. Ngati pali thupi lachibadwidwe, pali’nso lauzimu. Kotero’nso kwalembedwa, munthu wayamba, Adamu, anakhala mzimu wamoyo. Adamu wotsiriza’yo anakhala mzimu wakulenga moyo. Koma chauzimu sichiri choyamba, koma chachibadwidwe; pamenepo chauzimu. Munthu woyamba’yo ali wapansi, wanthaka. Munthu wachiwiri ali wakumwamba. Monga wanthaka’yo atero’nso anthaka; ndi monga wakumwamba, atero’nso akumwamba. Ndipo monga tabvala fanizo la wanthaka’yo tidzabvala’nso fanizo la wakumwamba’yo.

“Koma ndinena ichi, abale, kuti thupi ndi mwazi sizingathe kulowa Ufumu wa Mulungu; kapena chibvundi sichilowa chisabvundi. Taonani, ndikuuzani, chinsinsi; sitidzagona tonse, koma tonse tidzasandulika, m’kamphindi, m’kuthwanima kwa diso, pa lipenga lotsiriza; pakuti lipenga lidzalira, ndipo akufa adzaukitsidwa osabvunda, ndipo ife tidzasandulika. Pakuti chobvunda ichi chiyenera kubvala chisabvundi, ndi chaimfa ichi kubvala chosafa. Ndipo pamene chobvunda ichi chikadzabvala chisabvundi ndi chaimfa ichi chikadzabvala chosafa, pamenepo padzachitika mau olembedwa, Imfa’yo yamezedwa m’chigonjetso.”

CHIUKIRIRO CHATSOPANO

12. (a) Popeza kuti chiukiriro cha 144,000 chiri m’chifanefane cha chiukiriro cha Kristu, kodi chimene’chi chikusonyeza kukhala kwa Kristu ndi mtundu wotani wa chiukiriro? (b) Kodi n’chifukwa ninji chimene’chi chiri chiukiriro chatsopano, ndipo kodi n’chiani chimene chimachipangitsa kukhala “kuuka koyamba”?

12 Kuukitsidwira ku kusabvunda ndi kusafa kotero’ko mu “thupi lauzimu” ndiko kumene Aroma 6:5 akucha “chifanizidwe cha kuuka kwake.” Chimene’chi chikutanthauza kuti Yesu Kristu iye mwini’yo anali ndi chiukiriro chotero’cho osati kumka ku moyo n’thupi lanyama limene liri lobvunda ndi lokhoza kufa ndi lotsika koposa angelo, koma m’thupi lauzimu ndipo monga “mzimu wakulenga moyo.” (1 Akorinto 15:45) Tsopano tingazindikire chifukwa chake, pambuyo pa chiukiriro chake, Yesu anafunikira kubvala matupi aumunthu limodzi ndi zobvala zakuthupi m’malo mwakuti adzipangitse kuonedwa ndi ophunzira ake m’kati mwa masiku makumi anai kufikira pa kukwera’nso kwake kumwamba. Chimene’chi chiri’di chiukiriro chatsopano, chosaoneka ndi maso aumunthu. Icho chayambirira chiukiriro cha anthu onse chikudza’cho. Chiri’nso choyamba m’kufunika. Chotero chikuchedwa “kuuka koyamba.” Ndicho chimene mtumwi Paulo akucha “chiukiriro choyamba” Olowa nyumba anzake a Kristu 144,000 akukhalamo ndi phande. (Afilipi 3:11, NW) Amene’wa ndiwo amene anenedwa m’Chibvumbulutso 20:4-6 kuti:

“Anakhala ndi moyo, nachita ufumu pamodzi ndi Kristu zaka chikwi....Ndiko kuuka kwa akufa koyamba. Wodala ndi woyera mtima ali iye amene achita nao pa kuuka koyamba; pa iwowa imfa yachiwiri iribe ulamuliro; komatu adzakhala ansembe a Mulungu ndi a Kristu, nadzachita ufumu pamodzi ndi Iye zaka chikwi’zo”

13. Kodi ndi gulu la boma la mtundu wotani limene chiukiriro choyamba chimene’cho chidzapereka kaamba ka ubwino wa mtundu wa anthu, ndipo kodi ndi motani m’mene likunenedwera mu 2 Petro 3:13?

13 Motero ziwalo za “mkwatibwi, mkazi wa Mwana wankhosa,”zikukhala ndi mtundu umodzimodzi’wo wa chiukiriro chofanana ndi chimene Mkwati, Yesu Kristu, anali nacho. Kodi zikutichititsa kuzindikira bwino lomwe chimene kwenikweni chiukiriro chotero’cho chidzatulutsa? Chikutulutsa kagulu ka olamulira osakhoza kubvunda, osakhoza kufa kaamba ka ubwino wa mtundu wonse wa anthu. (1 Timoteo 6:15, 16) Yesu Kristu limodzi ndi mafumu anzake ndi ansembe 144,000 adzaposa boma liri lonse la pa dziko lapansi limene mtundu wa anthu unakhala nalo m’kati mwa zaka zikwi zisanu ndi chimodzi za kukhalako. Lidzakhala boma labwino kopambana ndi la mtundu wapamwamba kopambana limene Mulungu angapereke kwa anthu. Lidzachotsa maboma onse a anthu amene ayendetsedwa ndi Satana Mdierekezi ndi ziwanda zake. Mulungu adzaligwiritsira ntchito kudzetsa pa dziko lapansi dongosolo lake latsopano, pakuti iro lidzdakhala “miyamba” yatsopano ya boma.—2 Petro 3:13.

14. (a) Kodi n’chiani chimene chiyenera kuchitikira “miyamba” yakale iripo’yi pa mtunda wa anthu? (b) Kodi ndi m’jira yotani boma latsopano’lo lidzakhalira “miyamba” m’njira yeniyeni?

14 “Miyamba” ya boma yopangidwa ndi anthu iyenera kuchoka, limodzi ndi wochirikiza wao wosaoneka, Satana Mdierekezi, “wolamulira wa dziko lino.” (Yohane 12:31, NW) Iyo ikuyandikira chionongeko chake mu “chisautso chachikulu” chimene chidzafika pachimake cha ukali wake woononga pa HarMagedo, pamene “nkhondo ya tsiku lalikulu la Mulungu Wamphamvuyonse” ichititsa chipambano cholemekezetsa kwa Yehova, Mfumu ya kumwamba ndi dziko lapansi. (Chibvumbulutso 16:14-16; 19:11-21; Danieli 2:44) “Miyamba” yatsopano ya boma iyenera kuchita mphamvu ndi ulamuliro wake zosatsutsika. Iyenera kukhala yakumwamba, osati chabe m’njira yophiphiritsira, koma m’jira yeniyeni, mwa kupangidwa ndi olamulira auzimu okhala ndi “umulungu” ndi okhala osakhoza kufa ndi osakhoza kubvunda. (2 Petro 1:4) Maso athu adzakhala odalitsidwa pamene tidzaona kwenikweni zimene mtumwi Yohane anaona m’masomphenya. Kuifotokoza kwake n’kokondweretsa:

“Ndipo ndinaona m’mwamba mwatsopano ndi dziko [lapansi] latsopano; pakuti m’mwamba moyamba ndi dziko loyamba zidachoka, ndipo palibe’nso nyanja. Ndipo ndinaona mzinda woyera’wo, Yerusalemu watsopano, ulikutsika Kumwamba kwa Mulungu, wokonzeka ngti mkwatibwi wokometsedwera mwamuna wake,. Ndipo ndinamva mau akulu ochokera ku mpando wachifumu, ndi kunena Taonani, chihema cha Mulungu chiri mwa anthu; ndipo adzakhalitsa nao, ndi iwo adzakhala anthu ake, ndi Mulungu yekha adzakhala nao, Mulungu wao; ndipo adzawapukutira misozi yonse kuichotsa pamaso pao; ndipo sipadzakhala’nso imfa; ndipo sipadzakhala’nso maliro, kapena kulira, kapena chowawitsa, zoyamba’zo zapita.”—Chivumbulutso 21:1-4.

MZIMU UMACHIRIKIZA MFUMU YA MU MZERA WA DAVIDE

15, 16. (a) Kodi ndani amene anali magwero achibadwide a Davide ndi mzera wa mafumu a Israyeli? (b) Kodi ndi motani m’mene magwero achibadwidwe amene’wo anakhalira ngatichitsa cha mtengo ndi mizu yake, ndipo kodi magwero achibadwidwe amene’wo anafikira cholinga chake cha mbadwa mwa yani

15 Pambuyo pake m’masomphenya kwa Yohane, Mkwati wakumwamba’yo Yesu Kristu anati: “Ine ndine muzu ndi mbadwa ya Davide, nyenyezi yonyezimira ya nthanda.” (Chibvumbulutso 22:16) Atate wa Mfumu Davide anali Jese wa ku Betlehemu ndi wa pfuko la Yuda. Chotero Yesu anali mbadwa ya Jese kupyolera mwa Davide. Ndipo’nso Jese anali phata lakuthupi la Mfumu Davide ndi la mzera wa Davide wa mafumu pa Israyeli yense.

16 Ufumu Waudavide unali ngati mtengo wokhala ndi phata ndi mizu yake mwa atate wa Davide Jese. M’chaka cha 607 B.C.E., pa kuonongedwa kwa Yerusalemu ndi kuchotsedwa kwa mfumu yake kumka ku Babulo, mtengo waufumu umene’wo unadulidwa. Ufumu Waudavide sunadzabwezeretsedwe’nso ku Yerusalemu. Chimene chinatsala chinali ngati chitsa cha mtengo limodzi ndi mizu yake yonse. Chimene’chi chinaphiphiritsira atate wa Davide Jese. Jese anasiyidwa wopanda mbadwa yolamulira mokangalika monga mfumu pa Israyeli. Koma munli chikhalirebe nyonga m’chitsa cha mtengo ndi mizu yake, pakuti mbadwa ya mzera wa Jese kupyolera mwa Mfumu Davide inapitirizabe. Iyo inafika pa cholinga chake cha mbadwa mwa Mesiya Yesu.

17. (a) Kodi ndi motani m’mene Yesu Kristu anapatsira nyonga ufumu umene unali ndi magwero ake mwa Jese? (b) Kodi ndi liti pamene ufumu amene’wo unapatsidwa mphamvu, ndipo kodi ndi mphamvu yotani imene imapatsa nyonga Mfumu’yo imene iri mwana wa Jese kupyolera mwa Davide?

17 Mwa kubadwa mwa namwali Wachiyuda Mariya pa Betelehemu, Yesu anakhala ngati “mphukira” yotuluka pa tsinde la Jese ndi monga “nthambi” yotuluka m’mizu ya Jese. Monga wotero iye akatha kupatsa nyonga ufumu umene unazikidwa pa Jese, atate wa mafumu pa Israyeli. Pamene Yehova Mulungu anadzoza Yesu ndi mzimu yoyera, “mphukira” yophiphiritsira kapena “nthambi” imene’yi inakhala Woyembekezera kukhala Ufumu ya ufumu Waudavide. Pa mapeto a Nthawi za Akunja mu 1914 Mulungu anam’longa kukhala Mfumu kumwamba. Ponena za ntchito yake Yesaya 11:1-5 amati:

“Ndipo padzatuluka mphukira pa tsinde la Jese, ndi nthambi yotuluka m’mizu yake idzabala zipatso; ndipo mzimu wa Yehova udzam’balira iye mzimu wanzeru ndi wakuzindikira, mzimu wa uphungu ndi mphamvu, mzimu wakudziwa ndi wakuopa Yehova; ndipo adzakondwera nako kumuopa Yehova.”

“Ndipo sadzaweruza monga apenya maso, sadzadzudzula mwamphekesera: koma ndi chilungamo adzaweruza aumphawi, nadzadzudzulira ofatsa a m’dziko moongoka; ndipo adzamenya dziko lapansi ndi chibonga cha kukamwa kwake, nadzapha oipa ndi mpweya wa miromo yake. Ndipo chilungamo chidzakhala mpango wa m’chuuno mwake, ndi chikhulupiriko chidzakhala mpango wa pa zimpsyo zake.”

18. (a) Kodi ndi motani m’mene “mphukira” yophiphiritsira’yo ikumenyera dziko lapansi ndi chibonga cha kukamwa kwake? (b) Kodi ndi motani m’mene ikuphera oipa ndi mpweya wa miromo yake?

18 M’kati mwa “chitsautso chachikulu” chikudza’cho “mphukira pa tsinde la Jese” yophiphiritsira‘yo ‘idzamenya’di dziko lapansi ndi chibonga cha kukamwa kwake.’Malamulo aufumu ochokera pakamwa pake adzakhala ngati chibonga chimene chikuphwanya zidutswazidutswa makonzedwe a anthu a pa dziko lapansi a mtundu wa anthu, dongosolo lakale la zinthu. Malamulo ake ali amphamvu, ofulumira ndi osonkhezera ku ntchito, iwo akutuluka pa miromo pake ndi chiyambukiro cha mphamvu ya kupha pa adani ake a pa dziko lapansi ouma khosi.

19. Kodi ndi motani m’mene Mfumu, mochirikizidwa ndi mzimu wa Mulungu, akulanditsira ofatsa ndi aumphawi kwa wotsendereza woipa kwamuyaya?

19 Kulankhula ndi ulamuliro wa kupha wotsutsa adani ake oipa kumene’ku kukufanana ndi “lupanga lakuthwa lalitali” lophiphiritsiridwa kukhala likutuluka m’kamwa mwa Mfumu m’malo mwakuti ‘amenye nalo mitundu, ndipo iye adzaweta [mitundu] ndi ndondo yachisulo.’ (Chimvumbulutso 19:11-15, NW) Mwa kuchita zimene’zi, mfumu Yaumesiya’yo, mochirikizidwa ndi mzimu wa Yehova, ikulanditsa ofatsa ndi odzichepetsa a dziko lapansi. Pamene iye alamulira limodzi ndi mafumu anzake 144,000, iye sadzalola otsendereza oipa kupeza’nso ulamuliro pa dziko lapansi.

20. Mu Yesaya 11:10:12 kodi ndi kusonkhanitsidwa’nso kwa yani kumene kukunenedweratu, ndipo kodi iwo akusonkhanitsidwira’nso m’chiani ndipo m’mikhalidwe yotani?

20 Chiyambire pa kukhazikitsidwa kwake pa mpando wachifumu kumwamba pa mapeto a Nthawi za Akunja mu 1914, “mphukira” yophiphiritsira’yo yotuluka m’mizu ya Jese yachititsa kukwaniritsidwa kwa mbali ina ya ulosi wa Yesaya, chaputala cha khumi ndi chimodzi. Iwo yachititsa kusonkhanitsidwa kwa otsalira a olowa nyumba ake odzozedwa kuchokera ku mbali zonse za dziko lapansi kumene iwo anabalalitsidwirako ndi zizunzo m’kati mwa NkondoYoyamba ya Dziko. Iye wawalowetsa m’paradaiso wauzimu, kumene iwo akusangalala ndi mtendere ndi chigwirizano ndi Mulungu ndipo akutulutsa “zipatso za mzimu”zochuluka. (Agalatiya 5:22, 23) Uchinyama wa dziko ukuchotsedwamo! (Yesaya 11:6-9) Yesaya anayembekezera kusonkhanitsidwa ndi kubwezeretsedwa kwa Israyeli wauzimu, ndipo anati:

“Ndipo padzakhala tsiku lomwelo, kuti muzu wa Jese umene uima ngati mbendera ya mitundu ya anthu, amitundu adzafunafuna uwu; ndipo popuma pake padzakhala ulemerero.

“Ndipo padzakhala tsiku lomwelo, kuti Ambuye adzabweza kachiwiri ndi dzanja lake la anthu ake otsala ochokera ku Asuri, ndi ku Aigupto, ndi Patirosi, ndi ku Kusi, ndi ku Elamu, ndi ku Sinara, ndi ku Hamati, ndi ku zisumbu za m’nyanja yamchere. Ndipo Iye adzaimika mbendera ya amitundu, ndipo adzasonkhanitsa oingitsidwa a Israyeli, namema obalalika a Yuda, kuchokera ku madera anai a dziko lapansi.”—Yesaya 11:10-12.

21. Kodi “nthambi” yophiphiritsira yotuluka m’mizu ya Jese ikunenedwa pano kukhala chiani, ndipo kodi ndi motani m’mene iye wapangitsiridwa kutumikira monga “chizindikiro” kwa amitundu?

21 Pano “nthambi” yophiphiritsira’yo yotuluka m’mizu ya Jese ikunenedwa kukhala “muzu” weniweni wa Jese. Pa mapeto a Nthawi za Akunja mu 1914 ufumu Yaumesiya imene’yi inaukitsidwa m’mphamvu yaufumu. Pokhala italengezedwa pa dziko lonse lapansi, iyo inatumikira monga “mbendera” ku imene otsalira onse a Aisrayeli auzimu ayenera kusonkhanako, popeza kuti iyo ndiyo Mfumu yomalamulira. Osonkhanitsidwa’nso ndi kubwezeretsedwa’nso amene’wa kuyambira pa nthawi imene’yo akwaniritsa kudzozedwa kwao kubukitsa kwa anthu onse mfumu Yaumesiya ndi ufumu wake.

22. Kodi anthu a mwa amitundu tsopano atembenukira kwa yani mofuna kudziwa, ndipo kodi ndani amene wayankha mafunso ao, limodzi ndi chotulukapo chotani?

22 Anthu zikwi mazana ochuluka ochokera pakati pa mitundu yonse tsopano mofuna kudziwa atembenukira ku ufumu Waumesiya wonga mbendera’wo. Iwo adzikhutiritsa kuti Yesu Kristu wolemekezedwa’yo ali’di Mesiya wolonjezedwa wa Yehova. Otsalira odzozedwa, ndi mayankho ku mafunso ao, awathandiza kuchita chimene’chi. Mokondwera iwo asonkhana ku mbali ya ufumu Waumesiya wa Yehova, akumautamanda kukhala chiyembekezo chokha kaamba ka mtundu wa anthu. Iwo apanga kale “khamu lalikulu,” chiwerengero chake chotsirizira chimene pofika pa nthawi ya “chisautso chachikulu” sitikuchidziwa.—Chibvumbulutso 7:9-17.

“DZIKO LAPANSI LATSOPANO”

23. Kodi ndi mokhazikika chotani m’mene Yehova adzakhazikitsira miyamba yatsopano ndi dziko lapansi lapsopano, ndipo kodi kungafune kachitidwe kotani kwa iye kuti alowetse anthu ake ‘m m’Dongosolo Latsopano?

23 Dongosolo loipa lakale, limene ladzikhazikitsa zolimba m’dziko lapansi, liyenera kuchoka –kulowa m’chionongeko! Yehova tsopano akulinganiza zinthu zonse kaamba ka dongosolo latsopano laulemerero! Iye ‘wakhazikitsa’ “miyamba” yatsopano ya boma, akumaikhazikitsa mwamphamvu kwambiri m’gulu lake la m’chilengedwe chonse kwakuti singathe kuzulidwa ndi anthu kapena ziwanda. “Dziko lapansi latsopano” limene iye akuliyambitsa adzalikhazika pa maziko amphamvu otero’wo kwakuti palibe chiri chonse chidzalipangitsa kugwedezeka kapena kuweseka mpaka kuonongeka. Iye adzalowetsa m’dongosolo latsopano limene’li otsalira a Israyeli wauzimu ndi “khamu lalikulu” ngakhale ngati iye angafunikire kuchita mofanana ndi pa Nyanja Yofiira kale’lo m’nthawi ya Mose, kubvundula madzi ndi kuwapanga kukokoma kotero kuti agawe njira kaamba ka anthu ake olanditsidwa kudzerapo. Nazi zimene iye akunena mu Yesaya 51:15, 16:

“Ine ndine Yehova Mulungu wako, amene ndiutsa nyanja, kuti mafunde ake akokome; Yehova wa makamu ndi dzina lake. Ndipo ndaika mau anga m’kamwa mwako; ndipo ndakuphimba ndi mthunzi wa dzanja langa, kuti ndikhazike kumwamba ndi kuika maziko a dziko lapansi, ndi kunena kwa Ziyoni, Inu ndinu anthu anga.”

24. Kodi Yehova waika mkamwa mwa yani mau ake, ndipo kodi n’chifukwa ninji anawaphimba amene’wa ndi nthunzi wa dzanja lake?

24 Palibe chopinga choikidwa m’njira Yake ndi adani chidzakhala chosalakika kwa Yehova. Monga ngati pa Phiri la Sinai Iye anaika mau ake m’kamwa mwa anthu ake osankhidwa kupyolera mwa nkhoswe Mose ndipo pambuyo pake anawatsogolera pansi pa mthunzi wotetezera wa dzanja lake kulowa m’Dziko Lolonjezedwa, wachitira mofanamo otsalira a Israyeli wauzimu. Iye waika mau ake, uthenga wake wa pa nthawi ino, m’kamwa mwa otsalira auzimu kuti iwo abvomereze poyera pamaso pa dziko lonse, kaamba ka chipulumutso cha iwo eni ndi cha awo omvetsera molabadira. “Khamu lalikulu” la “nkosa zina” lachita mobvomereza zimene iro lamva ndipo lalowetsa mau a Mulungu m’kamwa mwao. Chifukwa chakuti lonse’li lakhala mboni zake Zachikristu, Yehova akuliphimba ndi mthunzi wa dzanja lake kaamba ka chitetezo chao m’dziko lino.

25. (a) Kodi Yehova adzapanga otsalira otetezeredwa’wo kukhala mbali ya chiani, ndipo kodi ndi kubvomereza kotani kumene Iye adzakupanga kwa iwo? (b) Kodi Mulungu adzapanga “khamu lalikulu” lotetezeredwa’lo kukhala chiani, ndipo kodi iwo adzanenedwa kukhala anthu a yani?

25 Yehova ali ndi cholinga m’kachitidwe kotereka. Cholinga chake ndicho kupangitsa otsalira okhulupirika potsirizira pake kukhala mbali ya “miyamba” yatsopano ya boma monga olowa nyumba limodzi ndi Mfumu Yesu Kristu. Ponena za “khamu lalikulu” la “nkhosa zina,” Yehova adzawapanga kukhala mbali yoyambirira ya “dziko [lapansi] latsopano,”chitaganya chatsopano cha pa dziko lapansi m’Dongosolo Latsopano. Mwa kupulumutsa osalira okhulupirika a Israyeli wauzimu kupyola “chisautso chachikulu” chikudza’cho iye adzakhala akunena ndi Aisrayeli auzimu amene’wa amene ‘akuyandikira Phiri la Ziyoni ndi Yerusalemu wakumwamba’ kuti, “Inu ndinu anthu anga.” (Ahebri 12:22; Yesaya 51:16) Ndipo’nso, “chihema cha Mulungu” chotetezera chidzayamba kukhala ndi “khamu lalikulu” lopulumuka’lo, ndipo, monga momwe Chibvumbulutso 21:3 chimanenera, “iwo adzakhala anthu ake.”

26. Kodi ndi mzimu wotani umene sudzakhalamo m’Dongosolo Latsopano, ndipo kodi oyembekezera kulowamo akudzazidwa chiani tsopano?

26 Mzimu woyera udzagwira ntchito ndi kuchuluka m’dongosolo latsopano la dziko lonse lapansi. Yehova adzakhala atachotsa ‘mzimu wakuchita tsopano mwa ana a kusamvera’ woipitsa. “Ana a kusamvera” otero’ wo adzaonongeka mu “chisauto chachikulu” ndipo Satana Mdierekezi ndi ziwanda zake adzakhala ataponyedwa m’mphompho. (Aefeso 2:2; Chibvumbultso 20:1-3) M’kukonzekera Dongosolo Latsopano, oyembekezera kukhala opulumuka “chisautso chachikulu”chirinkudza’cho akupitirizabe “kudzazidwa mzimu woyera” wochokera kwa Mulungu.—Aefeso 5:18, NW.

27. M’DongosoloLatsopano kodi n’chiani chimene chidzachitika chimene ngakhale luso la za mankhwala lopita patsogolo la lero lino silingalingane nacho?

27 Tingangoyerekezera m’mene udzakhalira pano pa dziko lapansi pambuyo pa “nkhondo ya tsiku lalikulu la Mulungu Wamphamvuyonse” pa HarMagedo ndi pambuyo pa kumangidwa kwa Satana ndi ziwanda zake “m’phompho.” Pamenepo mzimu woyera udzalamulira mwaufulu pa dziko lonse lapansi. Tikukumbutsidwa za m’mene mzimu woyera unagwirira ntchito modabwitsa m’masiku a Yesu Kristu ndi atumwi ake pa dziko lapansi zaka mazana kumi ndi asanu ndi anai zapita’zo. Zozizwitsa zodabwitsa zinachitika, mochititsa chisangalalo chosaneneka kwa anthu amene anapindula nazo. Kupita patsogolo kwa luso la za mankhwala achipatala lero lino kulibe kali konse kolingana ndi machiritso a pa nthawi yomwe’yo ndi kuchira kumene kunachitika pa nthawi imene’yo mochi titsidwa ndi mzimu woyera. Panali’nso kuukitsidwa kwa anthu wa akufa! Chabwino kwambiri koposa chimene’cho, panali’nso kuchiritsa kwauzimu mwa njira yakulengeza ndi kuphunzitsa mbiri yabwino yonena za ufumu Waumesiya wa Mulungu. Panali kumasulidwa kwa awo amene anasungidwa mu ukapolo nd miyambo yonyenga yachipembedzo yochititsa imfa.

ZIYEMBEKEZO ZA DONGOSOLO LATSOPANO!

28. Kodi mbali yotani pa dziko lapansi imene otsalira opulumuka’wo adzakhala nayo m’ntchito za Dongosolo Latsopano, ndipo kufikira pa nthawi ya chochitika chotani?

28 Zodabwitsa’di zinali zozizwitsa zimene’zo zimene zinachitika m’kati mwa nthawi’yo pamene mpingo Wachikristu unali kukhazikitsidwa. Koma zinali kuoneratu chimene chidzachitidwa ndi mzimu woyera m’dongosolo latsopano la Yehova. Tingayembekezere otsalira opulumuka kukhala ndi phande m’ntchito zosangalatsa pa chiyambi cha Dongosolo Latsopano la Yehova. Koma kuti ndi kwa utali wotani, sitikudziwa pa tsopano lino kuchokera m’Malemba Oyera. Iwo ali ndi “ukwati” wouyembekezera—ukwati wa kumwamba wa Mwanawankhosa kwa mpingo wake wathunthu wa mkwatibwi. Pa nthawi imene umene’wu ukachitika, iwo adzachoka pa dziko lapansi ndi kupfupidwa ndi mbali yosangalatsa mu “kuuka koyamba” Chotero iwo ayenera kukhala okhulupirika kufikira mapeto.

29. Kodi “khamu lalikulu”lidzaona chiukiriro cha kagulu ka Mkwati’bwi, kapena chiukiriro cha yani?

29 Chiukiriro cha kagulu ka Mkwatibwi chidzakhala chosaoneka ndi maso a “khamu lalikulu” la opulumuka chitsautso, amene akuyambekezera kukhala kosatha m’paradaiso wobwezeretsedwa’nso pa dziko lapansi. Koma padzakhala chiukiriro pa dziko lapansi chimene chidzakhala chooneka kwa “khamu lalikulu” pa “nthawi” ya Mulungu mwa Kristu ya kuukitsa anthu akufa.

30. Ponena za anthu akufa oomboledwa, kodi zikudalira pa chiani ponena zakuti kaya chiukiriro chao chidzatsogolera ku moyo wosatha kapena ku chiweruzo chachitsutso?

30 Yesu Kristu iye mwini akuyembekezera nthawi imene’yo. Iye anaineneratu pamene anali kulongosola tsiku la kuweruzidwa kwa dziko nati: “Ikudza nthawi imene onse ali m’manda adzamva mau ake, nadzatulukira, amene adachita zabwino, kukuuka kwa moyo; koma amene adachita zoipa kukuuka kwa kuweruza.” (Yohane 5:27-29) Ponena za awo oukitsidwa chifukwa cha kuyenera kwa nsembe ya dipo ya Yesu Kristu, zikungodalira pa njira yao yam’tsogolo pansi pa ufumu wa Kristu ponena zakuti kaya chiukiriro potsirizira pake chikutsogolera ku moyo wosatha pa dziko lapanso laparadaiso kapena chikutsogolera potsiriza ku chiweruzo mwa chimene iwo akutsutsidwa kumka ku chionongeko chosatha. Awo amene pa nthawi’yo akugonjera ku mzimu woyera wochuluka’wo ndi kuulola kukhala mphamvu yotsogoza m’miyoyo yao adzapeza moyo wamuyaya m’Paradaiso. Awo amene atsutsa mzimu woyera woonekera bwino pa nthawi’yo adzalandira chirango cha kuchimwira mzimu woyera, ndiko kuti, imfa yamuyaya.

31. Kodi ndi lonjezo lotani lopangidwa pa tsiku la kufa kwake limene Mfumu Yesu Kristu akuonabe kukhala wathayo kulikwaniritsa, ndipo kodi ndi liti pamene “nthawi” imene’yi idzakwana?

31 Mfumu yakumwamba, Yesu Kristu, akuonabe kukhala wathayo kukwanititsa lonjezo lumene iye anapereka kwa wochita zoipa womvera chisoni amene anafera pambali pake pa Kalvari, pa tsiku lamdima limene’lo la Nisan 14, 33 C.E. Ndithudi, wochita zoipa wopachikidwa amene’yo tsopano ali wakufa ndi wosakumbukira kanthu. (Mlaliki 9:5, 10) Koma Yesu Kristu wolemekezedwa’yo amakumbukira mau ake kwa womvera chisoni’yo: “Indetu ndikuuza iwe lero, Udzakhala ndi ine m’Paradaiso.” (Luka 23:39-43, NW) Polingalira kuchula Paradaiso kumene’ku, “nthawi” yakuti Yesu alole wochita zoipa’yo m’manda a chikumbukiro kumva mau ake sidzakwana kufikira kubwezeretsedwa kwa Paradaiso pa dziko lapansi kukuchitika ndipo wochita zoipa’yo angathe kuona kusintha pa dziko lapansi. Mwa kugwirizanitsa moyo wake ndi mzimu woyera umene umachokera kwa Mulungu kupyolera mwa Yesu Kristu, wochita zoipa’yo angapangitse chiukiriro chake kukhala cha mtundu umene ukuchititsa moyo wamuyaya m’Paradaiso wa pa dziko lonse lapansi.

32. Pakati pa awo olandiridwa kuchokera kwa akufa kumka ku moyo wa pa dziko lapansi kodi padzakhala “mtambo” wotani wochulidwa m’Malemba?

32 Pamenepo ife pa dziko lapansi tidzalandira kuchokera kwa akufa osati kokha achibale athu oomboledwa ndi mabwenzi koma’nso amuna ndi akazi okhulupirika a m’nthawi zakale amene anali mboni Yehova ndi amene anasonkhezeredwa ndi mzimu woyera. Amene’wa adzaphatikizamo “mtambo waukulu wa mboni,” kuyambira kwa Yohane M’batizi mpaka kukafika kwa woyambirira kufera Yehova, amene ali, Abele. (Ahebri 11:2 kufikira 12:1) Amene’wa mosakaikira adzakhala ndi mbali yolamulira m’Dongosolo Latsopano.

33. Kodi ndi malo a ntchito a boma otani amene amuna ochokera mu “mtambo” umene’wo adzapatsidwa limodzi ndi ena, ndipo kodi ndi kaamba ka kulankhulana kotani kumene owo adzatumikira monga ankhoswe?

33 Mwa amene’wa Mfumu Yesu Kristu adzasankhamo amuna awo amene iye “adzawaika akhale akalonga m’dziko lonse lapansi.” (Salmo 45:16, NW Padzakhala pali kale “akalonga” pa dziko lapansi iwo asanakhale. Ndani? Amuna’wo ochokera pakati “khamu lalikulu” la opulumuka “chisautso” amene adzakhala atasankhidwa kukhala otero pa kuyamba kwa Dongosolo Latsopano. (Chibvumbulutso 7:9-17; Yesaya 32:1, 2) Koma “akalonga” onse adzakhala oimira ooneka ndi maso a pa dziko lapansi a “miyamba yatsopano,” boma latsopano la kumwamba la Yesu Kristu ndi olowa nyumba limodzi ndi Yesu Kristu 144,000. Mosakaikira “akalonga” amene’wa adzatumikira monga ankhoswe a kulankhulana pakati pa Ufumu wosaoneka ndi chitaganya chooneka cha pa dziko lapansi cha mtundu wa anthu woomboledwa, “dziko [lapansi] latsopano.”a

34. M’Dongosolo Latsopano kodi ndi motani m’mene Yesu Kristu adzakwaniritsira ntchito yogwirizana ndi dzina lake laulemu la “Mulungu Wamphamvu, Atate Wosatha, Kalonga Wamtendere”?

34 Dongosolo Latsopano lidzakhala la mtendere wosadodometsedwa ku ngondya zinai za dziko lapansi. Lidzakhala mu ulamuliro wa ufumu wa uyo amene Atate wake wakumwamba anam’sankha kukhala ndi maina aulemu’wa “Wodabwitsa, Wauphungu, Mulungu wamphamvu, Atate Wosatha, Kalonga wa mtendere,” ndipo “za kuenjezera ulamuliro wake, ndi za mtendere sizidzatha.”(Yesaya 9:6, 7) Iye adzakhala AtateWosatha pakuti “ulamuliro” wake udzakhala wautate, womapereka moyo kwa nzika zake zonse zomvera monga ana ake. Iye adzakhala Mulungu Wamphamvu, pakuti iye adzakhala ngati Woweruza wonga Mulungu; koma iye sadzalambiridwa monga wotero ndi olandira mapindu ake a pa dziko lapansi otero’wo.—l Salmo 82:1-6; Yohane 1;1; 10:33-36.

35. Kodi ndani yekha pa nthawi imene’yo adzalambiridwa monga Mulungu?

35 Yehova yekha pa nthawi imene’yo adzalambiriridwa, pakuti ponena za Dongosolo Latsopano kwalembedwa kuti: “taonani, chihema cha Mulungu chiri mwa anthu; ndipo adzakhalitsa nao, ndi iwo adzakhala anthu ake, ndi Mulungu yekha adzakhala nao, Mulungu wao; ndipo adzawapukutira misozi yonse kuichotsa pamaso pao.” (Chibvumbulutso 21:3, 4) Satana Mdierekezi, “mulungu wa dongosolo lino la zinthu” sadzakhala mulungu wa Dongosolo Latsopano. (2 Akorinto 4:4, NW) Kulambira Mdierekezi, kulambira ziwanda, kudzathetsedwa. Yehova adzalambiridwa monga Mulungu.

36. Kodi ndi zipatso zotani zimene zidzalemeretsa Dongodolo Latsopano, koma kodi ndani amene adzaonekera pa kutha kwa zaka chikwi za ulamuliro wa Kristu?

36 Mzimu woyera udzadzaza Dongosolo lonse Latsopano. (Salmo 139:7-10) Paradaiso wa pa dziko lapansi adzalemeretsedwa ndi “zipatso” za mzimu umene’wo, monga ngati chikondi, chisangalalo, mtendere, kuleza mtima, kukoma mtima, chikhulupiriro, chifatso, chiletso. (Agalatiya 5:22, 23) Mkhalidwe wauzimu wobala zipatso umene’wo udzakhala chichulukire mpaka kukafika ku mapeto a ulamuliro wa zaka chikwi wa Kristu. Koma kodi ndiyeno chiani? Satana ndi ziwanda zake akutuluka m’phompho, amene’wa akumamasulidwa kwa “kanthawi.” Mwa achinyengo iwo adzayesa kuchititsa dziko lonse lapansi kulamulidwa kachiwiri’nso ndi “mzimu wakuchita tsopano mwa ana a kusamvera.” Kodi iwo adzapambana ku mlingo wotani kulimbana ndi mzimu woyera wa Mulungu womalamulira’wo?—Chibvumbulutso 20:3.

37. (a) M’Dongosolo Latsopano kodi ndi ziukiro zotani zimene Satana ndi ziwanda zake akupanga pa mzimu woyera womalamulira’wo? (b) Kodi motani m’mene Yehova akulemekezeredwa kosatha?

37 Adzafika kokha pa mlingo wa kuchititsa chiwerengero cha mtunda wa anthu wobwezeretsedwa’wo kuchita chimo losakhululukidwa lochimwira mzimu woyera. Motero iwo akudzidula ku Magwero a kumwamba a mzimu wa moyo, Yehova Mulungu. Kumene’ku kukuchititsa imfa yosatha kwa iwo, “imfa yachiwiri,” Koma bwanji unyinji wa mtundu wa anthu m’malo ao okhala a Paradaiso okongola’wo. Eya, mzimu woyera udzapambana mwaulemerero ponena za iwo. Mokonda kosatha mzimu woyera, iwo adzakaniza zinyengo zoyesa za Satana. Mosagwedezeka iwo adzakhalabe o khulupirika kwa Mfumu yoyenera ya chilengedwe chonse, Mulungu wao Yehova. Kupyola kwao mokhulupirika chiyeso chotsirizira chimene’chi kumagwira ntchito kaambaka ku kulemekezedwa kwamuyaya kwa Yehova. Chikufikitsa ku kuthetsedwa kotheratu kotsirizira kwa mkangano wolimbaniridwa kwambiri wa zaka mazana ochuluka, wonena za umphummphu wopanda dyera wa zolengedwa za Yehova kulinga kwa iye monga Mfumu ya M’chilengedwe Chaponseponse. Chinenezo chonyenga cha Satana chikutsutsidwa kotheratu, Yehova akutsimikiziridwa kukhala woona kotheratu. (Aroma 3:4) “Kanthawi” ka kumasulidwa kwa Satana tsopano katha. Chotero, pamenepo, mloleni iye ndi “mbeu” yake yonse aphwanyidwe kuti asakhaleko mokwaniritsa lonjezo la Yehova la pa Edene. (Genesis 3:15; Chibvumbulutso 20:7-15) Haleluya!

38. Kodi ndi motani m’mene m’tsogolo mwa amuna ndi akazi amene’wo amene pa nthawi imene’yo akukhalabe odzazidwa mzimu woyera mudzakhalira mwachimwemwe?

38 Kodi ife enife tiyenera kukhalako kuti tidzaone kuonongedwa kwamuyaya kwa kuipa konse kumwamba ndi dziko lapansi ndiyeno kupitirizabe kukhala ndi moyo limodzi ndi m’tsogolo patsogolo pathu? M’tsogolo mopanda mapeto m’menemo mudzakhala mosangalatsa kwa amuna ndi akazi awo amene adzakhalabe odzazidwa ndi mzimu woyera m’kudzipereka kosasweka kwa Mulungu ndi Atate wa Ambuye wathu Yesu Kristu! Pokhala otsimikiziridwa ndi Iye kukhala oyenerera mphatso ya moyo wamuyaya, Iwo adzakhala ndi unyamata mu ungwiro waumunthu pakati pa Paradaiso wa kukongola kosafwifwa ndi makonzedwa osalephera a kukhala ndi moyo kosangalatsa. Nthawi zonse iwo adzafuna kukhala ndi moyo mogwirizana ndi mzimu woyera umene nthawi zonse wakhala kutseri kwa dongosolo latsopano lolemekeza Mulungu lotero’lo. O, tiyenitu titsimikizire kukhala oyenerera dongosolo latsopano limene’lo! Mogwirizana ndi chikhumbo chochokera mu mtima chimene’cho, tiyeni pemphero lathu losalekeza likhale lija la wamasa lmo Davide monga momwe linaperekedwera kwa Mulungu m’kati mwa dziko laudani kuti:

“Mundilanditse kwa adani anga, Yehova; ndinabisala mwa Inu. Mundiphunzitse chokonda Inu; popeza Inu ndinu Mulungu wanga; Mzimu wanu ndi wokoma; munditsogolera kuchidikha.”—Salmo 143:9, 10.

39. Kodi potsiriza, tikunenanji, kwa awo amene ngakhale tsopano akukhumba kukhala ndi moyo mogwirizana ndi mzimu wa Mulungu?

39 Pamenepo, moona mtima, kwa anthu onse ofuna ngakhale tsopano kukhala ndi moyo mogwirizana ndi mphamvu yogwira ntachito yolemekeza Mulungu pomaliza tikuti: “Chisomo cha Ambuye Yesu Kristu, ndi chikondi cha Mulungu, ndi chiyanjano cha Mzimu Woyera zikhale ndi inu nonse.” 2 Akorinto 13:14.

[Mawu a M’munsi]

a Yerekezerani ndi Ezekieli 44:3; 45:7-22; 46:2-18; 48:21, 22.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena