Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • su mutu 2 tsamba 13-20
  • Nkhani Zimene Zitsimikiziritsa Mtsogolo Mwathu

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Nkhani Zimene Zitsimikiziritsa Mtsogolo Mwathu
  • Kupulumuka Kuloŵa m’Dziko Lapansi Latsopano
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • NKHANI YAULAMULIRO
  • KODI MUDZASANKHA MBALI ITI?
  • MITUNDU YONSE IKUMKA KU ARMAGEDO
  • Nkhani Imene Ikulowetsamo Inu
    Mtendere Weniweni ndi Chisungiko—Kodi Mungazipeze Motani?
  • Kodi Mulungu Analenga Dziko Lapansili Chifukwa Chiyani?
    Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni?
  • Olamulira Okhala m’Malo a Mizimu
    Nsanja ya Olonda—1995
  • Mtsogolo Mosungika Mmene Mungamupezere
    M’tsogolo Mosungika—M’mene Mungamupezere
Onani Zambiri
Kupulumuka Kuloŵa m’Dziko Lapansi Latsopano
su mutu 2 tsamba 13-20

Mutu 2

Nkhani Zimene Zitsimikiziritsa Mtsogolo Mwathu

M’ZAKA zaposachedwapa nkhani zofunika zimene zimakhudza mtsogolo mwathu zaikidwa pamaso pathu motsatizanatsatizana mofulumira kwambiri. Mikhalidwe njakuti anthu kulikonse akufuna mpumulo kwambiri. Mwinamwake amakhulupirira Mulungu, koma kungawonekere kwa iwo kuti ngati mkhalidwe padziko lapansi pano uti udzakhale bwino, anthu adzafunikira kuuchititsa. Ena amayesa kutero mwa maboma alipoŵa kapena mwa kutsutsa kwa aunyinji zosankha za maboma ameneŵa. Ena amakhulupirira kuti kupanduka ndiko njira yokha. Amalingalira kuti kusintha malamulo, kusintha olamulira kapena maboma athunthu kudzachititsadi mikhalidwe kusintha. Koma kodi maumboni akusonyezanji? Atayesa kwa zaka zikwi zambiri, anthu sanatulutse ngakhale boma limodzi limene labweretsa chilungamo chopanda tsankhu, chisungiko chenicheni ndi chimwemwe chosatha kwa nzika zake zonse. Kodi nchiyani chimene chimachititsa zimenezi?

2 Ziribe kanthu kuti kaya zolinga za olamulirawo zikhale zabwino motani, maboma onse a anthu akuyendetsedwa ndi mphamvu yosaletseka ndi olamulirawo. Ndi yani? Ndi mizimu yamphamvu, Satana Mdyerekezi ndi ziŵanda zake. Ndithudi, anthu ambiri amaseka kukhulupirira mizimu yoteroyo. Koma Yesu Kristu sanatero. Iye mwini anadziŵa chiyambi cha Satana namutcha “wolamulira wadziko [lino].” (Yohane 12:31) M’chinenero chophiphiritsira, Baibulo limasonyeza dongosolo landale zadziko ladziko lonse kukhala chirombo ndipo limavumbula kuti “chinjoka [Satana] chinapereka kwa chirombo mphamvu yake ndi mpando wake wachifumu ndi ulamuliro waukulu.” (Chivumbulutso 13:​1, 2, NW; yerekezerani ndi Danieli 7:​2-8, 12, 23-26.) Ndipo ponena za nthaŵi yathu Baibulo lidaneneratu ‘tsoka lowonjezereka la dziko lapansi . . . chifukwa Mdyerekezi watsikira kwa inu.’ (Chivumbulutso 12:12) Palibe chirichonse chimene chingalongosole mokhutiritsa zipolowe zimene anthu akankhidwiramo. Koma kodi zinachitika motani? Kodi tingachitenji kuti tipeze mpumulo?

NKHANI YAULAMULIRO

3 Mitu yoyambirira ya Baibulo imatiuza kuti pamene Yehova Mulungu analenga anthu aŵiri oyamba, Adamu ndi Hava, naŵaika m’munda wa Edeni anaŵalangiza za unansi wawo kwa iye. Iye anali Atate wawo, Wogaŵira wawo wowoloŵa manja, ndiponso Wolamulira Wachilengedwe chonse. Kaamba ka ubwino wawo, anafunikira kuzindikira kuti moyo wawo wopitirizabe unadalira pa kumvera kwa Mulungu.​—⁠Genesis 2:​16, 17; yerekezerani ndi Machitidwe 17:​24, 25.

4 Panthaŵi imeneyo chilengedwe chonse chinali changwiro. Mofanana ndi nyama angelo ndi anthu anali ndi mphamvu ya kudzisankhira. Koma mwamsanga pambuyo pa kulengedwa kwa munthu mmodzi wa angelo, pogwiritsira ntchito molakwa mphamvu zodabwitsa za kupanga zosankha zake, anapandukira ulamuliro wa Yehova. Iye motero anadzipanga kukhala mdani, kapena wotsutsa, limene liri tanthauzo lenileni la dzinalo Satana. (Yerekezerani ndi Yakobo 1:​14, 15; Chivumbulutso 12:⁠9.) Mosonkhezeredwa ndi chikhumbo, Satana anafunafuna kunyenga anthu aŵiri oyambirira kuchoka kwa Yehova Mulungu ndi kuŵaloŵetsa mu ulamuliro wake. Iye anawona mwa iwo kuthekera kwa dziko lapansi lodzazidwa ndi anthu omlemekeza monga mulungu wawo. (Yerekezerani ndi Yesaya 14:​12-14; Luka 4:​5-7.) Cholembedwa cha zimene zinachitika mu Edene sichiri nthano wamba. Yesu Kristu anachitchula monga chochitika chenicheni.​—⁠Mateyu 19:​4, 5.

5 Ponena za Mdyerekezi Yesu anati: “Sanaima m’chowonadi . . . Ali wabodza, ndi atate wake wabodza.” (Yohane 8:44) Bodza la Mdyerekezi loyamba kulembedwa linali kwa Hava pamene anakayikira kunena zowona kwa Mulungu. Analimbikitsa kukanidwa kwa lamulo la Mulungu nanena kuti kukakhala kopindulitsa kwa aliyense kukhazikitsa miyezo yake m’moyo. (Genesis 3:​1-5; yerekezerani ndi Yeremiya 10:23.) Motero ulamuliro wa Yehova mu Edene m’menemo unakayikiridwa. Monga momwe zochitika zapambuyo pake zimasonyezera, uphumphu wa zolengedwa zonse zaluntha kwa Mulungu unakayikiridwanso. Kodi izo zinatumikira Mulungu chifukwa chakuti zinamkondadi, kapena kodi zinakachititsidwa kufufunuka kwa iye? (Yobu 1:​7-12; 2:​3-5; Luka 22:31) Nkhanizi zikayambukira aliyense kumwamba ndi padziko lapansi. Kodi Wolamulira wa Chilengedwe chonse anachitanji?

6 Mmalo mwa kuwononga opandukawo mofulumira, Yehova mwanzeru anapereka nyengo yanthaŵi yoikika kuti nkhanizo zithetsedweretu. Mulungu anachitadi zimenezi, osati kuti atsimikiziritse chirichonse, koma kuti alole zolengedwa zokhala ndi kudzisankhira kuti zidziwonere zotulukapo zoipa zochititsidwa ndi kupandukira ulamuliro wake, ndiponso kuzipatsa mpata wa kusonyeza pamene izo zirizonse pazokha zikuima pankhani zofunika zimenezi. Nkhanizo pokhala zitathetsedwa, aliyense sakaloledwanso kuwononga mtendere.

7 Yehova Mulungu, pokhala Mlengi wa anthu, analinso wolamulira wawo woyenera. (Chivumbulutso 4:11) Komabe, m’kupita kwa nthaŵi, Satana ndi ziŵanda zake anayamba kusonkhezera mwa anthu chikhumbo osati kokha cha kudzikhazikitsira miyezo yawo yonena za chabwino ndi choipa komanso cha kulamulira anthu anzawo. Nimrode anali woyamba kudzikhazikitsa monga mfumu, akumalamulira mizinda m’Mesopotamiya. Iye anali “mpalu [wa nyama ndi wa anthu omwe] wamphamvu pamaso pa Yehova.” (Genesis 10:​8-12) Kuyambira m’nthaŵi ya Nimrode mpaka lerolino, mtundu uliwonse wothekera wa boma la anthu wayesedwa. Koma cholembedwa chonse, monga momwe wophunzira mbiri aliyense akudziŵira, chakhala chimodzi cha chisalungamo ndi kukhetsa mwazi.​—⁠Mlaliki 8:⁠9.

8 Pamene Yesu Kristu anali padziko lapansi, Satana anayesanso kumloŵetsa mu ulamuliro wake. Iye analonjeza Yesu “maufumu onse a dziko lokhalamo anthu” mosinthana ndi kachitidwe kamodzi ka kulambira. Yesu anakana. (Luka 4:​1-13) Pambuyo pake anthu anafuna kumpanga mfumu, koma Yesu anachoka. (Yohane 6:15) Anadziŵa chimene dongosolo landale zadziko ladziko linali, ndipo anazindikira kuti sichinali chifuniro cha Mulungu kuti iye ayese kulikonza.

9 Yesu anasonyeza kukhulupirika kotheratu kwa Yehova, Mulungu ndi Atate wake. Anakonda njira za Atate wake ndipo nthaŵi zonse anachita zinthu zomkondweretsa. (Yohane 8:29) Anadziŵa kuti zothetsera mavuto a anthu zikadza mwanjira ya Ufumu wa Mulungu, boma lenileni limene likalamulira liri kumwamba ndipo likapereka chitsogozo cholungama ndi chachikondi chofunidwa ndi anthu. Ufumu umenewo wokha ukatha kuchotsa ulamuliro wa Satana ndi ziŵanda zake. Uwo wokha ukatha kugwirizanitsa anthu a mafuko ndi mitundu yonse kukhala banja limodzi ladziko lonse lapansi lokhala mu mtendere. Uwo wokha ukatha kuwonjola anthu ku msinga ya uchimo ndi imfa. Uwo wokha ukatha kubweretsa chimwemwe chosatha kwa anthu. Ufumu umenewu suuli kakonzedwe kena kokhazikitsidwa ndi atsogoleri andale zadziko ndi kudalitsidwa ndi atsogoleri achipembedzo. Akristu owona samatembenukira ku zida zankhondo yokhetsa mwazi kupititsa patsogolo zinthu zake. Ndiboma la Mulungu, lokhala ndi Mfumu yakumwamba yangwiro yokhazikitsidwa pampando wachifumu ndi Mulungu mwiniyo. Uwu ndiwo Ufumu umene Yesu analalikira ndi umene anaphunzitsa omtsatira kuupempha.​—⁠Danieli 2:44; Chivumbulutso 20:​1, 2; 21:​3, 4.

KODI MUDZASANKHA MBALI ITI?

10 Nkhani imene muyenera kuyang’anizana nayo nayi: Kodi mukuvomereza kuti Yehova Mulungu, Mlengi wachilengedwe chonse, alinso Mfumu yake yoyenerera, Wolamulira wake Wamkulu? Kodi mwapeza nthaŵi ya kuphunzira chifuno chake ndi zofunika zake monga momwe zafotokozedwera m’Baibulo? Mwakulemekeza malo ake ndi moyamikira njira zake, kodi mukudzitsikizira kukhala omumvera mwachikondi?​—⁠Salmo 24:​1, 10; Yohane 17:3; 1 Yohane 5:⁠3.

11 Kodi anthu amene amasankha njira ina ngachimwemwepo? Kodi nchiyani chimene chatsatirapo m’kunena kwa Satana kwakuti anthu akapindula mwa kusonyeza kudziimira kwawo m’malo mwa kumvetsera Mulungu. Kukana kuvomereza kuti Mulungu ndiye mwini dziko lapansi ndi kuti anthu onse, monga mbadwa za aŵiri oyambirira, afunikira kukhala abale kwachititsa kuphedwa kwa amuna, akazi ndi ana okwanira mamiliyoni 99 m’zaka za zana lino lokha. Kulephera kugwiritsira ntchito miyezo ya makhalidwe abwino ya Baibulo kwachititsa mabanja osweka, miliri ya nthenda zopatsirana mwa kugonana, kuwonongedwa kwa thanzi kochititsidwa ndi kumwerekera ndi mankhwala ogodomalitsa, ndi upandu wachiwawa. Ngakhale anthu amene amazemba kuphedwa ndi chiwawa amakumanabe ndi imfa chifukwa cha uchimo wolandiridwa kwa Adamu. Umboni wonse ukusonyeza kuti anthu amangodzivulaza ndi awo owakweteza pamene anyalanyaza malamulo anzeru ndi achikondi a Mlengi. (Aroma 5:12; yerekezerani ndi Yesaya 48:​17, 18.) Ndithudi umenewo sindiwo mtundu wa moyo umene mukufuna. Mungasankhe kanthu kena kabwinopo kwambiri.

12 Mwakudandaulira kwachikondi, Baibulo likupereka chiitano chakuti: “Talaŵani, ndipo wonani kuti Yehova ndiye wabwino; wodala munthuyo wa kukhulupirira iye.” (Salmo 34:⁠8) Kuti mutero, muyenera kufika pakudziŵa Yehova ndiyeno kugwiritsira ntchito uphungu wake. Pamene mukutero, moyo wanu uzadzazidwa ndi tanthauzo. Mmalo mwa kupeza nyengo zazifupi za chisangalalo zimene zingakuthandizeni kwakanthaŵi kuiŵala mavuto koma zimene kaŵirikaŵiri zimachititsa chisoni chachikulu pambuyo pake, mudzaphunzira mmene mungalakire mwachipambano mavuto a moyo ndi mmene mungakhalire ndi chisangalalo chosatha. (Miyambo 3:​5, 6; 4:​10-13; 1:​30-33) Mudzakhalanso ndi chiyembekezo cha kulandira madalitso odabwitsa amene adzadza mwanjira ya Ufumu wa Mulungu. Ngati umenewu ndiwo mtundu wa moyo umene mukulakalaka, nkofunika kuchitapo kanthu tsopano. Chifukwa ninji?

MITUNDU YONSE IKUMKA KU ARMAGEDO

13 Yehova sadzalekerera kosatha anthu ndi magulu amene kaya mwadala kapena mwamphwayi amatsatira chitsogozo cha Satana. Iwo sadzaloledwa kupitirizabe kunyoza malamulo a Mulungu, kugwiritsira ntchito dziko lapansi molakwa ndi kuwonongera ena moyo. Iwo akuyang’anizana ndi tsiku la mlandu limene Baibulo limatcha “tsiku lalikulu la Yehova.”​—⁠Zefaniya 1:​2, 3, 14-18.

14 M’chivumbulutso cha zochitika zimene zikachitika mkati mwa masiku otsiriza a dongosolo la zinthu liripoli, Yesu Kristu anaulula kuti: “Mizimu ya ziŵanda” idzamka “kwa mafumu a dziko lonse, kuŵasonkhanitsira ku nkhondo ya tsiku lalikulu la Mulungu Wamphamvuyonse.” Monga momwe chivumbulutso chimenecho chinasonyezera, “anaŵasonkhanitsira kumalo otchedwa m’Chihebri Harmagedo [kapena, Armagedo].” Kusonkhanitsidwa kumeneko tsopano kukuchitika!​—⁠Chivumbulutso 16:​14, 16.

15 Armagedo imene Baibulo limalankhula sindiyo kanthu kena kamene kangapeŵedwe mwa kuletsa nyukliya. Makambitsirano a mitundu yonse sadzailetsa. Mwachiwonekere dzinalo latengedwa ku mzinda wakale wa Megido, koma zambiri zikuloŵetsedwamo koposa malowo m’Middle East. Yosonkhezeredwa ndi “wolamulira wa dziko lino” wosawonekayo, mitundu yonse, mosasamala kanthu za malingaliro awo a ndale zadziko osiyanasiyana, ikusonkhanitsidwira ku mkhalidwe wa dziko lonse umene umasonyeza kutsutsana kwawo ndi Yehova Mulungu. “Mafumu a dziko lonse lokhalidwa ndi anthu,” limodzi ndi otsatira awo onse, akuchititsidwa kutenga kaimidwe kawo. Mwamsanga Armagedo isanakanthe kutsutsa kwawo Ufumu wa Mulungu ndi onse amene amaulalikira kudzakula kwambiri padziko lonse lapansi. Kaya iwo akuzindikira kukhalapo kwa Satana kapena ayi, “dziko lonse ligona mwa woipayo,” monga momwe Mawu a Mulungu akulengezera. Dziko loipa lonse ndi onse amene amalidalira, inde onse amene amatsanzira njira zake, ayenera kupita nalo.​—⁠1 Yohane 5:19; 2:​15-17.

16 Kuyambira pamwamba mpaka pansi, dziko lino ladzazidwa ndi chisalungamo. Siotchuka ndi upandu okha koma nzika zambiri zimasonyeza kunyoza kwaliuma lamulo kwakukulu ndi kusadera nkhaŵa ndi munthu ndi chuma cha munthu mnzawo. Koposa zonse, iwo amakana kulabadira zimene Mulungu mwiniyo akunena m’Mawu ake, Baibulo. Samalemekeza ulamuliro wake. Nkofunika kuti Mulungu achitepo kanthu kuti achotsere dzina lake chitonzo chimene chaunjikidwapo, ndiponso kulambula njira yopangira dziko lapansi kukhala Paradaiso kumene okonda chilungamo adzakhoza kukhala ndi mtendere weniweni ndi chisungiko.

17 Pamene chiwonongeko chidza, sipadzakhala chikaikiro chakuti chikuchokera kwa Yehova. Chipululutso chidzakhala padziko lonse lapansi. Mitundu idzadziŵa kuti Yehova akuchitapo kanthu pamene magulu ake ankhondo akupha ayamba kugwira ntchito. Pamene ulamuliro waboma upasuka, dzanja la munthu aliyense lidzaukira mnzake. Kuchokera kumwamba, Mwana wa Mulungu adzatsogoza chotulukapo.​—⁠Chivumbulutso 6:​16, 17; 19:​11-13; Zekariya 14:⁠13.

18 Mosafanana ndi zotulukapo zankhondo yanyukliya yomenyedwa ndi anthu, chiwonongeko chimenechi sichidzakhala chosasankha. Koma kodi ndani amene adzakhala opulumuka? Kodi iwo adzakhala onse amene akudzinenera kukhala ndi mtundu uliwonse wa chipembedzo, kapena mwinamwake onse amene akudzitcha kukhala Akristu? Yesu anatcha “ambiri” a otero kukhala “ochita kusayeruzika.” (Mateyu 7:​21-23) Opulumuka kuloŵa “m’dziko lapansi latsopano” adzakhala awo okha amene akulitsadi unansi weniweni ndi Yehova ndi Mwana wake mfumuyo, Kristu Yesu. Mwakakhalidwe kawo ndi kuchitira kwawo umboni ponena za Ufumu, adzakhala atasonyeza kuti iwo ndithudi “amadziŵa Mulungu” ndi kuti iwo “amamvera uthenga wabwino wa Ambuye wathu Yesu.” Kodi mukudzisonyeza kukhala munthu wotero?​—⁠2 Atesalonika 1:8; Yohane 17:3; Zefaniya 2:​2, 3.

[Mafunso]

1. (a) Kodi ndinkhani zatsopano ziti zimene zikukulamulira kuganiza kwa anthu ambiri, ndipo kodi nkuti kumene akufunafuna mayankho? (b) Kodi iwo kaŵirikaŵiri amalephera kulingalira chiyani?

2. Kodi nchifukwa ninji mikhalidwe m’dziko iri yoipa kwambiri?

3. Kodi Genesis 2:​16, 17 amasonyeza chiyani ponena za unansi woyenera wa anthu ndi Mulungu?

4. (a) Kodi Satana anachokera kuti? (b) Kodi nchikhumbo cholakwa chiti chimeme iye analola kukula?

5. (a) Kodi ndinkhani ziti zimene zinadzutsidwa m’Edene? (b) Kodi ndani amene akuyambukiridwa nazo?

6. Kodi nchifukwa ninji Yehova sanawononge opandukawo nthaŵi yomweyo?

7. (a) Kodi ndimotani mmene maboma a anthu anayambira? (b) Kodi ndimbiri yotani imene iwo apanga?

8. Kodi nchifukwa ninji Yesu anakana kuloŵetsedwa m’dongosolo landale zadziko ladzikolo?

9. (a) Kuthetsa mavuto a anthu, kodi nchiyani chimene chiyenera kuchitidwa chimene Ufumu wa Mulungu wokha ungachite? (b) Kodi Ufumu umenewo nchiyani?

10. (a) Kodi nchiyani chimene chiri nkhani yaikulu imene aliyense wa ife ayenera kuyang’anizana nayo? (b) Kodi tiyenera kukhala tikuchitanji nayo?

11. Kodi nchifukwa ninji kusankha njira ina sikumabweretsa chimwemwe?

12. (a) Kodi ndichiitano chachikondi chotani chimene Baibulo limapereka kwa ife? (b) Pamene tikugwiritsira ntchito Mawu a Mulungu m’miyoyo yathu mopita patsogolo, kodi tidzawona chiyani?

13. Kodi nchifukwa ninji kuli kofunika kutenga kaimidwe kamphamvu kumbali ya Yehova?

14. Kodi nkuchiyani kumene mitundu yonse tsopano ikusonkhanitsidwirako?

15, 16. (a) Kodi Armagedo nchiyani? (b) Kodi nchifukwa ninji iri yofunika?

17. (a) Kodi chiwonongekocho chidzakhala chokulira motani? (b) Kodi ndani amene adzakhala akutsogolera chotulukapo chake?

18. Kodi opulumuka adzakhala ayani?

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena