Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 2/09 tsamba 1
  • Ntchito Yapadera Yoitanira Anthu ku Chikumbutso

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Ntchito Yapadera Yoitanira Anthu ku Chikumbutso
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—2009
  • Nkhani Yofanana
  • Kugawira Timapepala Toitanira Anthu ku Chikumbutso
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2010
  • Ntchito Yapadera Yoitanira Anthu ku Chikumbutso Idzayamba pa March 17
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2012
  • Ntchito Yogawira Timapepala Toitanira Anthu ku Chikumbutso Idzayamba pa March 22
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2014
  • Ntchito Yogawira Timapepala Toitanira Anthu ku Chikumbutso Idzayamba pa April 2
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2011
Onani Zambiri
Utumiki Wathu wa Ufumu—2009
km 2/09 tsamba 1

Ntchito Yapadera Yoitanira Anthu ku Chikumbutso

1. Kodi ofalitsa za Ufumu padziko lonse adzakhala ndi ntchito yotani kuyambira pa March 21, 2009, ndipo chifukwa chiyani?

1 Lachinayi, pa April 9, 2009, anthu olambira Yehova Mulungu padziko lonse adzasonkhana kuti akumbukire njira yaikulu imene Mulungu anasonyezera chikondi chake pa anthu. (Aroma 5:6-8) Tikukhulupirira kuti pa mwambo wokumbukira imfa ya Yesu umenewu tidzakhala ndi alendo ambiri. Kuyambira pa March 21, 2009, tidzayamba ntchito yapadera yoitanira anthu ku Chikumbutso imene idzachitike padziko lonse lapansi.

2. Kodi ndi mfundo ziti zimene muyenera kukumbukira pogawira kapepala koitanira anthu ku Chikumbutso?

2 Mfundo Zofunika Kuzikumbukira: Gwiritsani ntchito mokwanira zithunzi, mafunso, ndiponso malemba amene ali m’kapepalako. Mwachitsanzo, mungamusonyeze mwininyumba chithunzi chomwe chili kutsogolo kwa kapepalako ndi kumuuza kuti: “Ndikufuna kukuitanirani kumwambo wokumbukira imfa ya Yesu umene udzachitike Lachinayi pa April 9, 2009.” Ndiyeno musonyezeni mutu wa kapepalako komanso mafunso amene ali pamenepowo. Onetsetsani kuti mwamutsimikizira mwininyumbayo kuti akhoza kubwera ndi banja lake komanso anzake.

3. Kodi tizichita chiyani kwa anthu amene tinawaitana kumayambiriro kwa ntchito yapaderayi?

3 Ngati mpingo wanu uli ndi gawo lalikulu, akulu angakonze zoti muzisiya timapepalati pakhomo lomwe simunapezepo anthu. Pa tsiku Loweruka ndi Lamlungu, mungagawire timapepalati limodzi ndi magazini. Onetsetsani kuti mwagawira timapepalati kwa anthu amene mumawayendera pa maulendo obwereza, amene mumaphunzira nawo Baibulo, abale anu, anzanu a kusukulu ndi kuntchito, anthu amene mwayandikana nawo nyumba, ndiponso anthu ena onse owadziwa. Chaka chatha, mlongo wina anaitana abale ake 30 ndipo ankawakumbutsa mobwerezabwereza za kufunika kwa mwambowo. Iye anasangalala kwambiri kuona kuti abale ake 25 anapezeka pa mwambowo ndipo 4 anayamba kuphunzira Baibulo.

4. Kodi panopa tiyenera kukonza zochita chiyani, nanga n’chifukwa chiyani?

4 Konzekerani Panopa: M’mwezi wa March ndi April, ofalitsa ambiri angathe kuonjezera zimene amachita muutumiki. Ngati muli ndi ana kapena anthu amene mumaphunzira nawo Baibulo amene akupita patsogolo, imeneyi ingakhale nthawi yabwino yoti akhale ofalitsa osabatizidwa. Ino ndi nthawi yabwino yoyamba kukonzekera kuti mudzagwire nawo mokwanira ntchito imeneyi yoitanira anthu ku mwambo wokumbukira mmene Mulungu ndi Yesu Khristu anasonyezera chikondi chawo chachikulu kwa ife.—Yoh. 3:16; 15:13.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena