Ndandanda ya Mlungu wa February 16
MLUNGU WOYAMBIRA FEBRUARY 16
□ Phunziro la Baibulo la Mpingo:
cl-CN mutu 14 ndime 13-20 ndi bokosi
□ Sukulu ya Utumiki wa Mulungu:
Kuwerenga Baibulo: Genesis 29-31
Na. 1: Genesis 29:1-20
Na. 2: Chifukwa Chake Sitiyenera “Kudera Nkhawa” (Mat. 6: 25)
Na. 3: Kumvera Kumateteza (lr-CN mutu 7)
□ Msonkhano wa Utumiki:
Mph. 5: Zilengezo.
Mph. 15: “Chitani Zinthu Zonse Kaamba ka Uthenga Wabwino.” Kambiranani mwa mafunso ndi mayankho.
Mph. 15: Kodi Mungachite Upainiya Wothandiza Panyengo ya Chikumbutso? Nkhani yolimbikitsa yokambidwa ndi woyang’anira utumiki. Fotokozani ziyeneretso za apainiya othandiza. Tchulani madalitso amene apainiya othandiza amakhala nawo komanso zimene amasangalala nazo muutumiki. Fotokozani dongosolo lapadera lolowera muutumiki limene mpingo wakonza m’miyezi ya March, April, ndi May. Funsani ofalitsa awiri kapena atatu amene anachita upainiya wothandiza chaka chatha. Kuti athe kuchita upainiya, kodi anasintha chiyani pamoyo wawo? Kodi anapeza madalitso otani? Limbikitsani mabanja kuti akambirane zimene angachite kuti munthu mmodzi kapena angapo m’banjamo achite upainiya wothandiza m’nyengo ya Chikumbutso ikubwerayi.