Ndandanda ya Mlungu wa March 21
MLUNGU WOYAMBIRA MARCH 21
Nyimbo Na. 47 ndi Pemphero
□ Phunziro la Baibulo la Mpingo:
cf mutu 4, ndime 11-18 (Mph. 25)
□ Sukulu ya Utumiki wa Mulungu:
Kuwerenga Baibulo: Yobu 6-10 (Mph. 10)
Na. 1: Yobu 8:1-22 (Osapitirira mph. 4)
Na. 2: Kodi Kukhulupirira Yesu Khristu N’kokwanira Kuti Tidzapulumuke?—rs tsa. 430 ndime 4 (Mph. 5)
Na. 3: Kodi Malangizo a pa Mateyu 10:16 Tingawagwiritse Ntchito Motani? (Mph. 5)
□ Msonkhano wa Utumiki:
Mph. 5: Zilengezo.
Mph. 15: Muzigwiritsa Ntchito Baibulo Poyankha. Nkhani yokambirana yochokera m’buku la Sukulu ya Utumiki, tsamba 143-144. Chitani zitsanzo ziwiri zosonyeza wofalitsa akufunsidwa mafunso amene angakumane nawo m’deralo. M’chitsanzo choyamba, akupereka yankho lolondola koma sakugwiritsa ntchito Baibulo. M’chitsanzo chachiwiri, akugwiritsa ntchito Baibulo poyankha. Pemphani omvera kuti afotokoze chifukwa chimene chitsanzo chachiwiricho chili chabwino kwambiri.
Mph. 15: “Ntchito Yogawira Timapepala Toitanira Anthu ku Chikumbutso Idzayamba pa April 2.” Nkhani ya mafunso ndi mayankho. Gawirani kapepala kamodzi koitanira ku Chikumbutso kwa wofalitsa aliyense, kenako mukambirane zimene zili m’kapepalako. Fotokozani zimene zakonzedwa kuti mugawire kapepalaka m’gawo la mpingo wanu. Chitani chitsanzo chosonyeza kugawira kapepalaka.
Nyimbo Na. 5 ndi Pemphero