Ndandanda ya Mlungu wa February 18
MLUNGU WOYAMBIRA FEBRUARY 18
Nyimbo Na. 123 ndi Pemphero
□ Phunziro la Baibulo la Mpingo:
bt mutu 19 ndime 1-5 ndi bokosi patsamba 149 ndi 150 (Mph. 30)
□ Sukulu ya Utumiki wa Mulungu:
Kuwerenga Baibulo: Maliko 1-4 (Mph. 10)
Na. 1: Maliko 2:18 mpaka 3:1-6 (Osapitirira mph. 4)
Na. 2: Kodi Chiphunzitso cha Purigatoriyo Chinachokera Kuti?—rs tsa. 343 ndime 1-tsa. 344 ndime 3 (Mph. 5)
Na. 3: Kodi Malangizo Amene Paulo Ananena pa 1 Akorinto 7:29-31 Amatanthauza Chiyani? (Mph. 5)
□ Msonkhano wa Utumiki:
Mph. 15: Kutsogolera Anthu Achidwi ku Gulu la Yehova. (Mat. 28:19, 20) Nkhani yokambirana yochokera m’buku la Gulu, kuchokera patsamba 99 ndime 2, mpaka tsamba 101 ndime 2. Limbikitsani abale ndi alongo kuti azichita chidwi ndi anthu pa Nyumba ya Ufumu kuti athandize anthu amene amabwera kumisonkhano koma sanayambe kuphunzira Baibulo ndi Mboni za Yehova.
Mph. 15: “Ntchito Yapadera Yoitanira Anthu ku Chikumbutso Idzayamba pa March 1.” Mafunso ndi mayankho. Patsani aliyense kapepala koitanira anthu ku Chikumbutso, kenako mukambirane zimene zili pakapepalako. Pokambirana ndime yachiwiri, funsani woyang’anira utumiki kuti afotokoze zimene zakonzedwa kuti mugawire timapepalati kwa anthu ambiri m’gawo lanu. Pokambirana ndime yachitatu, chitani chitsanzo chosonyeza mmene tingagawirire timapepalati. Gwiritsani ntchito chitsanzo chimene chili pakamutu kakuti, “Zomwe Tinganene Poitanira Anthu ku Chikumbutso” patsamba 4.
Nyimbo Na. 8 ndi Pemphero