Ndandanda ya Mlungu wa February 25
MLUNGU WOYAMBIRA FEBRUARY 25
Nyimbo Na. 85 ndi Pemphero
□ Phunziro la Baibulo la Mpingo:
bt mutu 19 ndime 6-11 (Mph. 30)
□ Sukulu ya Utumiki wa Mulungu:
Kuwerenga Baibulo: Maliko 5-8 (Mph. 10)
Kubwereza za M’Sukulu ya Utumiki wa Mulungu (Mph. 20)
□ Msonkhano wa Utumiki:
Mph. 5: “Kodi Inunso Muyenera Kutuluka mu Utumiki?” Nkhani yokambirana.
Mph. 10: Uthenga Umene Tiyenera Kulalikira—‘Kuchitira Umboni za Yesu.’ Nkhani yolimbikitsa yochokera m’buku la Sukulu ya Utumiki, kuyambira pakamutu kamene kali patsamba 275 mpaka kumapeto kwa tsamba 278.
Mph. 15: Yehova Amatipatsa Mphamvu Kuti Tizitha Kulalikira. (Afil. 4:13) Funsani ofalitsa awiri kapena atatu amene amalalikira mwakhama ngakhale kuti amadwaladwala kapena ndi okalamba. Kodi amakumana ndi mavuto otani? N’chiyani chimene chimawathandiza kuti asamangokhala odandaula nthawi zonse chifukwa cha mavuto awo. Kodi mpingo wawapatsapo chithandizapo chotani? Kodi apindula chiyani chifukwa cholalikira nthawi zonse?
Nyimbo Na. 42 ndi Pemphero