Kodi Inunso Muyenera Kutuluka mu Utumiki?
Ofalitsa ena ali ndi nthawi imene anazolowera kutuluka mu utumiki wakumunda, mwina 12 koloko masana. M’pomveka kuti ofalitsa ena, malinga ndi mmene zinthu zilili pa moyo wawo, amafunika kutuluka mu utumiki pa nthawi inayake yokhazikika. Koma kodi inunso mumatuluka mu utumiki chabe chifukwa chakuti ofalitsa ena akutuluka, kapena chifukwa choti ofalitsa a m’dera lanu anazolowera kutuluka mu utumiki pa nthawi inayake? N’zotheka kupitiriza kulalikira kwa mphindi zingapo, ngakhale pamene anzanu akutuluka mu utumiki. Mwina mukhoza kuyamba kulalikira m’malo amene mumapezeka anthu ambiri, monga mumsewu. Pobwerera kunyumba kwanu, mungathenso kupita ku maulendo anu obwereza. Taganizirani mmene mungathandizire munthu wachidwi, ngakhale mmodzi yekha, yemwe mungamuyenderenso n’kumupeza pakhomo. Kapena taganizirani mmene mungathandizire anthu amene mwakumana nawo mumsewu n’kuwagawira magazini. Ngati ifeyo tingapitirize kulalikira kwa mphindi zingapo pamene ena akutuluka mu utumiki, ndiye kuti tikuwonjezerera “nsembe” yathu yotamanda Mulungu.—Aheb. 13:15.