Ndandanda ya Mlungu wa March 4
MLUNGU WOYAMBIRA MARCH 4
Nyimbo Na. 45 ndi Pemphero
□ Phunziro la Baibulo la Mpingo:
bt mutu 19 ndime 12-20 ndi bokosi patsamba 152 (Mph. 30)
□ Sukulu ya Utumiki wa Mulungu:
Kuwerenga Baibulo: Maliko 9-12 (Mph. 10)
Na. 1: Maliko 11:19 mpaka 12:1-11 (Osapitirira mph. 4)
Na. 2: Kodi Munthu Akafa Amalangidwabe Chifukwa cha Machimo Ake?—rs tsa. 344 ndime 5-tsa. 345 ndime 1 (Mph. 5)
Na. 3: N’chifukwa Chiyani Munthu Amene Wadzipereka Kwa Mulungu Amakhala Wachimwemwe?—Mac. 20:35 (Mph. 5)
□ Msonkhano wa Utumiki:
Mph. 10: Zimene Munganene Pogawira Magazini M’mwezi wa March. Nkhani yokambirana. Pemphani omvera kuti ayankhe mafunso otsatirawa: Pa masiku a Loweruka ndi Lamlungu tikamagawira timapepala toitanira anthu ku Chikumbutso, kodi n’chiyani chingatithandize kudziwa ngati m’pofunikanso kugawira magazini? Kodi munganene chiyani posintha ulaliki wanu kuchoka ku kapepala kupita ku magazini? Ngakhale kuti m’chitsanzo chilichonse cha zimene tinganene pogawira magazini muli funso komanso lemba, kodi mungatani kuti mufupikitse ulaliki wanu pogawira magaziniwa? Chitani chitsanzo chosonyeza mmene tingagawirire magazini iliyonse pamodzi ndi kapepala koitanira anthu ku Chikumbutso.
Mph. 10: Pindulani ndi kabuku ka Kusanthula Malemba Tsiku ndi Tsiku—2013. Nkhani yokambirana. Fotokozani mwachidule lemba lachaka limene lafotokozedwa patsamba 3 ndi 4. Mufotokozenso kamutu kakuti, “Mmene Mungagwiritse Ntchito Kabukuka,” patsamba 5. Kenako pemphani omvera kuti anene nthawi imene anasankha kuti azipanga lemba la tsiku. Anenenso phindu limene apeza pochita zimenezi. Limbikitsani onse kuti azikambirana lemba la tsiku, tsiku lililonse.
Mph. 10: Zosowa za pampingo.
Nyimbo Na. 119 ndi Pemphero