Purigatoriyo
Tanthauzo: “Mogwirizana ndi chiphunzitso cha Tchalitchi cha [Roma Katolika], ndiwo mkhalidwe, malo, kapena kakhalidwe m’dziko lotsatira . . . kumene miyoyo ya awo amene anafa mu mkhalidwe wa chisomo, koma amene sanawonjokebe kukupanda ugwiro konse, kupanga chitetezo kaamba ka machimo aang’ono osakhululukidwa kapena kaamba ka chilango cha kanthaŵi chifukwa cha machimo aang’ono ndi a kupha amene akhululukidwa kale ndipo mwa kutero amayeretsedwa asanaloŵe kumwamba.” (New Catholic Encyclopedia, 1967, Vol. XI, p. 1034) Sichiri chiphunzitso cha Baibulo.
Kodi chiphunzitso cha purigatoriyo chazikidwa pa chiyani?
Pambuyo pa kupenda zimene olemba Achikatolika anena ponena za malemba monga 2 Amakabeyo 12:39-45, Mateyu 12:32, ndi 1 Akorinto 3:10-15, New Catholic Encyclopedia (1967, Vol. XI, p. 1034) imavomereza kuti: “Potsirizira pake, chiphunzitso cha Katolika cha purigatoriyo nchozikidwa pamwambo, osati pa Malemba Opatulika.”
“Tchalitchi chimadalira pamwambo kuchirikiza malo achikatikati pakati pa kumwamba ndi Helo.”—U.S. Catholic, March 1981, p. 7.
Ponena za mpangidwe wa purigatoriyo, kodi olankhulira Chikatolika amanenanji?
“Ochuluka amalingalira kuti kuvutika konse kwa purigatoriyo nkogwirizanitsidwa ndi kuzindikiridwa kwa kuchedwetsedwa kwa kanthaŵi masomphenya adalitso, ngakhale kuli kwakuti kwakukulukulu lingaliro wamba limati, powonjezera, pali chilango chotsimikizirika . . . Kwakukulukulu m’Tchalitchi Chachilatini kwanenedwa kuti kupweteka uku kumachititsidwa ndi moto weniweni. Komabe, zimenezi siziri zofunikira pa chikhulupiriro cha purigatoriyo. Chiridi chosatsimikizirika. . . . Ngakhale ngati munthu asankha, kukana lingaliro lakuvutika kochititsidwa ndi moto, ndi aphunzitsi Akummaŵa, munthu ayenera kukhala wosamala kusaphatikiza kuvutika kotsimikizirika konse ndi purigatoriyo. Pakali chikhalirebe mazunzo enieni, chisoni, kuwawidwa mtima, manyazi a chikumbumtima, ndi zisoni zina zauzimu zokhoza kudzetsa ululu weniweni pamoyo. . . . Munthuyo ayenera kukumbukira, panthaŵi iriyonse, kuti pakati pa kuvutika kwawo miyoyo imeneyi imakhalanso ndi chisangalalo chachikulu kaamba ka kutsimikizirika kwa chipulumutso.”—New Catholic Encyclopedia (1967), Vol. XI, p. 1036, 1037.
“Zimene zimachitika mu purigatoriyo palibe munthu aliyense akudziŵa.”— U.S. Catholic, March 1981, p. 9.
Kodi moyo umapulumuka imfa ya thupi?
Ezek. 18:4, Dy: “Moyowo [M’Chihebri, neʹphesh; “munthu,” JB; “iye,” NAB: “moyo,” Kx] umene uchimwa, womwewo udzafa.”
Yak. 5:20, JB: “Yense amene angakhoze kubweza wochimwa kunjira yolakwa imene watenga adzakhala akupulumutsa moyo ku imfa ndi kukwirira unyinji wa machimo.” (Kanyenye wawonjezeredwa.) (Tawonani kuti apa pakunena za imfa ya moyo.)
Kamba ka maumboni owonjezereka, wonani mutu wakuti “Imfa” ndi “Moyo Soul.”
Kodi chilango chowonjezereka kaamba ka uchimo chimaperekedwa pambuyo pa imfa ya munthuyo?
Aroma 6:7, NAB: “Munthu amene wafa wamasuka ku uchimo.” (Kx: “Liwongo silimawonekanso pa munthu amene ali wakufa.”)
Kodi akufa ali okhoza kupeza chisangalalo chifukwa cha chikhulupiriro m’chiyembekezo cha chipulumutso?
Mlal. 9:5, JB: “Kwakukulukulu a moyo amadziŵa kuti adzafa, akufa sadziŵa chirichonse.”
Yes. 38:18, JB: “Sheoli samakutamandani inu [Yahweh], imfa simakulemekezani inu; awo amene atsikira kudzenje samapitirizabe kuika chidaliro m’kukhulupirika kwanu.” (Chotero kodi ndimotani mmene aliyense wa iwo “angakhalire ndi chisangalalo chachikulu chifukwa cha kutsimikizirika kwa chipulumutso”?)
Mogwirizana ndi kunena kwa Baibulo, kodi kuyeretsedwa kuuchimo kumachititsidwa ndi chiyani?
1 Yoh. 1:7, 9, JB: “Ngati tikhala ndi moyo m’kuunika, monga iye [Mulungu] ali m’kuunika, tiri m’chigwirizano wina ndi mnzake, ndipo magazi a Yesu, Mwana wake, amatiyeretsa muzoipa zonse. . . . Ngati tivomereza machimo athu, pamenepo Mulungu amene ali wokhulupirika ndi wolungama adzakhululukira machimo athu ndi kutiyeretsa ku chinthu chirichonse cholakwa [“zolakwa zathu zonse zimayeretsedwa,” Kx].”
Chiv. 1:5, JB: “Yesu Kristu . . . amatikonda ndipo watsuka zoipa zathu ndi mwazi wake.”