Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • ts mutu 7 tsamba 60-70
  • Kodi Akufa Amafuna Chithandizo Chanu?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Akufa Amafuna Chithandizo Chanu?
  • Kodi Moyo Uno Ndiwo Wokha Umene Ulipo?
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • KUKHULUPIRIRA PURIGATORIYO KWA CHIKRISTU CHA DZIKO
  • Kodi Mawu Oti Puligatoliyo Amapezeka M’Baibulo?
    Kuyankha Mafunso a M’Baibulo
  • Purigatoriyo
    Kukambitsirana za m’Malemba
  • Kodi Mungathe Kuthandiza Anthu Akufa?
    Galamukani!—2006
  • Zowonadi Ponena za Helo
    Nsanja ya Olonda—1989
Onani Zambiri
Kodi Moyo Uno Ndiwo Wokha Umene Ulipo?
ts mutu 7 tsamba 60-70

Mutu 7

Kodi Akufa Amafuna Chithandizo Chanu?

“KUTUMIKIRA awo amene tsopano ali akufa monga ngati kuti ali moyo,” umatero mwambi wakale Wachichaina, “ndiko chochita chapamwamba kopambana cha kulemekeza kweni-kweni kwachikondi.” Ngati akufa aliko’di m’dziko lina ndipo angathe kupindula ndi mautumiki a awo otsala pa dziko lapansi, chikakhala chinthu chachikondi kusonyeza kudera nawo nkhawa.

Ndithudi, anthu ambiri amangotsatira kusunga miyambo yakale, ngakhale kuli kwakuti sali kweni-kweni okhulupirira zolimba kukhalako kopitirizabe pambuyo pa imfa. Koma ena ali okhutiritsidwa maganizo kuti akufa amafuna chithandizo chao.

Anthu mamiliyoni ochuluka mu Asiya monse ndi mbali zambiri za Afirika amakhulupirira kuti iwo ayenera kupereka ulemu kwa makolo akufa kwa moyo wao wonse. Pamaso pa miyala ya pa manda a makolo a achibale ao akufa, iwo amaocha lubani, kupemphera, kuika maluwa ndipo ngakhale kupereka zakudya. Kumalingaliridwa kuti kulemekeza kotero’ko kudzathandiza akufa kusangalala ndi kukhala ndi moyo kosangalatsa m’moyo wina’wo ndi kuwaletsa kukhala mizimu yaudani.

Maka-maka mogwirizana ndi kulira maliro ndi maliro otsala’wo amapanga zoyesa-yesa zoonongetsa ndalama kwambiri kuthandiza akufa. Lingalirani machita-chita amwambo otsatirapo’wa amene anachitidwa Kum’mawa pa imfa ya phungu wa boma wochuka:

Ansembe Achibuda anachita madzoma’wo. Makombola anaphulitsidwa kuti athamangitse mizimu yoipa. Pepala lampunga lokhala ndi mapemphero linaochedwa, akumakhulupirira kuti zimene’zi zikapindulitsa mzimu wa munthu wakufa’yo. Chakudya, mowa ndi fodya zinaikidwa pafupi ndi mtembo’wo kotero kuti mzimu ukathe kusangalala nazo pali ponse pamene unasankha kutero.

Pambuyo pake mtembo’wo unaikidwa m’bokosi la maliro, limene linakhalabe m’chipinda cha nyumba ya maliro’yo kwa masiku makumi anai mphambu asanu ndi anai. Kwa masiku asanu ndi limodzi mwana wamwamuna wamkulu koposa onse analira pamene’po. Pa tsiku lachisanu ndi chiwiri iye anabwerera kunyumba kukagona, kusamba ndi kusintha zobvala. Nyengo ya masiku asanu ndi limodzi ya kulira maliro ndi tsiku limodzi la kupuma kenako inabwerezedwa kwa nthawi yonse ya masiku makumi anai mphambu asanu ndi anai. Popanda kulekeza konse m’nyengo yonse’yo, makombola anaphulitsidwa, pamene zitoliro, ng’oma ndi nguli yopfuula zinaimbidwa usana ndi usiku.

Tsiku la makumi anai mphambu asanu ndi anai linali ndi mpingo wa maliro wadzaoneni. Magulu oyimba anayimba. M’njira monse makombola omangiriridwa ku nsichi za telefoni, nsichi za magetsi ndi mitengo anaphulitsidwa. Zakudya, mowa ndi fodya zinaikidwa pa matebulo a guwa lansembe, ndi pepala lokhala ndi mapemphero, kudza’nso malubani, zinaochedwa m’tiakachisi tokhazikitsidwa m’njira monsemo. Kuulutsidwa kokongola kwa mapepala, masamba agolidi ndi nsungwi zinaonjezera kukongola kwa mpingo wa olira maliro. Ambiri a olira maliro’wo ananyamula nyali, chifuno cha nyali zotero’zo chikumakhala kuunikirira njira mzimu wa munthu wakufa’yo. Pa mbali pa manda zoulutsidwa zokongola zamapepala zosonyeza, mphala, ndege, sitima zam’madzi, magulu ankhondo, atumiki ndi zinthu zina, zinaochedwa.

Ponena za anthu okhala ndi chuma chochepera ndi osachuka kwambiri, njira zofanana’zo simatsatiridwa koma pa mlingo wochepera kwambiri. Mwa chitsanzo, zinthu zamapepala zowerengeka ndi zosakongola kwambiri zimaochedwa.

Kukhulupirira purigatoriyo ndiko maziko akulu a kuochedwa kwa zinthu zamapepala kotero’ko. Pambuyo pa imfa ya munthu, mzimu umakhulupiriridwa kukhala ukuyenda-yenda m’purigatoriyo kwa zaka ziwiri, koma wofuna chithandizo kuti ulowe kumwamba. Nsembe zoperekedwa mu mpangigwe wa zinthu zamapepala zimalinganizidwa kusonyeza kuti munthu wakufa’yo anakhala ndi moyo wabwino ndipo ali chiri chonse chofunika kupitirizabe m’dziko lina’lo. Zimene’zi pokhala choncho, Achaina ambiri amakhulupirira kuti, mzimu wake uyenera kumasulidwa m’purigatoriyo mwamsanga.

Kodi inu mumachita motani ndi madzoma okongola ndi oonongetsa ndalama kwambiri otero’wo? Kodi inu mukakhala ndi phande m’machita-chita ofanana’wo? Ngati ndi choncho, chifukwa ninji?

Ngati mumakhulupirira kuti akufa amafuna chithandizo chanu, kodi ndi umboni wotsimikizirika wotani umene muli nao wakuti kanthu kena kodziwa kamapulumuka imfa ya thupi? Kodi n’chiani chimene chimakupangitsani kukhala otsimikizira kuti njira zogwiritsiridwa ntchito kuthandiza akufa’zo ziri zamphamvu? Mwa chitsanzo, kodi ndi motani m’mene munthu, angatsimikizirire kuti nyali zimaunikirira njira mzimu, kuti makombola amathamangitsa mizimu yoipa ndi kuti zinthu zamapepala zoochedwa zingathandize mzimu wa wakufa’yo kulowa madalitso akumwamba? Kodi pali maziko otani onenera kuti zinthu zotero’zo ziri njira zamphamvu zothandizira mizimu ya akufa?

Pamene kuli kwakuti madzoma achipembedzo othandiza akufa angakhale osiyana kwambiri m’dera lanu, kodi ali yense angakutsimikizireni mokhutiritsa kuti zimene zimachitidwa zimadzetsa zotulukapo zopindulitsa?

Kuli’nso, kopindulitsa, kulingalira ukulu wa chilungamo ndi ubwino zimene zikupezeka m’zoyesa-yesa zothandiza akufa zimene’zi. Awo amene ali ndi chuma chochuluka mwachizolowezi angagule makombola ochuluka, zinthu zamapepala kapena zinthu zina zolingaliridwa kuthandiza akufa. Pamenepa, bwanji, munthu wosauka? Ngakhale kuli kwakuti angakhale atakhala ndi moyo wabwino, akakhala wopanda mwai ngati ali yense sanachita kanthu kali konse pambuyo pa imfa yake. Ndipo’nso, munthu wosauka amene amagula zinthu kuti athandize akufa amabvutika ndi katundu wamkulu wandalama, pamene munthu wolemera amangoyambukiridwa pang’ono chabe.

Kodi mumamva bwanji ndi tsankho lachoonekere lotero’lo? Kodi mukakokeredwa kwa mulungu amene akayanja olemera koposa osauka popanda kulingalira chimene iwo ali monga anthu? Mulungu wa Baibulo samasonyeza tsankho lotero’lo. Ponena za iye, Malemba Oyera amati: “Mulungu alibe tsankhu.”—Aroma 2:11.

Tsopano tinene kuti munthu anazindikira kuti madzoma achipemedzo ochitiridwira akufa anali opanda pake, osagwirizana kotheratu ndi chifuniro cha Mulungu wopanda tsankho. Kodi kukakhala kwanzeru kwa iye kuwachita chifukwa cha mwambo chabe ndi kupewa kukhala wosiyana ndi anansi ake? Kodi n’kwanzeru kuchirikiza madzoma achipembedzo amene munthu amawalingalira kukhala chinyengo? Kodi n’koyenera kugwirizana ndi kanthu kena kamene kamayanja olemera ndi kuika bvuto pa osauka?

KUKHULUPIRIRA PURIGATORIYO KWA CHIKRISTU CHA DZIKO

Chikhulupiriro chakuti akufa amafunikira chithandizo kuti atuluke m’purigatoriyo sichiri ku zipembedzo zosakhala Zachikristu zokha. The New Catholic Encyclopedia imalongosola kuti:

“Miyoyo yokhala m’purigatoriyo ingathandizidwe ndi ntchito za kulemekeza, monga ngati pemphero, zipepala zokhulukira machimo, mphatso zachifundo, kusala kudya ndi nsembe. . . . Pamene kuli kwakuti munthu sangalamule kuti Mulungu agwiritsire ntchito phindu lokhutiritsa la ntchito zake kwa miyoyo yosauka, iye angayembekezere’di kuti Mulungu adzamva zopempha zake ndi kuthandiza ziwalo zobvutika za Chalichi.”

Kodi ndi chitsimikiziritso champhamvu chotani chimene chikuperekedwa chakuti zoyesa-yesa zotero’zo zidzadzetsa phindu? Encyclopedia’yo ikupitirizabe kuti:

“Chifukwa chakuti kugwiritsiridwa ntchito kwa ntchito zabwino zimene’zi kumadalira pa kupempha kwa munthu kwa Mulungu, palibe chitsimikiziro chosalakwa chakuti mapemphero a munthu amathandiza moyo umodzi wokhala m’purigatoriyo, kapena uli wonse wa iyo, pa nthawi yomweyo. Koma chifundo ndi chikondi cha Mulungu kaamba ka miyoyo yokhala m’purigatoriyo, imene iri kale pafupi kwambiri ndi Iye, ndithudi zimam’sonkhezera kufulumizitsa kumasulidwa kwao m’nyengo ya kuyeretsa pamene okhulupirika pa dziko lapansi apereka mapemphero ao ku chifuno chimene’chi.”

Motero palibe chitsimikiziro cheni-cheni chimene chikuperekedwa chakuti zinthu zochitiridwa awo okhulupiriridwa kukhala ali m’purigatoriyo zimachita’di kanthu. Ndipo palibe maziko operekera chitsimikiziro chotero, pakuti Baibulo silimapereka. Iro liribe n’komwe liu’lo “purigatoriyo.” New Catholic Enclopedia imabvomerezo kuti: “M’kupenda kotsirizira, chiphunzitso Chachikatolika chonena za purigatoriyo chazikidwa pa mwambo, osati Malemba Opatulika.—Vol. 11, p. 1034.

Zoonadi, mwambo si woipa kweni-kweni. Koma mwambo umene’wuwu ndi wosagwirizana ndi Mau a Mulungu. Malemba samaphunzitsa kuti “moyo” umapulumuka imfa ya thupi. Pamenepa, mwachionekere, uwo sungakhale wofunikira nyengo ya kuyeretsedwa m’purigatoriyo. Chifukwa cha chimene’cho, mau a Yesu Kristu kwa atsogoleri achipembedzo Achiyunda angathe moyenerera kulunjikitsidwa kwa awo ophunzitsa chiphunzitso cha purigatoriyo: “Inu mupeputsa mau a Mulungu chifukwa cha miyambo yanu. Onyenga inu! Yesaya ananenera bwino za inu, ndi kuti, Anthu awa andilemekeza Ine ndi milomo yao; koma mtima wao uli kutali ndi Ine. Koma andilambira Ine kwachabe, ndi kuphunzitsa maphunzitso, malangizo a anthu.”—Mateyu 15:6-9.

Lingalirani’nso njira zothandizira awo amene ali m’purigatoriyo, mothandizidwa ndi zimene zimaphunzitsidwa m’Malemba Oyera. Monga momwe kwasonyezedwera mu New Catholic Encyclopedia, pemphero ndi imodzi ya ntchito za kulemekeza imene moyerekezera ingathandize miyoyo yokhala m’purigatoriyo. Ponena za mapemphero otero’wo, kabuku kochedwa Assist the Souls in Purgatory (kofalitsidwa ndi Benedictine Convent of Perpetual Adoration) kamati:

“Pemphero lalifupi koma lotenthedwa maganizo kawiri-kawiri limakhala la phindu lalikulu kwambiri kwa miyoyo yobvutika koposa mpangidwe wotalikitsidwa wa pemphero umene sumalabadiridwa. Ochuluka ali mapemphero afupi operekedwa ku amene Chalichi chapereka zikhululukiro za machimo, onse amene ali ogwira ntchito kwa miyoyo yobvutika . . . Ha, ndi mosabvuta chotani nanga m’mene tingachulukitsire mibvi yaing’ono yonga moto ya pemphero imene’yi m’kati mwa tsiku pamene tikugwira ntchito zosiyana-siyana, ndipo ngakhale pamene manja athu ali otanganitsidwa ndi ntchito ina! . . . Ha, ndi miyoyo yochuluka chotani nanga imene sitikanaipumuza kapena kuimasula ku purigatoriyo ngati nthawi ndi nthawi m’kati mwa tsiku sitikanapereka pemphero lalifupi lokhoza kukhululukira machimo la Chalichi limene’li lopempherera akufa: ‘Muwapatsetu mpumulo, O Ambuye, ndipo lolani kuwala kosatha kuwawalire. Akhaletu mu mtendere. Amen.’ (Chikhululukiro cha machimo cha masiku 300 pa nthawi iri yonse. ‘Bukhu la Zikhululukiro za machimo,’ 582.) Ngati tibwereza kupemphera motenthedwa maganizo maina oyera, a ‘Yesu, Mariya ndi Yosefe’ chikhululukiro cha machimo cha zaka zisanu ndi ziwiri chingapezedwe pa nthawi iri yonse.”

Kodi sikukuonekera kukhala kodabwitsa kwa inu kuti kubwerezedwa kwa maina atatu kukakhala ndi mphamvu yowirikiza kasanu ndi katatu koposa pemphero lotalikirapo, la mau makumi awiri? Kodi kubwerezedwa kwa pemphero kawiri-kawiri ndiko kumene Mulungu amakubvomereza? Ponena za kumene’ku Yesu Kristu anati: “Popemphera musamabwereza-bwereza chabe iai, monga amachita anthu akunja, chifukwa ayesa kuti adzamvedwa ndi kulankhula-lankhula kwao. Chifukwa chake inu musafanane nao.”—Mateyu 6:7, 8.

M’malo mwa kunena kwanu mobwereza-bwereza mau olowezedwa, Baibulo limalimbikitsa pemphero la mau ochokera mu mtima.

Chosati n’kunyalanyazidwa ndicho mbali imene ndalama zakhala nayo mogwirizana ndi chiphunzitso cha purigatoriyo. Ndithudi, kungatsutsidwe kuti kukondweretsedwa ndi kupezera ndalama chalichi sindiko chifukwa cha chiphunzitso chimene’cho. Koma chimene’chi sichikusintha cheni-cheni chakuti magulu achipembedzo amene amachirikiza chiphunzitso cha purigatoriyo amakondweretsa kulandira nsembe za zinthu zakuthupi. Palibe ali yense amene amadzudzulidwa ndi chalichi chifukwa cha kuyesa kugula kutuluka kwake kapena kwa munthu wina m’purigatoriyo. Palibe ali yense amene amalangizidwa ndi chalichi kuti kukakhala bwino kwambiri kwa iye kugwiritsira ntchito chuma chake chakuthupi chochepa’cho kaamba ka zofunika za moyo. Kwa zaka mazana ochuluka olemera ndi osauka mofanana akhala akudzaza mabokosi a ndalama a magulu achipembedzo moyembekezera kuchepetsa nthawi imene iwo kapena okondedwa ao angakhale m’purigatoriyo. Wolemba Corliss Lamont, m’bukhu lake lakuti The Illusion of Immortality akunena kuti:

“Madzoma achipembedzo ogwirizanitsidwa ndi akufa atanthauza chuma chosaneneka ku Chalichi. Maka-maka zimene’zi zakhala choncho m’Chiroma Katolika ndi m’zipembedzo Zakum’mawa za Orthodox kumene chigogomezero chochuluka chimaikidwa pa misa, mapemphero ndi ntchito zina zabwino zochitiridwa akufa, omafa ndi awo amene m’njira iri yonse ali odera nkhawa ndi mkhalidwe wao wam’tsogolo.

“Chiyambire kuchiyambi-yambi kwa Zaka za Zana la Khumi ndi chimodzi Chalichi Chachikatolika chapeza, mwa kupereka zipepala zokhululukira machimo kokha, ndalama zochukula kwambiri kuchokera kwa olemera ndi osauka mofanana. Zipepala zokhululukira machimo zimene’zi zoperekedwa mosinthanitsa ndi malipiro a ndalama, kupereka mphatso zachifundo kapena mitundu ina ya zopereka, zimakhala zakuti moyo wake kapena moyo wa wachibale wakufa kapena bwenzi upulumutsidwe chonse kapena mbali ya chilango chake choikidwiratu m’purigatoriyo . . . Mu Rasha Chalichi cha Orthodox chakundika chuma chochuluka kwambiri mwa mapemphero ofanana’wo opempherera akufa. Kuphatikiza pa ndalama za nthawi ndi nthawi zopezedwa kuchokera kwa ogwira ntchito ndi alimi ofunitsitsa kuchepetsa chilango chaumulungu, ziwalo zambiri za olemekezeka ndi apamwamba zalipira ndalama kumalo okhala ansembe ndi machalichi kuti mapemphero a tsiku ndi tsiku aziperekedwera miyoyo ya akufa ao.”

Ngati zikanakhala zoona kuti zopereka za zinthu zakuthupi zotero’zo zinapindulitsa’di akufa, zimene’zi zikanatanthauza kuti Mulungu ndi wokondweretsedwa ndi ndalama. Koma iye samafuna ndalama kapena chuma chakuthupi cha ali yense. Ponena kupyolera mwa wamasalmo wouziridwa, Mulungu akulengeza kuti: “Sindidzatenga ng’ombe m’nyumba mwako, kapena mbuzi m’makola mwako. Pakuti zamoyo zonse za kuthengo ndi zanga, ndi ng’ombe za pa mapiri zikwi. Ndidziwa mbalame zonse za m’mapiri: ndipo nyama za kuthengo ziri ndi Ine. Ndikamva njala, sindidzakuuza: pakuti dziko lonse ndi langa, ndi kudzala kwake komwe.”—Salmo 50:9-12.

Ndithudi, chuma chonse cha m’dziko sichingathandize munthu wakufa. Ndalama ndi chuma chakuthupi sizingam’letse’di kufa. Monga momwe Baibulo limanenera kuti: “Iwo akutama kulemera kwao; nadzitamandira pa kuchuluka kwa chuma chao; kuombola mbale sangadzamuombole, kapena kum’perekera dipo kwa Mulungu: (Popeza chiomboledwe cha moyo wao n’cha mtengo wapatali, ndipo chilekeke nthawi zonse kuti akhale ndi moyo osafa, osaona chibvundi.”—Salmo 49:6-9.

Sipangakhale chikaikiro kuti zoyesa-yesa za kuthandiza akufa ziri zopanda malemba. Chiphunzitso chakuti akufa angathe kuthandizidwa ndi amoyo changoika katundu wolemera pa anthu. Komabe, chidziwitso cha Mau a Mulungu, chimamasula munthu ku lingaliro lonyenga limene’li. Chimene’chi chingatipatse chisonkhezero cheni-cheni kuti tichite zomwe tingathe pamene ziwalo za banja lathu zikali ndi moyo kuzipangitsa kuona kuti izo zikufunidwa, kukondedwa ndi kuyamikiridwa. Pambuyo pa imfa yao ndi m’mbuyo mwalendo kwa munthu ali yense kukwichiza machitidwe onyalanyazidwa a kukoma mtima ndi kulingalira.

[Chithunzi patsamba 64]

Madzoma Achitao, onenedwa kukhala akumasula moyo ku purigatoriyo

[Chithunzi patsamba 65]

Madzoma Achikatolika, onenedwa kukhala akuthandiza miyoyo yokhala m’purigatoriyo

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena