Kubwereza za M’Sukulu ya Utumiki wa Mulungu
Mafunso otsatirawa tidzawakambirana pa Sukulu ya Utumiki wa Mulungu ya mlungu woyambira February 25, 2013. Taika tsiku limene likusonyeza mlungu umene mfundoyo idzakambidwe n’cholinga choti muthe kufufuza pamene mukukonzekera sukulu mlungu uliwonse.
1. N’chifukwa chiyani Yesu ananena kuti “anthu amene akumva chisoni” ndi odala? (Mat. 5:4) [Jan. 7, w09 2/15 tsa. 6 ndime 6]
2. Kodi Yesu ankatanthauza chiyani m’pemphero la chitsanzo limene anaphunzitsa ophunzira ake kuti: “Musatilowetse m’mayesero”? (Mat. 6:13) [Jan. 7, w04 2/1 tsa. 16 ndime 13]
3. N’chifukwa chiyani Yesu ananena kuti ophunzira ake sadzamaliza kulalikira kuzungulira mizinda yonse “Mwana wa munthu asanafike”? (Mat. 10:23) [Jan. 14, w10 9/15 tsa. 10 ndime 12; w87 8/1 tsa. 8 ndime 6]
4. Kodi fanizo la Yesu lonena za kanjere ka mpiru limanena za zinthu ziwiri ziti? (Mat. 13:31, 32) [Jan. 21, w08 7/15 tsa. 17-18 ndime 3-8]
5. Kodi Yesu ankafuna kuphunzitsa ophunzira ake chiyani pamene ananena kuti: “Mukapanda kutembenuka n’kukhala ngati ana aang’ono, simudzalowa mu ufumu wakumwamba”? (Mat. 18:3) [Jan. 28, w07 2/1 tsa. 9-10 ndime 3-4]
6. Kodi Yesu ankatanthauza chiyani pamene anati “mwanena nokha”? (Mat. 26:63, 64) [Feb. 11, w11 6/1 tsa. 18]
7. N’chifukwa chiyani Yesu akutchedwa “Mbuye wa sabata”? (Maliko 2:28) [Feb. 18, w08 2/15 tsa. 28 ndime 7]
8. N’chifukwa chiyani Yesu anayankha chonchi zokhudza mayi ake komanso abale ake ndipo ifeyo tikuphunzirapo chiyani? (Maliko 3:31-35) [Feb. 18, w08 2/15 tsa. 29 ndime 5]
9. Malinga ndi zimene zili palemba la Maliko 8:22-25, n’chifukwa chiyani Yesu anachita zinthu ziwiri pochiritsa munthu wakhungu, ndipo tikuphunzirapo chiyani? [Feb. 25, w00 2/15 tsa. 17 ndime 7]
10. Kodi tikuphunzira chiyani pa zimene Yesu anachita Petulo atamudzudzula pa Maliko 8:32-34? [Feb. 25, w08 2/15 tsa. 29 ndime 6]