Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w87 8/1 tsamba 8-9
  • Phunziro M’chifundo

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Phunziro M’chifundo
  • Nsanja ya Olonda—1987
  • Nkhani Yofanana
  • Phunziro m’Chifundo
    Munthu Wamkulu Woposa Onse Amene Anakhalako
  • Anawaphunzitsa Kukhululukira Ena
    Yesu—Ndi Njira, Choonadi ndi Moyo
  • Mafunso Ochokera kwa Owerenga
    Nsanja ya Olonda—2010
  • Yesu Anakadya Chakudya ku Nyumba kwa Simoni ku Betaniya
    Yesu—Ndi Njira, Choonadi ndi Moyo
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1987
w87 8/1 tsamba 8-9

Moyo ndi Uminisitala za Yesu

Phunziro M’chifundo

YESU angakhale adakali ku Naini, kumene iye posachedwapa anaukitsa kwa akufa mwana wamwamuna wa mkazi wa masiye, kapena mwinamwake iye akuchezera mizinda yapafupi. M’farisi wotchedwa Simoni akukhumba kumuwo nera chapafupi amene akupanga ntchito zozizwitsa zimenezi. Chotero iye akumuitana Yesu kuti akadye limodzi naye.

Kuiwona nthawiyi monga mwawi wakulalikira kwa awo omwe alipo, Yesu akuvomereza chiitanocho monga momwe iye anavomerezera ziitano kukadya ndi okhometsa msonkho ndi ochimwa. Komabe, pamene iye alowa m’nyumba ya Simoni, Yesu sakulandira chisamaliro chaubwenzi chomwe kawirikawiri chimaperekedwa kwa alendo.

Mapazi ovala nsapato zazingwe amatentha ndi kuda chifukwa cha kuyenda mu misewu ya fumbi ya mu Galileya, ndipo uli mwambo wa kachitidwe ka ufulu kusambitsa mapazi a alendo ndi madzi ozizira. Koma mapazi a Yesu sanasambitsidwe pamene iye wafika. Sanalandirenso ku psyompsyonedwa kwa kulandiridwa, komwe kali kachitidwe kofala. Ndipo mwambo wa ufulu wakutsira mafuta sunaperekedwe kaamba ka tsitsi lake. Mkati mwa kudya chakudya, pamepe alendo adakali kuseyama pagome, mkazi wosaitanidwa akulowa mwa kachetechete m’chipindamo. lye ali wodziwika kwambiri mu mzinda kaamba ka makhalidwe ake ochimwa. Mwachidziwikire iye wamva za ziphunzitso za Yesu, kuphatikizapo chiitano chake kaamba ka ‘onse akulema kudza kwa iye kaamba ka mpumulo.’ Ndipo kukhala atafulumizidwa mozama ndi zimene wawona ndi kumva, iye tsopano wamufunafuna Yesu.

Mkaziyo akubwera kumbuyo kwa Yesu pagome ndi kugwada pansi pa mapazi ake. Pamene misozi yake inagwa pa mapazi ake, iye akuipukuta ndi tsitsi lake, lye akutenganso mafuta ake onunkhira bwino kuchokera mu nsupa yake, ndipo pamene apsyompsyonetsa mapazi ake, iye akuthira mafutawo pa iwo. Simoni akuyang’ana mosavomereza. “Akadakhala mneneri uyu,” iye akulingalira, “akadazindikira ali yani ndipo ndi wotani mkaziyo womkhudza iye chifukwa ali wochimwa.”

Kuzindikira malingaliro ake, Yesu akuti: ‘‘Simoni, ndiri ndi kanthu ka kunena kwa iwe.”“Mphunzitsi, nenani!” iye ayankha.

“Munthu wokongoletsa ndalama anali nawoamangawa awiri,“ Yesu ayamba. “Mmodziyo anali ndi mangawa ake amalupiya mazana asanu, koma mnzake makumi asanu. Popeza analibe chobwezera iwo anawakhululukira onse awiri. Chotero, ndani wa iwo amene adzaposa kumkonda?”

“Ndiyesa kuti,” akutero Simon, mwina mwake Moyo ndiUminisitala za Yesu wokhala ndi malingaliro osiyana ponena za funso lowoneka losagwirizanalo, “iye amene anamukhululukira zoposa.”

“Waweruza bwino,” atero Yesu. Ndipo kenaka kutembenukira kwa mkazi, iye akumuuza Simoni: “Upenya mkazi ameneyu kodi? Ndinalowa mnyumba yako, sunandipatse madzi kusambitsa mapazi anga; koma uyu anakonkha mapazi anga ndi misozi, nawapukuta ndi tsitsi lake. Sunandipatsa mpsyompsyono wachibwenzi; koma uyu sanaleke kupsyompsyonetsa mapazi anga chilowere muno ine. Sunandidzoza mutu wanga ndi mafuta; koma uyu anadzoza mapazi anga ndi mafut onunkhira bwino.”

Mkaziyo mwakutero anapereka chitsimikiziro cha kulapa kochokera mu mtima kaamba ka kuchimwa kwake kwapita. Chotero Yesu akumaliza: “Chifukwa chake, ndinena kwa iwe, machimo ake ndiwo ambiri akhululukidwa; chifukwa anakonda kwambiri; koma munthu amene anamkhululukira pang’ono, iye akonda pang’ono.”

Yesu mu njira iriyonse sakukhululukira kapena kuzengeleza khalidwe loipa. M’malo mwake, chochitika chimenechi chikuvumbula kumvetsetsa kwake kwa chifundo kwa anthu omwe amapanga zolakwa m’moyo koma omwe pambuyo pake amatsimikizira kuti ali achisoni kaamba ka zimenezi ndipo mwakutero kudza kwa Yesu kaamba ka mpumulo. Kupereka mpumulo weniweni kwa mkaziyo, Yesu akuti: “Machimo ako akhululukidwa. “. . . Chikhulupiriro chako chakupulumutsa iwe, muka ndi mtendere.” Luka 7:36-50; Mateyu 11:28-30.

◆ Kodi ndimotani mmene Yesu walandiridwira ndi womchereza wake Simoni?

◆ Ndi ndani amene akufunafuna Yesu, ndipo nchifukwa ninji?

◆ Kodi ndi fanizo lotani limene Yesu wapereka, ndipo ndimotani mmene iye waligwiritsira ntchito?

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena