Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w87 8/1 tsamba 7
  • Mphatso Yapadera ya Ana

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Mphatso Yapadera ya Ana
  • Nsanja ya Olonda—1987
  • Nkhani Yofanana
  • “M’kamwa mwa Makanda”
    Nsanja ya Olonda—1995
  • Ana Amene Amatamanda Mulungu
    Kumamumvetsera Mphunzitsi Wamkuru’yo
  • Ananu, Tamandani Yehova!
    Nsanja ya Olonda—2005
  • Achinyamata Amene Amatamanda Yehova Amakhala ndi Moyo Wabwino
    Nsanja ya Olonda—2005
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1987
w87 8/1 tsamba 7

Mphatso Yapadera ya Ana

CHISONYEZERO chofunitsitsa cha ana kaŵirikaŵiri chimapangitsa achikulire kuima ndi kuganizira. Pachochitika chimodzi, pambuyo pa kuwona Yesu akuchita zozizwitsa zina zake, anyamata anayamba kufuula: “Hosana kwa Mwana wa Davide!” Atsogoleri achipembedzo anatsutsa ichi. Ochititsidwa khungu ndi nsanje, iwo sakanazindikira kuti Yesu anali mbadwa ya Umesiya ya Mfumu Davide. Koma Yesu anayankha iwo ndi kunena: “Simunawerenga kodi, ‘M’kamwa mwa makanda ndi oyamwa munafotokozera zolemekezeka’?”(Mateyu21:15, 16)Lerolino, Mulungu adakagwiritsira ntchito “pakamwa pa makanda” kuthandiza awo amene malingaliro awo ali ochititsidwa khungu ndi chiphunzitso chonyenga.​—2 Akorinto 4:4.

◻ Daleen, wa zaka 12, anadzitsimikizira iyemwini kukhala msungwana wathayo ku sukulu. Tsiku lina iye anagawiridwa kusunga kalasi yotanganitsidwa pamene mphunzitsi wake anali kuchita ntchito ina. Kodi nchiyani chimene iye akanachita? “Ndinalingalira kulongosola kwa anzanga a m’kalasi kuti anthu olungama adzakhala kosatha padziko lapansi ndi kuti aliyense sadzapita kumwamba,” anatero Daleen. Ndi chilolezo cha mphunzitsi wake, Daleen anapereka chidziwitso chake ku kalasi mu mtundu wa kukambitsirana ndi wophunzira wina wofunitsitsa. lye anawerenga malemba ochulukirapo, kuphatikizapo Masalmo 37:29: “Olungama adzalandira dziko lapansi, nadzakhala momwemo kosatha.” Kodi nchiyani chomwe chinali chivomerezo? “Mphunzitsiyo analeka ntchito yake ndi kumvetsera mosamalitsa monga anawo“, watero Daleen. “Pambuyo pake anandithokoza ine, ndipo ochepera a anawo anafunsa mafunso.”

◻ Lillian, wa zaka 5, ndi makolo ake ankakhala mamailosi 12 (19 km) kuchokera ku tauni yaing’ono ya ku South Africa kumene iwo kaŵirikaŵiri ankapezeka pa misonkhano ndi kudzilowetsa mu ntchito yolalikira ya kunyumba ndi nyumba. Tsiku la Sande limodzi, chifukwa chamavuto ena a galimoto, makolo ake analingalira kukhala kunyumba. “Nchifukwa ninji sitikupita kukalalikira?“ anafunsa Lillian. Wosakhutiritsidwa ndi chifukwa chake, iye anati: “Sindidzalola chimenechi kundiletsa ine.” Pambuyo pake mayi wake anazindikira kuti Lillian ndi chola chake chochitira umboni anasowa. Msungwana wachichepereyo anali wotanganitsidwa kuchezera nyumba za pafupipo, akumagawira kwaulerere mabukhu a Baibulo​—kuphatikizapo Baibulo laumwini la mayi wake! Mkazi mmodzi wachikulire anasangalatsidwa ndi kulongosola kwa Lillian kwa Paradaiso ikudzayo kotero kuti iye pambuyo pake analandira chogawira cha phunziro la Baibulo kuchokera kwa mayi wake wa Lillian. Mkazi ameneyo kenaka anadzakhala mlambiri wodzipereka wa Yehova. Nanga Lillian? Tsopano, pokhala anamaliza sukulu, iye wasankhautumiki wa nthawi zonse monga ntchito yake.

Inde, Mulungu adakali kugwiritsira ntchito “m’kamwa mwa makanda” kupereka chilemekezo. Kuwona mtima kwawo kungakhudze mozama mitima ya achikulire. Chotero, moyenerera, ana limodzi ndi achikulire akuphatikizidwamo mu chiitano chachikulu: “Lemekezani Yehova kuchokera ku dziko lapansi, . . . anyamata ndiponso anamwali, okalamba pamodzi ndi ana. Alemekeze dzina la Yehova, pakuti dzina lake lokha ndi lokwezeka.”​—Masalmo 148:7, 12, 13.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena