Zitsanzo za Ulaliki
Zomwe Tinganene Poitanira Anthu ku Chikumbutso
“Tabwera n’cholinga choti tikupatseni kapepala aka, koitanira inuyo pamodzi ndi banja lanu ku mwambo wofunika kwambiri, womwe umachitika chaka chilichonse padziko lonse. Mwambo wake ndi wokumbukira imfa ya Yesu. Chaka chino mwambo umenewu uchitika pa March 26. Pa mwambowu padzakambidwa nkhani yochokera m’Baibulo yomwe idzafotokoze mmene imfa ya Yesu imatithandizira. Simudzafunikira kulipira ndalama iliyonse kuti mumvere nkhaniyi. Kapepalaka kakusonyeza nthawi ndi malo amene kukachitikire mwambowu m’dera lino.”
Nsanja ya Olonda March 1
“Anthu ena akhala akufunsa funso ili, ‘Kodi timadziwa bwanji kuti Yesu anaukitsidwa?’ Kodi inuyo munayamba mwaganizirapo funso limeneli? [Yembekezani ayankhe.] Taonani chifukwa chake yankho la funso limeneli lili lofunika kwambiri. [Werengani 1 Akorinto 15:20-22.] Magazini iyi ikufotokoza zimene zimatithandiza kudziwa kuti nkhani yoti Yesu anaukitsidwa siyongopeka koma ndi yeniyeni.”
Galamukani! March
“Kodi mungavomereze mfundo yakuti masiku ano kusamalira banja si ntchito yamasewera? [Yembekezani ayankhe.] Makolo ambiri aona kuti m’Baibulo muli malangizo othandiza. Mwachitsanzo, vesi ili lathandiza abambo ambiri kuti azipeza nthawi yoti aziyamikira ana awo komanso kuwalimbikitsa. [Werengani Akolose 3:21.] Magazini iyi ikufotokoza mfundo zisanu zofunika kwambiri zimene zingathandize abambo kusamalira bwino ana awo.”