Zochitika mu Utumiki Wakumunda
M’mwezi wa September chaka chatha, alongo 6 a mpingo wa Lilongwe Central anapita kukathandiza mpingo wa Chankhanga ku Kasungu kulalikira uthenga wabwino m’gawo lake lonse. Pa mlungu umodzi wokha, alongowa analalikira maola 362, anagawira magazini 1,650 ndipo anayambitsa maphunziro a Baibulo 8. Mtima wodzipereka woterewu umathandiza pa mbali imene abale athu akuperewera. Sitikukayikira kuti Yehova adalitsa zimenezi.—2 Akor. 8:14.