Ndandanda ya Mlungu wa March 11
MLUNGU WOYAMBIRA MARCH 11
Nyimbo Na. 125 ndi Pemphero
□ Phunziro la Baibulo la Mpingo:
bt mutu 20 ndime 1-7 ndi bokosi patsamba 156 (Mph. 30)
□ Sukulu ya Utumiki wa Mulungu
Kuwerenga Baibulo: Maliko 13-16 (Mph. 10)
Na. 1: Maliko 14:22-42 (Osapitirira mph. 4)
Na. 2: N’chifukwa Chiyani Tiyenera Kukumbukira Imfa ya Yesu?—rs tsa. 70 ndime 3-tsa. 71 ndime 2 (Mph. 5)
Na. 3: Kodi Zizindikiro za pa Chikumbutso Zimaimira Chiyani?—rs tsa. 71 ndime 2-tsa. 72 ndime 2 (Mph. 5)
□ Msonkhano wa Utumiki:
Mph. 10: Kodi Tikuphunzirapo Chiyani? Nkhani yokambirana. Werengani Mateyu 10:7-10 ndi Luka 10:1-4. Kambiranani mmene mavesi amenewa angatithandizire mu utumiki.
Mph. 10: Njira Zowonjezera Utumiki Wanu—Mbali Yoyamba. Nkhani yokambirana yochokera m’buku la Gulu, tsamba 111, ndime yoyamba mpaka tsamba 112 ndime yachiwiri. Funsani wofalitsa mmodzi kapena awiri amene asamukira mumpingo wachinenero china kapena amene aphunzira chinenero china kuti awonjezere utumiki wawo. Kodi ndi mavuto ati amene anali nawo ndipo anawatheta bwanji? Kodi achibale awo kapena mpingo unawathandiza bwanji? Kodi ndi madalitso otani amene apeza?
Mph. 10: “Khalani ndi Mtima Wosangalala Pokonzekera Chikumbutso.” Mafunso ndi mayankho. Kambiranani zimene mpingo wakonza zokhudza Chikumbutso. Fotokozani mmene ntchito yoitanira anthu ku Chikumbutso ikuyendera pa mpingo wanu.
Nyimbo Na. 8 ndi Pemphero