Zitsanzo za Ulaliki
Zimene Munganene Pogawira Kapepala Koitanira Anthu ku Chikumbutso
“Tikugawira kapepala aka kokuitanirani ku mwambo wofunika kwambiri. Pa 3 April, anthu mamiliyoni ambiri adzabwera ku mwambo wokumbukira imfa ya Yesu Khristu. Kudzakhala nkhani yofotokoza mmene imfa yake imatithandizira. Kapepalaka kakusonyeza nthawi komanso malo omwe mwambowu udzachitikire.”
Nsanja ya Olonda March 1
“Pa 3 April padzachitika mwambo wokumbukira imfa ya Yesu Khristu. Anthu ambiri adzabwera ku mwambowu. Komabe pali anthu ena amene sadziwa kufunika kwa imfa ya Yesu. Kodi inuyo mukuganiza kuti imfa ya Yesu komanso kuukitsidwa kwake kumatithandiza bwanji? [Yembekezerani ayankhe.] Taonani zimene lemba ili likunena. [Werengani 1 Akorinto 15:22, 26.] Magaziniyi ikusonyeza kuti imfa ya Yesu idzathandiza kuti anthu akhale ndi moyo wosatha.”
Galamukani! March
“Tikucheza mwachidule ndi anthu m’dera lino ndipo tikuwasonyeza magazini yatsopano ya Galamukani! [Asonyezeni chikuto cha magaziniyo.] Anthu ali ndi maganizo osiyanasiyana pa funso ili: ‘Kodi kukhulupirira zoti kuli Mulungu n’kothandiza bwanji?’ Kodi mukuganiza kuti ndi anthu ati omwe ali ndi tsogolo labwino? Amene amakhulupirira kuti kuli Mulungu kapena amene sakhulupirira zimenezi? [Yembekezerani ayankhe.] Taonani lonjezo la m’Baibulo ili. [Werengani Salimo 37:10, 11.] Magaziniyi ikufotokoza mmene munthu angapindulire atadziwa kuti Mulungu alipodi.”